Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki
DECEMBER 7-13
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LEVITIKO 10–11
“Cikondi pa Yehova Ciyenela Kukhala Cacikulu Kuposa Cikondi pa Acibale”
it-1 1174
Zosaloleka Mwalamulo
Moto na Zofukiza Zosaloleka. Pa Levitiko 10:1, liwu la Ciheberi lakuti zar (liwu lacikazi, za·rahʹ; kweni-kweni kutanthauza, cacilendo) linagwilitsidwa nchito pokamba za moto umene ana a Aroni anaseŵenzetsa pamaso pa Yehova, umene unacititsa kuti iye awaphe na moto. Lembali limati unali “moto wosaloledwa ndi Yehova, umene iye sanawalamule.” (Lev. 10:2; Num. 3:4; 26:61) Pambuyo pake, Yehova anauza Aroni kuti: “Pamene mukubwela kucihema cokumanako, iwe ndi ana ako musamamwe vinyo kapena zakumwa zina zoledzeletsa, kuti mungafe. Limeneli ndi lamulo ku mibadwo yanu yonse mpaka kalekale, kuti muzisiyanitsa pakati pa cinthu copatulika ndi coipitsidwa ndiponso pakati pa codetsedwa ndi coyela. Kutinso muziphunzitsa ana a Isiraeli malamulo onse amene Yehova wanena kwa iwo kudzela mwa Mose.” (Lev. 10:8-11) Izi zionetsa kuti mwina Nadabu na Abihu anali oledzela, n’cifukwa cake anapeleka zofukiza pa moto umene Mulungu sanawalamule. Moto umenewo unali wosaloleka mwacionekele cifukwa ca nthawi imene anaupeleka, malo ake, kapena mmene anacitila popelekapo. N’kuthekanso kuti anaseŵenzetsa zofukiza zosiyana na zimene zafotokozedwa pa Ekisodo 30:34, 35. Kukhala oledzela sicinali cifukwa codzikhululukila pa chimo lawo.
w11 7/15 31 ¶16
Kodi Mwaloŵa mu Mpumulo wa Mulungu?
16 Aroni, amene anali mkulu wake wa Mose, anakumananso na vuto cifukwa ca ana ake aamuna aŵili. Ganizilani cisoni cimene Aroni anali naco pamene Yehova anawononga Nadabu ndi Abihu cifukwa copeleka kwa Yehova zofukiza pamoto wosaloledwa. N’zoona kuti izi zinacititsa kuti asacezenso na makolo awo. Koma nkhani sinathele pamenepa. Yehova analangiza Aroni ndi ana ake okhulupilika kuti asalile malilo awo. Iye anawauza kuti: “Musalekelele tsitsi lanu osalisamala, ndipo musang’ambe zovala zanu [polila] kuti mungafe ndiponso kuti Mulungu angakwiyile khamu lonseli.” (Lev. 10:1-6) Kodi tiphunzila ciani pamenepa? Tiyenela kukonda kwambili Yehova kuposa acibale athu osakhulupilika.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
Tifunika Kukhala Oyela m’Makhalidwe Athu Onse
18 Kuti tikhale oyela, tifunika kuphunzila Malemba mosamalitsa na kucita zimene Mulungu amafuna. Ganizilani za ana a Aroni, Nadabu ndi Abihu, amene anaphedwa cifukwa cofukiza “pamoto wosaloledwa,” mwina cifukwa cakuti anali okolewa. (Lev. 10:1, 2) Ndiyeno ganizilaninso zimene Mulungu anauza Aroni. (Ŵelengani Levitiko 10:8-11.) Kodi nkhani imeneyi itiphunzitsa kuti sitiyenela kumwa zakumwa zina zoledzeletsa tisanapite ku misonkhano yacikhristu? Ganizilani mfundo izi: Ife sitili pansi pa Cilamulo ca Mose. (Aroma 10:4) M’maiko ena, okhulupilila anzathu amamwa zakumwa zoledzeletsa mosapitilila malile pa cakudya asanapite ku misonkhano. Ndipo pamwambo wa Pasika, panali kukhala makapu anayi a vinyo. Poyambitsa mwambo wa Cikumbutso, Yesu anauza atumwi ake kuti amwe vinyo amene anali kuimila magazi ake. (Mat. 26:27) Baibo imaletsa kumwa moŵa mopitilila malile ndi kuledzela. (1 Akor. 6:10; 1 Tim. 3:8) Ndipo Akhristu ambili cikumbumtima cawo cimawaletselatu kumwa vinyo asanacite zinthu zilizonse za kuuzimu. Komabe, malinga ndi maiko, mikhalidwe imasiyana-siyana. Koma cofunika kwa Akhristu ndi ‘kusiyanitsa pakati pa cinthu copatulika ndi coipitsidwa,’ kuti akhale ndi khalidwe loyela limene limakondweletsa Mulungu.
