Ndandanda ya Mlungu wa May 25
MLUNGU WA MAY 25
Nyimbo 56 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 10 ndime 1-7, (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: 2 Samueli 13-15 (Mph. 8)
Na. 1: 2 Samueli 13:34–14:7 (Mph. 3 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi Baibulo Limakamba Ciani za Nchito?—(igw-CIN tsa. 20 ndime 1-3) (Mph. 5)
Na. 3: Bezaleli—Mutu: Mzimu wa Yehova Umathandiza Atumiki Ake pa Nchito Iliyonse Yabwino—(w11 12/15 tsa. 19 ndime 6-7) (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Lemba la Mwezi: Thandizani anthu a mitundu yonse kudziŵa coonadi molondola.—1 Tim. 2:3, 4.
Nyimbo 121
Mph. 10: Kufunsa Mafunso Woyang’anila Kagulu ka Ulaliki. Kodi mumagwila nchito yotani pa udindo wanu? Kodi mumakwanitsa bwanji kusamalila ofalitsa a m’kagulu kanu ndi kuwathandiza mu ulaliki? N’cifukwa ciani ofalitsa afunika kukudziŵitsani ngati asintha nambala ya foni kapena malo okhala? N’cifukwa ciani akulu amakonza zakuti kagulu ka ulaliki kazikumana pakokha pokonzekela ulaliki m’malo mocitila pa malo amodzi?
Mph. 20: “Thandizani Anthu Akhungu Kuphunzila za Yehova.” Mafunso ndi mayankho. Mucitenso citsanzo.
Nyimbo 96 ndi Pemphelo