Ndandanda ya Mlungu wa July 13
MLUNGU WA JULY 13
Nyimbo 75 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 27 ndime 10-18 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: 1 Mafumu 9-11 (Mph. 8)
Na. 1: 1 Mafumu 9:24–10:3 (Mph. 3 kapena zocepelapo)
Na. 2: Mungacepetse Nkhawa Mwa Kuphunzila Mau a Mulungu—igw-CIN tsa. 24 ndime 4–tsa. 25 ndime 2 (Mph. 5)
Na. 3: Koresi—Mutu: Mau a Mulungu Amakwanilitsidwa Nthawi Zonse—w14 5/1 tsa. 5 ndime 2 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Lemba la Mwezi: “Pitani mukaphunzitse anthu.”—Mat. 28:19, 20.
Nyimbo 17
Mph. 10: Pitani Mukaphunzitse Anthu. Nkhani yozikidwa pa lemba la mwezi. Fotokozaninso mfundo za m’buku la “Bwera Ukhale Wotsatira Wanga,” masamba 87-89. Mwacidule, chulani nkhani za mu Msonkhano wa Nchito zamwezi uno, ndipo fotokozani mmene zikugwilizanilana ndi lemba la mwezi.
Mph. 10: Anali Wokonzeka Kuyambitsa Phunzilo la Baibulo. Nkhani yokambilana yocokela mu Buku la Pacaka la 2015, tsamba 55, ndime 1, mpaka tsamba 56, ndime 1 ndi tsamba 69, ndime 2-5. Ndiyeno pemphani omvela kuti akambe zimene aphunzilapo.
Mph. 10: “Ikani Maganizo Anu pa Nchito Yophunzitsa Anthu.” Mafunso ndi mayankho. Mwacidule funsani mafunso ofalitsa mmodzi kapena aŵili amene amacita bwino poyambitsa ndi kucititsa phunzilo la Baibulo. Ndi mapindu otani amene apeza pothandiza winawake kuphunzila coonadi?
Nyimbo 16 ndi Pemphelo