it-1 111 ¶5
Nyama
Malamulo amenewa oletsa kudya nyama zina anakhudza cabe anthu amene anali pansi pa Cilamulo ca Mose, cifukwa pa Levitiko 11:8 pali mawu akuti: “Zikhale zodetsedwa kwa inu,” kutanthauza Aisiraeli. Pamene Cilamulo cinathetsedwa pa maziko a nsembe ya Khristu Yesu, malamulo amenewonso anathetsedwa, ndipo anthu tsopano anafunika kutsatila malamulo okhudza anthu onse, amene Mulungu anapeleka kwa Nowa pambuyo pa Cigumula.—Akol. 2:13-17; Gen. 9:3, 4.
DECEMBER 14-20
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LEVITIKO 12-13
“Phunzilamponi Kanthu pa Malamulo Okhudza Nthenda ya Khate”
Kodi Inatha Nchito Kapena Imakambilatu Zinthu Zimene Anthu Akalibe Kuzitulukila?
• Kupatula anthu odwala matenda oyambukila.
Cilamulo ca Mose cinakamba kuti anthu odwala matenda a khate ayenela kukhala kwaokha. Madokota anadziŵa kufunika koseŵenzetsa mfundo imeneyi pambuyo pa milili ya matenda a m’zaka za pakati pa 500 C.E. na 1500 C.E. Mpaka pano mfundo imeneyi yakhala yothandiza.—Levitiko, caputa 13 na 14.
Kodi Mudziŵa?
Ayuda akale anali kuopa khate limene linali lofala m’nthawi imeneyo. Nthenda yoopsa imeneyi inali kuwononga minyewa ya munthu wodwalayo n’kumupundula. Kunalibe mankhwala ocilitsa khate pa nthawiyo. M’malomwake, amene anali kudwala matendawa, anali na udindo wodziŵitsa ena kuti ali na khate.—Levitiko 13:45, 46.
