Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki
JULY 6-12
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 6-7
“Tsopano Uona Zimene Ndicite kwa Farao”
it-2 436 ¶3
Mose
Panalinso kusintha mtima kwakukulu pakati pa amuna aciisiraeli. Poyamba anavomeleza udindo wa Mose, koma pambuyo pogwila nchito yolimba kwambili imene Farao anawalamula, anadandaula za iye mpaka kufika poti Mose mwacisoni anacondelela Yehova. (Eks. 4:29-31; 5:19-23) Panthawiyo, Wam’mwamba-mwamba anam’limbikitsa pomuuza kuti adzakwanilitsa cimene Abulahamu, Isaki na Yakobo anayembekezela, inde kudziŵikitsidwa bwino kwa tanthauzo la dzina lake lakuti Yehova, mwa kupulumutsa Aisiraeli na kuwakhazikitsa monga mtundu waukulu m’dziko limene anawalonjeza. (Eks. 6:1-8) Ngakhale n’conco, amuna aciisiraeli sanamumvele Mose. Koma pambuyo pa mlili wa namba 9, iwo anam’cilikiza na mtima wonse, anacita zinthu mogwilizana naye cakuti pambuyo pa mlili wa namba 10, Mose anatha kuwasonkhanitsa na kuwatsogolela mwadongosolo “lomenyela nkhondo.”—Eks. 13:18.
it-2 436 ¶1-2
Mose
Pamaso pa Mfumu Farao ya Iguputo. Mose na Aroni ndiwo anali patsogolo pa ‘nkhondo yomenyana na milungu.’ Poseŵenzetsa ansembe amatsenga, amene anali akulu oyang’anila, amenenso mwacionekele maina awo anali Yane ndiponso Yambure (2 Tim. 3:8), Farao anaitanitsa mphamvu za milungu yonse ya Iguputo potsutsana na mphamvu za Yehova. Cozizwitsa coyamba cimene Aroni anacita pamaso pa Farao mouzidwa na Mose, cinaonetsa ukulu wa Yehova pa milungu ya Iguputo. Ngakhale n’conco, Farao anaumitsabe mtima wake kwambili. (Eks. 7:8-13) Pambuyo pake, pamene mlili wa namba 3 unabwela, ngakhale ansembe anakakamizika kuvomeleza kuti, “Cimeneci ndi cala ca Mulungu!” Ndipo anali atakanthidwa kwambili na mlili wa zithupsa zomaphulika pa matupi awo, cakuti onse pamodzi sanakwanitse kuonekela pamaso pa Farao, kuti atsusane na Mose pa nthawi ya mlili umenewu.—Eks. 8:16-19; 9:10-12.
Milili ifewetsa komanso kuumitsa mitima ya anthu. Mose na Aroni ndiwo anali kulengeza mlili uliwonse wa Milili 10. Mlili uliwonse unali kucitika ukalengezedwa, kuonetsa kuti Mose anatumidwadi na Yehova monga womuimila. Dzina la Yehova linalengezedwa, ndipo linali m’kamwa-m’kamwa mu Iguputo, kukwanilitsa zonse ziŵili kufewetsa komanso kuumitsa mitima ya anthu. Kufewetsa mitima ya Aisiraeli komanso ya Aiguputo ena. Kumbali ina, kuuimitsa mtima wa Farao na alangizi ake, komanso anthu amene anali kuwacilikiza. (Eks. 9:16; 11:10; 12:29-39) M’malo mokhulupilila kuti anakhumudwitsa milungu yawo, Aiguputo anadziŵa kuti ni Yehova anali kuweluza milungu yawo. Pa nthawi imene mlili wa namba 9 unacitika, nayenso Mose “analemekezeka kwambili m’dziko la Iguputo, pamaso pa atumiki a Farao ndi pamaso pa Aiguputo onse.”—Eks. 11:3.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
it-1 78 ¶3-4
Wamphamvuzonse
Yehova anaseŵenzetsa dzina la udindo wake lakuti “Mulungu Wamphamvuyonse” (ʼEl Shad·daiʹ) popanga lonjezo kwa Abulahamu lokhudza kubadwa kwa Isaki. Lonjezoli linafuna kuti Abulahamu akhale na cikhulupililo cacikulu mu mphamvu ya Mulungu yokwanilitsa lonjezo limenelo. Dzina la udindo limeneli linachulidwanso pamene lonjezo linapelekadwa, lakuti Mulungu adzadalitsa Isaki na Yakobo monga olandila colowa ca pangano la Abulahamu.—Gen. 17:1; 28:3; 35:11; 48:3.
