Ndandanda ya Mlungu wa September 7
MLUNGU WA SEPTEMBER 7
Nyimbo 3 ndi Pempelo
Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 15 ndime 1-10 (Mph. 30)
Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: 2 Mafumu 12-15 (Mph. 8)
Na. 1: 2 Mafumu 13:12-19 (Mph. 3 kapena zocepelepo)
Na. 2: Dorika—Mutu: Akristu Oona Amacita Nchito Zambili Zabwino—w11 1/15 tsa. 20 ndime 13-14 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi m’Malemba Acigiriki Acikristu Muli Uthenga Wotani?—igw-CIN tsa. 31 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Lemba la Mwezi: “Koma ine ndi a m’nyumba yanga, tizitumikila Yehova.”—Yoswa 24:15.
Nyimbo 89
Mph. 10: Tinacita Zotani? Kukambilana. Pemphani omvela kuti akambe mapindu amene apeza pogwilitsila nchito mfundo za m’nkhani yakuti, “Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Phunzitsani Atsopano.” Pemphani omvela kuti afotokoze zocitika zabwino za mu ulaliki.
Mph. 10: Mabanja, Kodi Muli ndi Cizoloŵezi Copezeka pa Misonkhano ya Mpingo? Nkhani yocokela pa Aheberi 10:24, 25. Funsani mafunso banja limene lili ndi ana. Kodi mutu wa banja umacita ciani kuti onse m’banja aziona misonkhano kukhala yofunika kwambili? Nanga aliyense amacita ciani kuti athandize banjalo kupezeka pa misonkhano nthawi zonse? Ndi liti pamene amakonzekela misonkhano? Amadzimana zinthu zotani kuti apezeke pa misonkhano? Malizani mwa kulimbikitsa onse kuti azisonkhana ndi kutengako mbali pa misonkhano nthawi zonse.
Mph. 10: Kodi Mukubzala Mbeu za Coonadi ca m’Baibulo mwa Acibale Anu? (Machitidwe 10:24, 33, 48) Kukambilana kozikidwa mu Buku Lapacaka la 2015 tsamba 87, ndime 1-2; ndi tsamba 90, ndime 1-3. Pemphani omvela kuti akambe zimene aphunzilapo.
Nyimbo 118 ndi Pempelo