CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 YOHANE 1-13; 3 YOHANE 1-14-YUDA 1-25
Tifunika Kumenya Nkhondo kuti Tikhalebe m’Coonadi
Yuda 3
Yesu anatiilimbikitsa kuti: “Yesetsani mwamphamvu kuloŵa pakhomo lopapatiza.” (Luka 13:24) Mawu a Yesu aonetsa kuti tifunika kulimbikila, kuyesetsa kuti Mulungu atiyanje. Yuda m’bale wake wa Yesu, anauzilidwa kulemba mawu ofanana na amenewa. Anati: ‘Menyani mwamphamvu nkhondo yacikhulupililo.’ Timafunika kuyesetsa mwakhama kuti tikwanitse kucita zotsatilazi:
Kupewa dama.—Yuda 6, 7
Kulemekeza amene ali na ulamulilo.—Yuda 8, 9
Kudalila kwambili ziphunzitso zozikidwa pa “cikhulupililo . . . coyela kopambana,” kutanthauza ziphunzitso zacikhristu.—Yuda 20, 21