it-2 238 ¶3
Khate
Pa zovala na m’nyumba. Khate linalinso kufalikila ku zovala zaubweya wa nyama kapena zansalu, kapenanso ku zinthu zina zopangidwa na cikopa. Nthawi zina nthendayo inali kutha akacapa cinthuco, ndipo zikakhala conco cinthuco anali kuciika kwacoka kwa nthawi inayake. Koma ngati nthenda yobiliŵila mopitila ku cikasu kapena yofiilila imeneyi ipitiliza osaleka, ndiye kuti linali khate loopsa ndipo cinthuco anali kucitentha. (Lev. 13:47-59) Ngati ku cipupa kwa nyumba kwaonekela maŵanga obiliŵila opita ku cikasu kapena ofiilila, wansembe anali kutseka nyumbayo kwa masiku. Nthawi zina anali kucotsa miyala imene pafalikila nthendayo na kulamula kuti apale mkati mwa nyumbayo. Miyalayo komanso dothi lomangila limene apala anali kukazitaya kunja kwa mzinda, kumalo odetsedwa. Nthendayo ikabwelelanso, wansembe anali kugamula kuti nyumbayo ni yodetsedwa ndipo inali kugwetsedwa. Zinthu zonse zimene anamangila nyumbayo anali kukazitaya ku malo odetsedwa. Koma ngati wansembe wakamba kuti nyumbayo ni yoyela, panali kukhala makonzedwe oiyeletsa. (Lev. 14:33-57) Ena amakamba kuti khate limene linali kufalikila ku zovala kapena m’nyumba linali lamtundu wachuku. Koma palibe umboni wokwanila wotsimikizila zimenezi.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
w04 5/15 23 ¶2
Mfundo Zazikulu za M’buku la Levitiko
12:2, 5—N’cifukwa ciani mkazi anali kukhala “wodetsedwa” akabeleka mwana? Ziwalo zobelekela zinapangidwa kuti zizibeleka munthu wangwilo. Koma cifukwa ca ucimo wobadwa nawo, ana anapatsidwa moyo wopanda ungwilo ndi wocimwa. Kukhala “wodetsedwa” kwa nthaŵi yocepa cifukwa ca kubeleka mwana, ndiponso zinthu zina, monga kukhala padela kwa akazi, kapena kuti kusamba, ndi kugona uipa kwa amuna, kapena kuti kutulutsa ubwamuna, kunali kuwakumbutsa Aisiraeliwo za ucimo wobadwa nawo umenewu. (Levitiko 15:16-24; Salimo 51:5; Aroma 5:12) Malamulo amene analipo othandiza kuti munthu ayeletsedwe, anali kuthandiza Aisiraeli kuzindikila kufunika kwa nsembe ya dipo yophimba ucimo wa anthu na kuwabwezeletsa ku ungwilo. Motelo, Cilamulo cinakhala ‘mtsogoleli wowafikitsa kwa Khristu.’—Agalatiya 3:24.
Kodi Inatha Nchito Kapena Imakambilatu Zinthu Zimene Anthu Akalibe Kuzitulukila?
• Nthawi yabwino yocita mdulidwe.
Malinga ni Cilamulo ca Mulungu, mwana wa mwamuna anali kudulidwa pa tsiku la namba 8 kucokela pamene anabadwa. (Levitiko 12:3) Capezeka kuti magazi a makanda amatha kuundana mosavuta pakapita wiki imodzi kucokela pamene anabadwa. M’nthawi za m’Baibo kunalibe njila zamakono zotsogola zacipatala. Koma kucita mdulidwe pambuyo pa wiki imodzi kunali citetezo cabwino.
DECEMBER 21-27
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LEVITIKO 14-15
“Kulambila Koona Kumafuna Kukhala Oyela”
it-1 263
Kusamba
Aisiraeli anali kufunika kusamba mwapadela kuti adziyeletse pa zifukwa zosiyana-siyana. Munthu aliyense amene wacila nthenda ya khate, aliyense amene wakhudza cinthu cimene munthu wa nthenda “ya kukha kumalisece” wagwila, mwamuna aliyense amene watulutsa umuna usiku, mkazi akaleka kusamba kapena akaleka kukha magazi cifukwa ca nthenda ya kukha magazi, kapena aliyense wogonana na mkazi kapena mwamuna, anali kukhala “wodetsedwa,” ndipo anali kufunika kusamba. (Lev. 14:8, 9; 15:4-27) Munthu amene ali m’hema imene muli mtembo wa munthu, kapena wokhudza mtembo wa munthu anali kukhala “wodetsedwa” ndipo anali kufunika kumuyeletsa na madzi oyeletsela. Aliyense wokana kutsatila malangizo amenewa anali kuphedwa “kuti asakhalenso pakati pa mpingowo, cifukwa waipitsa malo opatulika a Yehova.” (Num. 19:20) Conco, mpake kuti mophiphilitsila, kusamba kumaimila kukhala pa ubale wabwino na Yehova. (Sal. 26:6; 73:13; Yes. 1:16; Eze. 16:9) Kusamba m’mawu a Yehova a coonadi, amene akuyelekezedwa na madzi, kungathe kuyeletsa munthu.—Aef. 5:26.
