MAY 6-12
MASALIMO 36-37
Nyimbo 87 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. “Usakhumudwe Cifukwa ca Anthu Oipa”
(Mph. 10)
Anthu oipa amatibweletsela mavuto ambili (Sal. 36:1-4; w17.04 10 ¶4)
Tikamasungila mkwiyo “anthu oipa” timadzivulaza tokha (Sal. 37:1, 7, 8; w22.06 10 ¶10)
Kukhulupilila malonjezo a Yehova kumatipatsa mtendele (Sal. 37:10, 11; w03-CN 12/1 14 ¶20)
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi nimathela nthawi yoculuka kutamba zocitika zoipa komanso zankhanza panyuzi?’
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
Sal. 36:6—Kodi wamasalimo ayenela kuti anatanthauzanji ponena kuti cilungamo ca Yehova “cili ngati mapili akulu-akulu [kapena kuti, “cili ngati mapili a Mulungu,” mawu a m’munsi]”? (it-2-E 445)
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutigaŵilako?
3. Kuŵelenga Baibo
(Mph. 4) Sal. 37:1-26 (th phunzilo 10)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 3) KU NYUMBA NA NYUMBA. (lmd phunzilo 1 mfundo 5)
5. Kubwelelako
(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. Yambitsani phunzilo la Baibo kwa munthu amene m’mbuyomu anakana kuphunzila. (lmd phunzilo 9 mfundo 4)
6. Nkhani
(Mph. 5) ijwbv 45—Mutu: Kodi Salimo 37:4 itanthauza ciyani? (th phunzilo 13)
Nyimbo 33
7. Kodi Mwaikonzekela “Nthawi ya Mavuto”?
(Mph. 15) Kukambilana.
Abale na alongo padziko lonse afeledwa okondedwa awo na kutaikilidwa zinthu zawo, cifukwa ca matsoka a zacilengedwe komanso oyambitsidwa na anthu. (Sal. 9:9, 10) Zoona zake n’zakuti “nthawi ya mavuto” imagwela munthu aliyense. Conco, tonsefe tifunika kukhala okonzeka kukumana na mavuto.
Kuwonjezela pa kukonzekela kuthupi,a n’ciyani cingatithandize kupilila tikagweledwa matsoka?
Konzekeletsani maganizo anu: Dziŵani kuti ngozi zimacitika ndithu, ndipo ganizilani zimene mungacite ngozi ikacitika. Pewani kukondetsetsa zinthu zanu zakuthupi. Mukatelo mudzacita zinthu mwanzelu na kupanga zisankho zimene zingapulumutse moyo wanu komanso wa anthu ena, m’malo moyesa kuteteza katundu wanu. (Gen. 19:16; Sal. 36:9) Mudzathanso kupilila na kusapanikizika maganizo mukataikilidwa zinthu zanu pambuyo pa ngozi.—Sal. 37:19
Konzekani mwauzimu: Khalani na cikhulupililo colimba cakuti Yehova adzakusamalilani. (Sal. 37:18) Tsoka lisanacitike, muzikumbukila kuti nthawi zonse Yehova adzatsogolela atumiki ake na kuŵathandiza ngakhale titataya zinthu zonse zakuthupi n’kupulumutsa moyo wathu wokha.—Yer. 45:5; Sal. 37:23, 24
Tikamakumbukila malonjezo a Yehova nthawi zonse, timamupanga kukhala malo athu “acitetezo camphamvu pa nthawi ya mavuto.”—Sal. 37:39.
Tambitsani VIDIYO YAKUTI Kodi Mwakonzekela Tsoka la Zacilengedwe? Kenako funsani omvela kuti:
Kodi Yehova angatithandize bwanji pakacitika tsoka la zacilengedwe?
Kodi tingacite ciyani kuti tikhale okonzeka?
Tingaŵathandize bwanji anthu ena omwe akhudzidwa na matsoka a zacilengedwe?
8. Phunzilo la Baibo la Mpingo
(Mph. 30) bt mutu 9 ¶8-16