LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb24 March masa. 14-15
  • April 29–May 5

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • April 29–May 5
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2024
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2024
mwb24 March masa. 14-15

APRIL 29–MAY 5

MASALIMO 34-35

Nyimbo 10 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. “Nidzatamanda Yehova Nthawi Zonse”

(Mph. 10)

Davide anatamanda Yehova ngakhale pokumana na mavuto (Sal. 34:1; w07 3/1 22 ¶11)

Davide anadzitama mwa Yehova, osati mwa iye mwini (Sal. 34:2-4; w07 3/1 22 ¶13)

Mawu a Davide acitamando analimbikitsa mabwenzi ake (Sal. 34:5; w07 3/1 23 ¶15)

David speaking to his men in a cave.

Davide atapulumuka kwa Abimeleki, amuna 400 osakondwa na ulamulilo wa Sauli anapita kukagwilizana naye m’cipululu. (1 Sam. 22:1, 2) Mwina Davide anali kuganizila amunawa polemba Salimoli.—Sal. 34, tumawu twa pamwamba.

DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ningakamutamande bwanji Yehova pokamba na munthu ku msonkhano wa mpingo wotsatila?’

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal. 35:19—Kodi pempho la Davide loti asalole adani ake ‘kum’tsinzinila diso’ likutanthauza ciyani’? (w06 5/15 20 ¶1)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutigaŵilako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal. 34:1-22 (th phunzilo 5)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 2) ULALIKI WAMWAYI. Makambilano atha musanamulalikile n’komwe. (lmd phunzilo 1 mfundo 4)

5. Kubwelelako

(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. (lmd phunzilo 2 mfundo 4)

6. Kufotokoza Zimene Mumakhulupilila

(Mph. 5) Citsanzo. ijwfq 59—Mutu: Kodi a Mboni za Yehova Amadziŵa Bwanji Ngati Holide Inayake ni Yovomelezeka? (th phunzilo 17)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 59

7. Njila Zitatu Zotamandila Yehova pa Misonkhano

(Mph. 15) Kukambilana.

Zithunzi: A sister praising Jehovah at a meeting. 1. She converses with two other sisters before the meeting. 2. She gives a comment. 3. She sings enthusiastically with the congregation.

Misonkhano ya mpingo imatipatsa mipata yotamandila Yehova. Nazi njila zitatu.

Makambilano: Pokambilana na ena, chulan’koni za ubwino wa Yehova. (Sal. 145:1, 7) Kodi munamvako kapena kuŵelengapo mfundo ina yake imene inakupindulilani? Kodi munakumanako na cocitika cosangalatsa mu ulaliki? Kodi pali munthu wina amene anakulimbikitsam’poni mwa zokamba kapena zocita zake? Kodi munaonako cina cake m’cilengedwe cimene cinakukondweletsani? Zonsezi ni mphatso zocoka kwa Yehova. (Yak. 1:17) Muzifika mwamsanga ku misonkhano kuti muzipeza nthawi yoceza na anthu ena.

Ndemanga: Muziyesetsa kuyankhapo ngakhale kamodzi kokha pa msonkhano uliwonse. (Sal. 26:12) Mungayankhe funso lolembedwa, kupeleka ndemanga yowonjezela, kufotokoza lemba, zithunzi, kapena mmene tingaseŵenzetsele zimene taphunzila. Popeza si inu nokha amene mudzanyamula dzanja kuti muyankhepo, konzekelani ndemanga zingapo. Ngati ndemanga zathu sizipitilila masekondi 30, anthu ambili adzakhala na mpata wopeleka nsembe yotamanda Mulungu.—Aheb. 13:15.

Nyimbo: Imbani nyimbo za Ufumu mokondwela. (Sal. 147:1) Ngati mumpingo wanu muli ofalitsa ambili, si nthawi zonse pamene mungapelekepo ndemanga. Komabe nthawi zonse mukhoza kumaimbila capamodzi nyimbo za Ufumu. Ngakhale mutakhala mulibe luso loimba, Yehova amakondwelabe na kuimba kwanu pa misonkhano! (2 Akor. 8:12) Muzikonzekela mwa kuyeseza nyimbozi muli kunyumba.

Tambitsani VIDIYO yakuti Mbili ya Kupita Patsogolo kwa Gulu Lathu—Mphatso ya Nyimbo, Gawo 1. Kenako funsani omvela kuti:

Kumayambililo kwa gulu lathu lamakono, tinaonetsa bwanji kuti kuimba nyimbo zotamanda Yehova n’kofunika?

8. Phunzilo la Baibo la Mpingo

(Mph. 30) bt mutu 9 ¶1-7, mawu oyamba a cigawo 3 na bokosi pa tsa. 70

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo Yatsopano ya Msonkhano wa Cigawo wa 2024 na Pemphelo

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani