LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 5/14 tsa. 2
  • Khalani ndi Cizoloŵezi Cosunga Nthawi

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Khalani ndi Cizoloŵezi Cosunga Nthawi
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
km 5/14 tsa. 2

Khalani ndi Cizoloŵezi Cosunga Nthawi

1. N’citsanzo cotani cimene Yehova amapeleka pankhani yosunga nthawi?

1 Yehova nthawi zonse amasunga nthawi. Mwacitsanzo, amapeleka thandizo kwa atumiki ake ‘pa nthawi imene akufunika thandizo.’ (Aheb. 4:16) Amapelekanso ‘cakudya ca kuuzimu panthawi yoyenela.’ (Mat. 24:45) Conco, tingakhale ndi cidalilo cakuti tsiku la mkwiyo wake limene likubwela ‘silidzacedwa.’ (Hab. 2:3) Kunena zoona, timapindula kwambili cifukwa cakuti Yehova amasunga nthawi. (Sal. 70:5) Popeza ndife anthu opanda ungwilo amenenso timakhala otangwanika, kusunga nthawi kungamativute kwambili. Komabe, n’cifukwa ciani tiyenela kukhala ndi cizoloŵezi cosunga nthawi?

2. N’cifukwa ciani kusunga nthawi kumalemekezetse Yehova?

2 Kusunga nthawi kwakhala cinthu covuta m’masiku otsiliza ano pamene anthu ambili ndi odzikonda okha ndiponso osadziletsa. (2 Tim. 3:1-3) Conco Akristu akamafika pa nthawi yake ku nchito, kumisonkhano ndiponso pa zimene apangana ndi ena, anthu ena amaona ndipo zimenezi zimalemekezetsa Yehova. (2 Pet. 2:12) Kodi nthawi zonse timayamba nchito yathu ya kuthupi panthawi yake, koma nthawi zambili n’kumacedwa pa zinthu za kuuzimu? Kufika pamisonkhano yampingo nthawi yabwino, kuphatikizapo kupezeka pa nyimbo ndi pemphelo loyamba, kumasonyeza kuti tikufuna kutsanzila Atate wathu wakumwamba amene ndi wadongosolo.—1 Akor. 14:33, 40.

3. N’cifukwa ciani tikamasunga nthawi timaonetsa kuti timaganizila ena?

3 Kusunga nthawi kumaonetsanso kuti timaganizila ena. (Afil. 2:3, 4) Mwacitsanzo, ngati siticedwe pamene tifika pa misonkhano ya Cikristu, kuphatikizapo misonkhano yokonzekela utumiki wakumunda, sitingasokoneze alambili anzathu. Komabe, ngati tili ndi cizoloŵezi cofika mocedwa, timapangitsa anthu ena kuyamba kuganiza kuti timaona nthawi yathu kukhala yofunika kwambili kuposa yao. Kusunga nthawi kumaonetsa kuti ndife odalilika, akhama ndiponso okhulupilika. Amenewa ndi makhalidwe amene anthu amene timakhala nao amayamikila.

4. Ngati nthawi zambili timacedwa, tingaongolele bwanji?

4 Ngati nthawi zambili mumacedwa, ganizilani zimene zimakupangitsani kucedwa. Ndiyeno pangani ndandanda imene ingakuthandizeni kumaliza zocita zanu pa nthawi yake. (Mlal. 3:1; Afil. 1:10) Pemphani Yehova kuti akuthandizeni. (1 Yoh. 5:14) Kusunga nthawi ndi njila imodzi yoonetsela kuti timayamikila malamulo aakulu aŵili a m’Cilamulo amene ndi kukonda Mulungu ndi kukonda anzathu.—Mat. 22:37-39.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani