May 27–June 2
AGALATIYA 1-3
Nyimbo 106 na Pemphelo
Mawu Oyamba (3 min. olo kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Ndinamutsutsa Pamasom’pamaso”: (10 min.)
[Tambitsani vidiyo yakuti Mfundo Zokhudza Buku la Agalatiya.]
Agal. 2:11-13—Akhristu Aciyuda atafika kwa Petulo, iye analeka kuyanjana na Akhristu a mitundu ina cifukwa coopa anthu (w17.04 27 ¶16)
Agal. 2:14—Paulo anamuwongolela Petulo (w13 3/15 5 ¶12)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Agal. 2:20—Kodi dipo mufunika kuliona bwanji? Cifukwa ciani? (w14 9/15 16 ¶20-21)
Agal. 3:1—N’cifukwa ciani Paulo anauza Agalatiya kuti “opusa inu!”? (it-1 880)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Agal. 2:11-21 (th phunzilo 10)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Vidiyo ya Ulendo Wobwelelako Waciŵili: (5 min.) Tambitsani na kukambilana vidiyoyi.
Ulendo Wobwelelako Waciŵili: (3 min. olo kucepelapo) Seŵenzetsani makambilano acitsanzo. (th phunzilo 2)
Phunzilo la Baibo: (5 min. olo kucepelapo) bhs 202-203 ¶18-19 (th phunzilo 6)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Mmene Tonse Tingatengeleko Mbali pa Kusamalila Malo Athu Olambilila”: (15 min.) Nkhani yokambilana yokambidwa na mkulu. Pambuyo potambitsa vidiyo yakuti Kusamalila Malo Athu Olambilila, na kukambilana mafunso, mwacidule funsani mafunso ali pansipa m’bale wam’komiti yosamalila Nyumba ya Ufumu wa mumpingo mwanu. (Ngati mumpingo wanu mulibe m’baleyo funsani mgwilizanitsi wa bungwe la akulu. Ngati mu Nyumba yanu ya Ufumu mumasonkhana mpingo wanu wokha, funsani woyang’anila zokonza-konza.) Kodi mpingo wathu ucita bwanji pambali yotsatila ndandanda yoyeletsa na kukonza zinthu? Kodi timatsatila malangizo a citetezo pogwila nchito? Ni nchito ziti zokonza-konza zimene zacitika posacedwa, komanso zimene mufuna kudzacita kutsogoloku? Ngati wina ali na luso la zokonza-konza, kapena ngati afuna kuphunzila maluso kwa amene ali nawo kale, angacite bwanji? Kodi tonse, mosasamala kanthu za mmene zinthu zilili mu umoyo wathu, tingathandizile bwanji kusamalila Nyumba ya Ufumu?
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 68
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 72 na Pemphelo