Ndandanda ya Mlungu wa June 22
MLUNGU WA JUNE 22
Nyimbo 67 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 11 ndime 9-16 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: 1 Mafumu 1-2 (Mph. 8)
Na. 1: 1 Mafumu 1:15-27 (Mph. 3 kapena zocepelapo)
Na. 2: Cifukwa Cake Akristu Enieni Amakhala Okhutila ndi Osangalala—igw-CIN tsa. 23 ndime 1-3 (Mph. 5)
Na. 3: Kalebe—Mutu: Yehova Amapatsa Mphamvu Amene Amamutsatila ndi Mtima Wonse—w09 3/15 tsa. 8 ndime 5-tsa. 9 ndime 2 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Lemba la Mwezi: “Kumbukilani masiku akale.”—Deut. 32:7.
Nyimbo 75
Mph. 7: Ciitano Cacindunji. Mafunso ndi mayankho. Pokambilana ndime 3, mucite citsanzo coonetsa zimene tingakambe pogawila kapepala kaciitano.
Mph. 10: Zikumbutso za Msonkhano wa Cigawo. Nkhani yokambilana yokambidwa ndi kalembela. Kambilanani mfundo za m’Baibulo ndi mmene zingathandizile pa msonkhano wacigawo wa 2015. Fotokozani mfundo zikuluzikulu za m’kalata yopita ku mipingo yonse ya August 3, 2013, yokamba za mmene tingadzitetezele pa msonkhano wa cigawo.
Mph. 13: Zikondwelelo Zapacaka. Nkhani yocokela mu Nsanja ya Olonda ya September 15, 2012, masamba 31-32, ndime 15-19. Thandizani onse kuyembekeza msonkhano wa cigawo mwacidwi. Limbikitsani omvela kuonelatu nkhani zimene zidzakambidwa pa msonkhanowo mwa kuŵelenga pulogalamu ya msonkhano pa jw.org.
Nyimbo 107 ndi Pemphelo