it-2 372 ¶2
Kusamba kwa akazi
Mkazi anali kuonedwanso kuti ni wodetsedwa pa nthawi imene akukha magazi pamene si nthawi yake yosamba, kapena “akapitiliza kukha magazi nthawi yake yokhala odetsedwa cifukwa ca kusamba kwake itatha.” Pa nthawi imeneyo, ciliconse cimene wagonapo kapena kukhalapo cinali kukhala codetsedwa. Komanso aliyense amene wakhudza cinthuco anali kukhala wodetsedwa. Mkazi akasiya kukha magaziko, anali kufunika kuŵelenga masiku 7, ndipo pambuyo pake anali kukhala woyela. Pa tsiku la 8, anali kutenga njiwa ziŵili kapena ana aŵili a nkhunda na kupita nawo kwa wansembe. Wansembeyo anali kupeleka kwa Yehova mbalamezo, imodzi monga nsembe ya macimo, ina monga nsembe yopseleza.—Lev. 15:19-30.
it-1 1133
Malo Oyela
2. Cihema cokumanako, pambuyo pake, kacisi. Malo onse, kuphatikizapo bwalo la cihema na mabwalo a kacisi, anali malo oyela. (Eks. 38:24; 2 Mbiri 29:5; Mac. 21:28) Zinthu zikulu-zikulu zimene zinali kukhala m’bwalo la cihema ni guwa lansembe komanso beseni lamkuwa. Zimenezi zinali zinthu zoyela. Anthu okhawo amene anali oyela mwalamulo ndiwo anali kuloŵa m’bwalo la cihema nthawi iliyonse. Mofananamo, munthu aliyense wodetsedwa sanali kuloledwa kuloŵa m’mabwalo a kacisi. Mwacitsanzo, mkazi wodetsedwa sanali kuloledwa kugwila cinthu ciliconse coyela kapena kuloŵa m’malo oyela. (Lev. 12:2-4) Komanso n’zoonekelatu kuti Aisiraeli akapitiliza kukhala odetsedwa, zinali kuonedwanso kuti akudetsa cihema. (Lev. 15:31) Anthu amene anafuna kupeleka nsembe podziyeletsa ku nthenda ya khate, anali kungofika nazo pacipata ca bwalo la cihema nsembe zawozo. (Lev. 14:11) Munthu aliyense wodetsedwa sanali kuloledwa kudya nawo nsembe yaciyanjano pa cihema kapena pa kacisi. Munthu akacita zimenezi, cilango cake cinali kuphedwa.—Lev. 7:20, 21.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
it-1 665 ¶5
Khutu
Pa nthawi yolonga unsembe mu Isiraeli, Mulungu analamula Mose kuti atengeko magazi a nkhosa yamphongo yolongela unsembe n’kuwapaka pakhutu la kudzanja lamanja la Aroni na ŵana ŵake, komanso kudzanja lamanja na kumwendo wa kudzanja lamanja, poonetsa kuti zimene amvetsela, nchito imene acita, ndiponso kayendedwe kawo ziyenela kukhala zogwilizana na zocitika za pamalowo. (Lev. 8:22-24) N’zimenenso zinali kucitika kwa munthu wakhate amene wacila. Cilamulo cinakamba kuti wansembe azitenga ena mwa magazi a nkhosa yamphongo imene munthuyo wapeleka monga nsembe yopalamula, komanso ena mwa mafuta amene wapeleka nsembe na kuwapaka pakhutu la kudzanja lamanja la munthuyo. (Lev. 14:14, 17, 25, 28) Zofananako na zimenezi zinali kucitikanso kwa munthu amene wasankha kukhala kwa mbuye wake monga kapolo mpaka kale-kale. Kapolo akasankha zimenezi, anali kupita naye pafelemu, ndipo mbuye wake anali kum’boola khutu na coboolela. Mwacionekele, cidindo cokhalitsa cimeneci, coikidwa pa khutu, ciwalo cimene timaseŵenzetsa pomvetsela, cinali cizindikilo cakuti kapoloyo ni wofunitsitsa kupitiliza kumvela mbuye wake.—Eks. 21:5, 6.
