Ndandanda ya Mlungu wa May 19
MLUNGU WA MAY 19
Nyimbo 131 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 8 ndime 14 mpaka 20 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: Ekisodo 30-33 (Mph. 10)
Na. 1: Ekisodo 32:1-14 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Malamulo Khumi Anathela Limodzi ndi Cilamulo ca Mose—rs tsa. 348 ndime 2-3 (Mph. 5)
Na. 3: N’cifukwa Ciani Sitiyenela Kuopa Satana Ndiponso Ziŵanda Zake?—bh tsa. 104-105 ndime 17 mpaka 19) (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 45
Mph. 10: Cifukwa Cake Ndife Atumiki a Uthenga Wabwino. Nkhani yogwila mtima yocokela m’buku la Gulu tsamba, 77 mpaka 78, ndime 2. Pemphani omvela kuti afotokoze cifukwa cake amasangalala ndi utumiki.
Mph. 10: Kodi Mudzacitako Upainiya Wothandiza pa Chuti Chanu? Kukambilana. Mwacidule kambilanani mfundo zimene zili pa tsamba 113 ndime 1, m’buku la Gulu ndipo fotokozani zofunika kuti munthu akhale mpainiya wothandiza. Pemphani amene anacitako upainiya wothandiza panthawi ya chuti cao ca kunchito kapena kusukulu kuti afotokoze madalitso amene anakhala nao. Ndiyeno limbikitsani onse kuti aziganizila zocitako upainiya wothandiza pa chuti cao cotsatila.
Mph. 10: “Khalani ndi Cizoloŵezi Cosunga Nthawi.” Mafunso ndi mayankho. Mukafika ndime 4, pemphani omvela kuti afotokoze zimene zimawathandiza kusunga nthawi.
Nyimbo 44 ndi Pemphelo