Mogwilizana na zimenezi, Yehova pambuyo pake anauza Mose kuti: “Ndinali kuonekela kwa Abulahamu, Isaki ndi Yakobo monga Mulungu Wamphamvuyonse [beʼElʹ Shad·daiʹ]. Koma za dzina langa lakuti Yehova, ine sindinadzidziwikitse kwa iwo.” (Eks. 6:3) Izi sizitanthauza kuti makolo akalewo sanali kulidziŵa dzina la Yehova. Zili conco cifukwa iwo anali kuliseŵenzetsa kaŵili-kaŵili dzinali, ngakhalenso anthu ena amene anakhalako iwo asanakhaleko. (Gen. 4:1, 26; 14:22; 27:27; 28:16) Ndipo m’buku la Genesis, limene limafotokoza umoyo wa makolo akalewo, dzina lakuti “Wamphamvuyonse” limangopezeka maulendo 6, pamene dzina lake leni-leni lakuti Yehova linalembedwa maulendo 172 m’malemba Aciheberi oyambilila. Makolo akale amenewo analidziŵa dzinali podzionela okha nchito za Mulungu, zoonetsa kuti alidi woyenelela kuchedwa “Wamphamvuyonse.” Ngakhale n’telo, iwo anali asanakhalepo na mwayi womvetsa bwino-bwino tanthauzo lonse la dzina lakuti Yehova. Pa mbali imeneyi, buku lakuti Illustrated Bible Dictionary (Vol. 1, p. 572) linati: “Vumbulutso limene makolo akalewo analandila linali lokhudza malonjezo akutsogolo kwambili. Anaunikilidwa powatsimikizila zakuti Iyeyo, Yahweh, anali Mulungu (ʼel) wokhoza (mbali imodzi yokhudza tanthauzo la sadday) kuwakwanilitsa malonjezowo. Vumbulutso la pa citsamba linali lalikulu kupambana pamenepo komanso lolimbikitsa. Linali lakuti dzina lodziŵikalo lakuti Yahweh, limanthauzanso kuti Iye ali na mphamvu ndipo anali nawo nthawi zonse.”—Edited by J. D. Douglas, 1980.
it-2 435 ¶5
Mose
Manyazi a Mose sanam’pangitse kukhala wosayenelela. Pokhala wamanyazi, anakana kuti sangakwanitse kukakamba bwino-bwino. Apa Mose anasinthilatu. Kodi si uja amene anadzisankha yekha kukhala wopulumutsa Aisiraeli zaka 40 kumbuyoko. Iye anadodoma kwa Yehova, mpaka pothela pake anapempha Yehova kuti asam’patse nchitoyo. Ngakhale kuti izi zinaputa mkwiyo wa Mulungu, iye sanamukane Mose. M’malo mwake anam’patsa Aroni m’bale wake kuti akhale womulankhulila. Popeza Mose anali kuimilako Mulungu, anakhala monga “Mulungu” kwa Aroni, amene anali kukamba momuimilako. Pokambilana na akulu Aciisiraeli komanso pokakamba na Farao, zioneka kuti Mulungu anali kupatsa Mose malangizo na malamulo. Ndipo Mose anali kuuza Aroni, kuti iye ndiye amene akakambe pamaso pa Farao (amene analoŵa m’malo Farao amene Mose anathawako zaka 40 kumbuyoko). (Eks. 2:23; 4:10-17) Pambuyo pake, Yehova anakamba za Aroni kuti anali monga “mneneli” wa Mose, kutanthauza kuti, monga mmene Mose analili mneneli wa Mulungu, amene anali kum’tsogolela, nayenso Aroni anafunika kutsogoleledwa na Mose. Komanso Mose anauzidwa kuti adzaikidwa kukhala “Mulungu kwa Farao,” kutanthauza kuti adzapatsidwa mphamvu ya Mulungu na ulamulilo pa Farao, kuti asacite mantha na mfumu ya Iguputo.—Eks. 7:1, 2.
