Ndandanda ya Mlungu wa May 18
MLUNGU WA MAY 18
Nyimbo 50 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 9 ndime 21-24, ndi bokosi pa tsa. 96 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: 2 Samueli 9-12 (Mph. 8)
Na. 1: 2 Samueli 10:13–11:4 (Mph. 3 kapena zocepelapo)
Na. 2: Benaya—Mutu: Khalani Olimba Mtima Komanso Okhulupilika—(w05 5/1 tsa. 15 ndime 11) (Mph. 5)
Na. 3: Tingakhale ndi Ciyembekezo Cotani Kaamba ka Anthu Akufa?—(igw-CIN tsa. 19 ndime 1-3) (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Lemba la Mwezi: Thandizani anthu a mitundu yonse kudziŵa coonadi molondola.—1 Tim. 2:3, 4.
Nyimbo 73
Mph. 10: Mmene Paulo Anathandizila Agiriki Kudziŵa Coonadi Molondola. Kukambilana. Ŵelengani Machitidwe 17:22-31. Ndiyeno kambilanani mmene nkhaniyi ingatithandizile mu ulaliki.
Mph. 20: Yehova Adzakuthandizani Kukhala Olimba Mtima. Kukambilana. Onelelani vidiyo yakuti, Jehovah Will Help You Be Bold [Yehova Adzakuthandizani Kukhala Olimba Mtima]. (Pitani pa jw.org, ndi kuona polemba kuti BIBLE TEACHINGS > CHILDREN.) Pemphani omvela kuti akambe zimene aphunzila m’vidiyo imeneyi. Ngati n’zosatheka kuonelela vidiyoyi, kambilanani nkhani ya mu Nsanja ya Olonda ya February 15, 2012 tsa. 12 ndime 11. Pemphani ana a sukulu kuti afotokoze zimene zawathandiza kukhala olimba mtima polalikila kwa ana a sukulu anzao ndi aphunzitsi. Mwana wa sukulu acite citsanzo ca cocitikaco pamene anali kulalikila kusukulu.
Nyimbo 60 ndi Pemphelo