g 1/06 14, bokosi
Nkhungu Imathandiza Komanso Imawononga
KODI NKHUNGU INACHULIDWAPO M’BAIBO?
Baibo imachula za “nthenda yakhate m’nyumba,” kutanthauza m’nyumba mweni-mwenimo. (Levitiko 14:34-48) Ena amati n’kutheka kuti vuto limeneli, lomwe limachedwanso kuti “khate loopsa,” linali nguwi kapena nkhungu, koma zimenezi n’zosadziŵika bwino-bwino. Kaya vutoli linali ciani, koma Cilamulo ca Mulungu cinalangiza eninyumba kuti azicotsa miyala imene ili na vutoli, kupala mkati monse mwa nyumbayo, ndiponso kukataya kunja kwa mzinda, “kumalo odetsedwa,” cinthu ciliconse cimene akucikayikila kuti cingakhale na vutoli. Mliliwo ukabwelanso, nyumba yonseyo anali kuicha yodetsedwa, ndipo anali kuipasula n’kukataya zimene agumulazo. Malangizo atsatane-tsatane a Yehova anasonyeza kuti anali kuwakonda kwambili anthu ake ndipo anali kufuna kuti azikhala athanzi.
DECEMBER 28–JANUARY 3
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LEVITIKO 16-17
“Zimene Tingaphunzile pa Zocitika za pa Tsiku la Mwambo Wophimba Macimo”
Mfundo Zimene Tingaphunzile mu Buku la Levitiko
4 Ŵelengani Levitiko 16:12, 13. Yelekezelani kuti mukuona zimene zinali kucitika pa tsiku la Mwambo Wophimba Macimo. Mkulu wa nsembe akuloŵa m’cihema. Ndipo aka ni koyamba pa nthawi zitatu zimene afunika kuloŵa m’Malo Oyela Koposa pa tsikuli. Pamene akuloŵa, dzanja lina wanyamula ciwiya codzala na zofukiza zonunkhila, ndipo dzanja linalo wanyamula ciwiya ca golide cofukizila cimene n’codzala na makala amoto. Atafika pa nsalu yochinga khomo loloŵela ku Malo Oyela Koposa, iye akuima pang’ono. Ndiyeno mwaulemu kwambili, akuloŵa m’cipinda ca Malo Oyela Koposa na kuima pafupi na likasa la pangano. Mophiphilitsa, iye waima pamaso peni-peni pa Yehova Mulungu! Ndiyeno, mosamala wansembeyo akuthila zofukiza zopatulika zija pa makala amoto, ndipo fungo lonunkhila bwino likudzala m’cipinda conse. Iye akutuluka m’cipindaco. Koma pambuyo pake, adzaloŵanso m’Malo Oyela Koposa atanyamula magazi a nsembe zophimba macimo. Onani kuti mkulu wa ansembe coyamba anali kufukiza zofukiza asanapeleke magazi a nsembe zophimba macimo.