JULY 13-19
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 8-9
“Farao Wonyadayo Mosadziŵa Anathandiza Kuti Cifunilo ca Mulungu Cikwanilitsidwe”
it-2 1040-1041
Kuuma Khosi
Pocita ndi anthu, Yehova Mulungu, moleza mtima walola kuti aliyense payekha komanso mitundu, olo kuti ni oyenela kufa, apitilize kukhalapo na moyo. (Gen. 15:16; 2 Pet. 3:9) Ena alabadila na mtima wonse kotelo kuti akalandile cifundo cake. (Yos. 2:8-14; 6:22, 23; 9:3-15) Koma ena aumitsa mtima wawo motsutsana na Yehova komanso anthu ake. (Deut. 2:30-33; Yos. 11:19, 20) Yehova saletsa anthu kukhala ouma khosi. Baibo imakamba kuti iye ‘amawalola kuumitsa mtima.’ Koma nthawi ikafika yowabwezela cilango, mpamene anthuwo amaziona mphamvu zake, ndipo dzina lake limalengezeka.—Yelekezani na Eks. 4:21; Yoh. 12:40; Aroma 9:14-18.
it-2 1181 ¶3-5
Kuipa
Kuwonjezela apo, Yehova Mulungu amatengelapo mwayi pa zinthu zimene zimacitika, m’njila yakuti anthu oipa mosadziŵa amathandizila pa kukwanilitsa cifunilo cake. Olo kuti amatsutsa Mulungu, iye angawaletse pa mlingo woyenela kuti atumiki ake akhalebe na mtima wosagaŵika, komanso angapangitse kuti zocita zawo zionetse cilungamo cake. (Aroma 3:3-5, 23-26; 8:35-39; Sal. 76:10) Mfundo imeneyi ili pa Miyambo 16:4: “Yehova anapanga ciliconse n’colinga, ndipo ngakhale woipa anamusungila tsiku loipa.”
Citsanzo pa nkhaniyi ni Farao amene Yehova, kupitila mwa Mose na Aroni, anamuuza kuti amasule Aisiraeli mu ukapolo. Mulungu sanapangitse wolamulila wa Iguputo ameneyu kukhala woipa, koma anamulola kukhalabe na moyo. Anabweletsanso milili imene inaonetsa poyela kuti Farao analidi munthu woipa, ndipo anali woyenela kufa. Colinga ca Yehova pocita izi cili pa Ekisodo 9:16: “Koma ndakusiya ndi moyo kuti ndikusonyeze mphamvu zanga, ndi kuti dzina langa lilengezedwe padziko lonse lapansi. Koma ndithu cifukwa cake ndakuimika kuti ndikuwonetse mphamvu yanga, ndi kuti alalikile dzina langa pa dziko lonse lapansi.”
Milili 10 imene inagwela Aiguputo, inatha na kuwonongedwa kwa Farao komanso magulu ake a nkhondo pa Nyanja Yofiila, umene unali umboni wamphamvu kwambili wa mphamvu za Yehova. (Eks. 7:14–12:30; Sal 78:43-51; 136:15) Pambuyo pake kwa zaka, mitundu yowazungulila inapitiliza kukamba za nkhani imeneyi. Ndipo izi zinapangitsa kuti dzina la Mulungu lilengezedwe pa dziko lonse lapansi. (Yos. 2:10, 11; 1 Sam. 4:8). Yehova akanapha Farao mwamsanga, umboni waukulu umenewu wa mphamvu zake, komanso ulemelelo Wake kuti anthu Ake apulumutsidwe sizikanakhala zotheka kuonekela.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
it-1 878
Tudoyo Touluka Toyamwa Magazi
N’zosatsimikizilika bwino-bwino kuti tudoyoto tunali totani, tochulidwa na mawu Aciheberi cakale anagwiitsidwa nchito m’Malemba, pokamba za mlili wacinayi umene unagwela Aiguputo. Uwu unali mlili woyamba umene Aisiraeli ku Goseni sanakhudzidwe nawo. (Eks. 8:21, 22, 24, 29, 31; Ps 78:45; 105:31) Liwu lakuti ʽA·rov’ lamasulidwa m’njila zosiyan-siyana, monga “mizaza” (JB, NW, Ro), “mnangalile” (Yg), “nchenche” (AS, KJ, RS), komanso “cimpanga” (LXX).
