UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Mungapambane Ngakhale Kuti Muli na “Munga M’thupi”!
M’masiku otsiliza ovuta ano, mavuto amene ali ngati minga amasautsa atumiki onse a Mulungu. (2 Tim. 3:1) Kodi tingamudalile bwanji Yehova kuti tikwanitse kulimbana nawo mavuto amenewo? Tambitsani vidiyo yakuti “Maso a Anthu Akhungu Adzatseguka,” kuti muone zimene Talita Alnashi na makolo ake anacita. Kenako, yankhani mafunso aya:
N’ciani cili ngati “munga m’thupi” kwa Talita?
Ni malonjezo a m’Baibo ati amene athandiza Talita na makolo ake kukhalabe acimwemwe?
Kodi makolo a Talita anaonetsa bwanji cidalilo cawo pa Yehova pambuyo pa opaleshoni ya Talita?
Kodi makolo a Talita anaseŵenzetsa bwanji zofalitsa za gulu pothandiza mwana wawo kukulitsa cikondi cake pa Mulungu?
Kodi Talita anaonetsa bwanji kuti akukula mwauzimu olo kuti ali na “munga m’thupi”?
Kodi citsanzo ca Talita cakulimbikitsani bwanji?