Mfundo Zimene Tingaphunzile mu Buku la Levitiko
5 Kodi tiphunzilapo ciani tikaganizila mmene mkulu wa ansembe anali kuseŵenzetsela zofukiza pa tsiku la Mwambo Wophimba Macimo? Baibo imaonetsa kuti mapemphelo a atumiki okhulupilika a Yehova ali ngati zofukiza. (Sal. 141:2; Chiv. 5:8) Kumbukilani kuti mkulu wansembe anali kubweletsa zofukiza pa maso pa Yehova mwaulemu kwambili. Mofananamo, pamene tipemphela kwa Yehova, tiyenela kupemphela mwaulemu kwambili. Timacita zimenezi cifukwa timamulemekeza kwambili. Timayamikila ngako kuti Mlengi wacilengedwe conse, amatilola kukamba naye na kukhala naye pafupi, monga mmene tate amacitila na mwana wake. (Yak. 4:8) Iye watilola kukhala mabwenzi ake. (Sal. 25:14) Timayamikila kwambili mwayi umenewo, ndipo sitifuna kucita ciliconse cimene cingam’khumudwitse.
Mfundo Zimene Tingaphunzile mu Buku la Levitiko
6 Kumbukilani kuti mkulu wansembe asanapeleke nsembe, coyamba anali kufukiza zofukiza. Anali kucita izi n’colinga cakuti Mulungu akondwele naye pamene apeleka nsembezo. Kodi tiphunzilapo ciani? Pamene Yesu anali pa dziko lapansi, anacita zinazake zofunika kwambili asanapeleke moyo wake monga nsembe. Zimene anacitazo zinali zofunika kwambili kuposa kupulumutsa mtundu wa anthu. Kodi anacita ciani? Anakhalabe wokhulupilika kwa Yehova mu umoyo wake wonse pa dziko lapansi kuti Yehova alandile nsembe yake. Mwa kucita zimenezo, Yesu anaonetsa kuti kutsatila malamulo a Yehova n’kumene kungatithandize kukhala na umoyo wabwino. Iye anakweza ucifumu wa Atate wake. Anaonetsa kuti ulamulilo wa Yehova ndiwo wabwino komanso wacilungamo.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
it-1 226 ¶3
Azazeli
Monga mmene mtumwi Paulo anafotokozela, pamene Yesu anapeleka moyo wake wangwilo monga nsembe ya macimo a anthu, anacita zazikulu kwambili kuposa zimene zinali kukwanilitsidwa mwa kupeleka “magazi a ng’ombe zamphongo ndi mbuzi.” (Aheb. 10:4, 11, 12) Conco anakhala ngati mbuzi “ya Azazeli,” cifukwa “anatinyamulila matenda athu,” komanso “anabayidwa cifukwa ca zolakwa zathu.” (Yes. 53:4, 5; Mat. 8:17; 1 Pet. 2:24) Iye “ananyamula macimo” a anthu onse amene amakhulupilila nsembe yake. Yesu anaonetsa colinga ca Mulungu cothetselatu ucimo kwamuyaya. Mwanjila zimenezi, mbuzi “ya Azazeli” imacitila cithunzi nsembe ya Yesu Khristu.
Cifukwa Cake Tifunika Kukhala Oyela
10 Ŵelengani Levitiko 17:10. Yehova analamula Aisiraeli kuti asadye “magazi alionse.” Akhristu nawonso afunika kumvela lamulo lopewa magazi a nyama kapena a munthu. (Mac. 15:28, 29) Timacita mantha tikaganiza zocita zinthu zimene zingacititse kuti Mulungu atikane na kuticotsa mumpingo wake. Motelo, timam’konda ndipo timafunitsitsa kumvela malamulo ake. Kaya moyo wathu ukhale pangozi, sitidzagonja kwa anthu amene sadziŵa Yehova amene angatikakamize kuti tisamvele Mulungu. Tidziŵa kuti anthu ena angatinyoze cifukwa cokana kuikidwa magazi, koma timafuna kumvela Mulungu. (Yuda 17, 18) N’ciani cingatithandize kuti tikhale ‘otsimikiza mtima kwambili’ kukana kudya kapena kuikidwa magazi?—Deut. 12:23.