Mawu a Chichewa akuti “tizilombo touluka toyamwa magazi,” angatanthauzenso tudoyo twina monga nchenche zina zoluma monga akamzembe. Nchenche zina zimenezi zimaluma nyama kapena munthu na kuyamwa magazi. Zina pamene zikali mbozi zimakhala m’matupi a nyama ndi anthu. Zokhala m’matupi a anthu zimepezeka maka-maka kumadela otentha. Conco, mlili wa tudoyo touluka toyamwa magazi unawazunza kwambili Aiguputo na ziŵeto zawo, nthawi zina ngakhale kuwapha kumene.
w04 3/15 25 ¶9
Mfundo Zazikulu za M’buku la Ekisodo
8:26, 27—N’cifukwa ciani Mose anakamba kuti nsembe za Aisiraeli zikanakhala “conyansa ca Aiguputo”? Ku Iguputo, nyama zambili anali kuzilambila. Motelo, kukamba kuti apeleke nsembe nyama kunawonjezela mphamvu komanso cifukwa cokwanila cakuti Aisiraeli aŵalole kuti acoke akapeleke nsembe kwa Yehova, zimene Mose anakamba mobweleza-bweleza.
JULY 20-26
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 10-11
“Mose na Aroni Anaonetsa Kulimba Mtima Kwambili”
w09 7/15 20 ¶6
Tsanzilani Yesu mwa Kulalikila Molimba Mtima
6Taganizilaninso za kulimba mtima kumene Mose anaonetsa. Iye analankhula na Farao, amene anthu anali kumuona, osati ngati woimila cabe milungu, koma ngati mulungu amene, mwana wa Ra, mulungu dzuŵa. N’zotheka kuti iye, mofanana na Afarao ena, anali kulambila fano loimila iyeyo. Farao anali mfumu yakuti ikakamba yakamba, palibe anali kuyelekeza kutsutsa zimene wagamula. Pokhala wamphamvu, wodzikuza, ndiponso waliuma, Farao sanazolowele kuuzidwa zocita. N’kumene Mose, m’busa wofatsa uja, anapita mobweleza-bweleza popanda kuitanidwa, ndipo sanali kumufunanso ngakhale pang’ono. Kodi kumeneko Mose anali kulosela za ciani? Analosela milili yoopsa. Ndipo kodi anapempha ciani? Anapempha kuti Farao alole akapolo ake mamiliyoni angapo kutuluka m’dzikolo. Kodi pamenepa Mose anafunika kulimba mtima? N’zosacita kufunsa!—Num. 12:3; Aheb. 11:27.
it-2 436 ¶4
Mose
Kulimba mtima na cikhulupililo zinali zofunika kuti aonane na Farao. Ni mphamvu ya Yehova cabe komanso thandizo la mzimu wake woyela, zimene zinathandiza Mose na Aroni kukwanitsa nchito imene anapatsidwa. Yelekezani kuti mukuiona nyumba ya Farao, mfumu yomveka mbiliyo, munthu waulemelelo waukulu, wonyada, wodziona kukhala mulungu, atazungulilidwa na alangizi, akulu-akulu a asilikali, olonda komanso akapolo. Kuwonjezela apo, palinso atsogoleli acipembedzo, ansembe amatsenga, akulu oyang’anila amene anali pakati pa anthu amene anali kutsutsa Mose. Anthu onsewa anali kumbali ya Farao cabe, anthu a mphamvu mu ufumu wake. Anthu onse amenewa anaikidwa kuti aikile kumbuyo Farao pokweza milungu ya Iguputo. Mose na Aroni anafika kwa Farao, osati kamodzi, koma kambili, cifukwa iye sanali kufuna konse kumasula akapolo ake a mtengo wapataliwo. Ndipo pambuyo polengeza mlili wa namba 8, Mose na Aroni anacotsedwa pamaso pa Farao. Kenako pambuyo pa mlili wa namba 9, analamulidwa kuti asadzayesenso kuonekela pamaso pa Farao cifukwa akadzatelo adzaphedwa.—Eks. 10:11, 28.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
w95 9/1 11 ¶11
Mboni Zotsutsa Milungu Yonama
11Pamene Aisiraeli anali mu Iguputo, Yehova anatuma Mose kwa Farao kuti: “Pita kwa Farao pakuti ndalola iye pamodzi ndi atumiki ake kuumitsa mitima yawo, kuti ndicite zizindikilo zanga pamaso pake. Ndacita zimenezi kuti mufotokozele ana anu, ndi ana a ana anu, mmene ndakhaulitsila Iguputo ndi zizindikilo zimene ndacitila Aiguputo. Ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.” (Ekisodo 10:1, 2) Aisiraeli omvela anayenela kufokozela ana awo zocita zamphamvu za Yehova. Ana awo nawonso, anayenela kufotokozela kwa ana awo, conco anatelo kumibadwo-mibadwo. Motelo, anakumbukila zocita zamphamvu za Yehova. Masiku anonso, makolo ali na udindo la kucitila umboni kwa ana awo.—Deuteronomo 6:4-7; Miyambo 22:6.
