Ikani Maganizo Anu pa Nchito Yophunzitsa Anthu
1. N’ciani cimene cifunika kuti anthu apulumutsidwe?
1 Lipoti la caka ca utumiki ca 2014, lionetsa kuti anthu a Mulungu anadzipeleka kwambili pa nchito yolalikila uthenga wabwino wa Ufumu. (Mat. 24:14) Kuposa ndi kale lonse, anthu ambili akulandila uthenga wa m’Baibulo kupitila mu ulaliki wa kunyumba ndi nyumba, nchito yapadela yogaŵila tumapepala twauthenga ndi twa ciitano, ndiposo ulaliki wa poyela. Ngakhale n’conco, kuti anthu apulumuke, tifunika kuwathandiza kukhala ophunzila a Yesu mwa kuphunzila nao Baibulo.—1 Tim. 2:4.
2. Ndi mafunso ati amene mungadzifunse omwe angatithandize kuyambitsa phunzilo la Baibulo?
2 Khalani Okonzeka Kuyambitsa Phunzilo la Baibulo: Munthu akacita cidwi ndi uthenga wathu, kodi mumatenga adilesi yake ndi kumufikila mwamsanga kuti muyambe kuphunzila naye Baibulo? Ndi liti pamene munayesa kuyambitsa phunzilo la Baibulo pa ulendo woyamba? Nanga ndi liti pamene munapempha anthu amene mumacitako ulendo wa magazini kuti muyambe kuphunzila nao Baibulo? Kodi munaonetsapo anzanu a kunchito, kusukulu, aneba, acibale ndi ena amene mudziŵa vidiyo yakuti N’cifukwa Ciani Muyenela Kuphunzila Baibulo? ndi yakuti Kodi Phunzilo la Baibulo Limacitika Bwanji? Mukamagwilitsila nchito shelufu kapena thebulo la zofalitsa polalikila, kodi mumayesetsa kuuza anthu amene atenga cofalitsa cophunzitsila Baibulo kuti angaphunzile Baibulo kwaulele?
3. Kodi cofunika n’ciani kuti tiphunzitse bwino coonadi?
3 Thandizo Locokela kwa Yehova ndi Yesu: Yesu popeleka lamulo lakuti “mukaphunzitse anthu,” anayamba ndi mau akuti “pitani.” Zimenezi zionetsa kuti tifunika kucita khama ndi kukhala aluso pa nchitoyi. Ngakhale n’telo, iye anatilonjeza kuti sadzatisiya. (Mat. 28:19, 20) Kuonjezela apo, Yehova watipatsa mzimu wake woyela, zida, ndi maphunzilo amene timafunikila pophunzitsa anthu coonadi. (Zek. 4:6; 2 Akor. 4:7) Tingamupemphe kuti ‘alimbitse zolakalaka zathu kuti ticite zinthu zonse zimene iye amakonda’—Afil. 2:13.
4. N’cifukwa ciani tifunika kuika maganizo athu pa kuphunzitsa anthu?
4 Kulalikila uthenga wabwino kumatibweletsela cimwemwe. Koma timasangalala kwambili tikaphunzitsa munthu wina coonadi ndi kumuthandiza kuloŵa nafe pa “cipata coloŵela ku moyo.” (Mat. 7:14; 1 Ates. 2:19, 20) Cofunika kwambili ndi kuika maganizo athu pa nchito yophunzitsa anthu kuti tikondweletse Yehova amene “safuna kuti wina aliyense adzaonongedwe, koma amafuna kuti anthu onse alape.”—2 Pet.3:9.