Ndandanda ya Mlungu wa July 20
MLUNGU WA JULY 20
Nyimbo 73 ndi Pemphelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 12 ndime 16-21 ndi bokosi pa tsa. 127 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: 1 Mafumu 12-14 (Mph. 8)
Na. 1: 1 Mafumu 12:21-30 (Mph. 3 kapena zocepelapo)
Na. 2: Danieli—Mutu: Yehova Amadalitsa Anthu Odzipeleka ndi Mtima Wonse—w13 1/15 tsa. 10 ndime 14 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Baibulo Lingathandize Bwanji Mwamuna Kapena Tate?—igw-CIN tsa. 26 ndime 1-2 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Lemba la Mwezi: “Pitani mukaphunzitse anthu.”—Mat. 28:19, 20.
Nyimbo 89
Mph. 20: Gwilitsilani Nchito Zithunzi Zofotokoza Nkhani za m’Baibulo Pothandiza Ana Anu kuti Akhale Ophunzila. Nkhani yokambilana yozikidwa pa zithunzi zofotokoza nkhani za m’Baibulo, ya mutu wakuti “Mulungu anatumiza Mose ku Iguputo.” (Pitani pa jw.org, ndi kuona pa BIBLE TEACHINGS > CHILDREN.) Onetsani zithunzi za nkhaniyi pa TV yanu kuti onse m’gulu aone ndi kutsatila. Ngati n’kotheka, mungapatse ana pasadakhale, mbali zoŵelenga pamene pali munthu aliyense wochulidwa m’nkhaniyi. Koma muyenela kupempha cilolelo ca makolo musanawapatse mbali. Pambuyo pake, mungapemphe anao kuti abwele kutsogolo ndi kukambilana nao mafunso amene ali pa kabokosi kakuti: “Kodi Tikuphunzila Ciani Pankhaniyi?” Ngati n’zosatheka kuona zithunzi zimenezi pa TV, gwilitsilani nchito buku lakuti Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso, mutu 4 wakuti “Mulungu Ali ndi Dzina Lake.” Pemphani pasadakhale acicepele oyenelela kuti adzaŵelenge mbali za anthu osiyanasiyana ochulidwa pa Ekisodo 3:1-15. Mmodzi adzaŵelenge mbali ya wosimba nkhani. Pambuyo pake, mungapemphe anao kuti abwele kutsogolo ndi kukambilana nao mafunso ogwilizana ndi cithunzi ciliconse mu mutu umenewu. Musanacite zimenezi muyenela kupempha cilolezo ca makolo. Malizani mwa kulimbikitsa makolo kuti azigwilitsila nchito bwino cida cimeneci pothandiza ana ao kuti akhale ophunzila.
Mph. 10: Bokosi la Mafunso. Kukambilana.
Nyimbo 66 ndi Pemphelo