it-1 783 ¶5
Ekisodo
Poonetsa mphamvu zake m’njila yodabwitsa, Yehova anakweza dzina lake na kupulumutsa Aisiraeli. Atafika kumbali ina ya Nyanja Yofiila ali otetezeka, Mose anatsogolela ana Aisiraeli kuimba nyimbo, pamene mlongo wake Miriamu, mneneli wamkazi anatenga masece m’manja mwake, na kutsogolela akazi ena onse kuimba masece komanso kuvina, pamene amuna anali kuimba, iwo anathilila mang’ombe. (Eks. 15:1, 20, 21) Kupatukana kothelatu kwa Aisiraeli na adani awo kunatheka. Pamene anacoka ku Iguputo, Aisiraeli sanavutitsidwe na munthu kapena zilombo, ngakhale galu sanawauwe. (Eks. 11:7) Ngakhale kuti nkhani ya mu Ekisodo sikambapo zoti Farao iye mwini anangena pa nyanja pamodzi na gulu lake la nkhondo na kuphedwa nalo pamodzi, Salimo 136:15 imakamba kuti Yehova “anakutumulila Farao ndi gulu lake lankhondo m’Nyanja Yofiila.”
JULY 27–AUGUST 2
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 12
“Mwambo wa Pasika—Zimene Umatanthauza kwa Akhristu”
w07 1/1 20 ¶4
“Iwe Uzikhala Wosangalala Basi”
4Yesu anafa pa Nisani 14, mu 33 C.E. Mu Isiraeli, Nisani 14 linali tsiku lacisangalalo la madyelelo a Pasika. Caka ciliconse, pa tsiku limeneli mabanja anali kudyela pamodzi cakudya cimene cinali kuphatikizapo mwana wa nkhosa wopanda cilema. Mwa njila imeneyi, anali kukumbukila nchito imene magazi a mwana wa nkhosa anagwila pa kulanditsidwa kwa ana oyamba a Aisiraeli pamene mngelo wakupha anapha ana oyamba a Aiguputo pa Nisani 14, mu 1513 B.C.E. (Ekisodo 12:1-14) Mwana wa nkhosa wa pa Pasika anacitila cithunzi Yesu, amene ponena za iye mtumwi Paulo anati: “Pakuti Khristu wapelekedwa monga nsembe yathu ya pasika.” (1 Akorinto 5:7)Mofanana ndi magazi a mwana wa nkhosa wa pa Pasika, magazi a Yesu amene anakhetsedwa amapulumutsa anthu ambili.—Yohane 3:16, 36.
it-2 583 ¶6
Pasika
Zinthu zina zimene zinali kucitika pa mwambo wa Pasika zinakwanilitsidwa na Yesu. Cimodzi mwa izo ni mfundo yakuti magazi amene anapakidwa pa nyumba za Aisiraeli m’dziko la Aiguputo anateteza ana oyamba, kuti mngelo asawawononge. Paulo anakamba za Akhristu odzozedwa monga mpingo wa ana oyamba kubadwa (Aheb. 12:23), komanso za Khristu monga mpulumutsi wawo kupitila m’magazi ake. (1 Ates. 1:10; Aef. 1:7) Pa mwambo wa Pasika sanali kufunika kuphwanya fupa lililonse la nkhosa. Ulosi unakambilatu kuti palibe fupa ngakhale limodzi la Yesu limene lidzathyoledwa, ndipo izi zinakwanilitsidwa pa imfa yake. (Sal. 34:20; Yoh. 19:36) Conco, mwambo wa Pasika umene Ayuda anali kucita kwa zaka zambili, unali mthunzi wa cimodzi mwa zinthu zochulidwa m’Cilamulo, komanso kucitila umboni kuti Yesu Khristu ndiye “Mwanawankhosa wa Mulungu.”—Aheb. 10:1; Yoh. 1:29.
w13 12/15 20 ¶13-14
‘Ici Cidzakhala Cikumbutso Kwa Inu’
13Pamene ana anali kukula, makolo awo anali kuwaphunzitsa mfundo zofunika zokhudza Pasika. Imodzi mwa mfundozo inali yakuti Yehova amateteza olambila ake. Ana anaphunzila kuti Yehova ni Mulungu wamoyo, ndiponso kuti ni weni-weni amene amasamalila anthu ake na kuwathandiza. Iye anasonyeza zimenezi mwa kuteteza ana oyamba kubadwa a Aisiraeli “pamene anali kupha Aiguputo ndi mlili.”
14Masiku ano, makolo acikhristu safunikila kweni-kweni kumafotokozela ana awo tanthauzo la Pasika caka na caka. Koma kodi inu makolo mumaphunzitsa ana anu mfundo yakuti Mulungu amateteza anthu ake? Kodi mumawaonetsa kuti mumakhulupilila na mtima wonse kuti Yehova ndi Mtetezi wa anthu ake ngakhale masiku ano? (Sal. 27:11; Yes. 12:2) Ndipo kodi mumawaphunzitsa zimenezi mwaubwenzi kapena monga mukuwapatsa uphungu? Kuphunzila zimenezi pa kulambila kwanu kwa pabanja kudzathandiza banja lanu kupita patsogolo mwa kuuzimu.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
it-2 582 ¶2
Pasika
Milili 10 imene inagwela Aiguputo inaonetsa kuti inali cilango pa milungu ya Iguputo, maka-maka mlili wa namba 10, umene unapha ana oyamba kubadwa. (Eks. 12:12) Nkhosa yamphongo inali yopatulika kwa mlungu wawo Ra, conco kwa Aiguputo, kuwaza magazi a nkhosa ya mwambo wa Pasika pamakomo a nyumba za Aisiraeli kunali kunyoza mulungu wawo. Komanso, ng’ombe yamphongo inali yopatulika. Ndipo kuphedwa kwa mwana woyamba wa ng’ombe yamphongo kunakhumudwitsa kwambili mulungu wawo Osirisi. Farao anali kulambilidwa monga mwana wamwamuna wa Ra. Kuphedwa kwa mwana woyamba kubadwa wa Farao kunaonetsa kusoŵa mphamvu kwa Ra komanso Farao.
it-1 504 ¶1
Msonkhano
Mbali yocititsa cidwi ya “misonkhano yopatulika” imeneyi ni yakuti pa nthawi ya misonkhanoyi anthu sanali kufunika kugwila nchito yolemetsa kwambili. Mwacitsanzo, tsiku loyamba komanso la 7 la cikondwelelo ca mikate yopanda cofufumitsa, inali “misonkhano yopatulika,” imene Yehova anati: “Masiku amenewa musamadzagwile nchito. Koma cakudya coti munthu aliyense adye, cimeneco cokha muzidzaphika.” (Eks. 12:15, 16) Komabe, pa nthawi ya “misonkhano yopatulika,” ansembe anali kutangwanika kupeleka nsembe kwa Yehova (Lev. 23:37, 38), uku sikunali kuphwanya lamulo lililonse lokhudza nchito imene anali kugwila tsiku lililonse. Nthawi ya zocitika zimenezi siinali yakuti anthu akhale manja lende. Inali nthawi yakuti apindule kwambili mwauzimu. Pa Sabata ya wiki iliyonse, anthu anali kusonkhana pamodzi kuti alambile Mulungu na kulandila malangizo. Ndiyeno anali kulimbikitsidwa mwa kuŵelenga pamaso pa anthu, komanso kufotokozela mawu a Mulungu. Pambuyo pake anayamba kucita zimenezi m’masunagoge. (Mac. 15:21) Conco, pa nthawi imene anthu sanali kugwila nchito yolemetsa pa Sabata, kapena pa “misonkhano yopatulika” ina, iwo anali kudzipeleka kupemphela na kusinkha-sinkha za Mlengi komanso cifunilo cake.