MAY 20-26
MASALIMO 40-41
Nyimbo 102 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. N’cifukwa Ciyani Ni Cinthu Canzelu Kuthandiza Anthu Ena?
(Mph. 10)
Kuthandiza anthu ena kumatibweletsela cimwemwe (Sal. 41:1; w18.08 22 ¶16-18)
Yehova amathandiza anthu omwe amathandiza anzawo (Sal. 41:2-4; w15 12/15 24-25 ¶7)
Yehova amalemekezeka tikamathandiza ena (Sal. 41:13; Miy. 14:31; w17.09 12 ¶17)
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi pali wina wake mumpingo mwathu amene angafunike kumuthandiza kuseŵenzetsa mokwanila JW Library?’
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
Sal. 40:5-10—Kodi pemphelo la Davide litiphunzitsa ciyani pa nkhani yovomeleza udindo wa Yehova monga Wolamulila? (it-2-E 16)
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutigaŵilako?
3. Kuŵelenga Baibo
(Mph. 4) Sal. 40:1-17 (th phunzilo 12)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 3) ULALIKI WAMWAYI. Yambani kukambilana na munthu wooneka wokondwela. (lmd phunzilo 2 mfundo 3)
5. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. Yambani kukambilana na munthu wooneka wosakondwa. (lmd phunzilo 3 mfundo 5)
6. Kupanga Ophunzila
(Mph. 5) lff phunzilo 14 mfundo 6. Kambilanani mfundo imodzi m’nkhani yakuti “Tamandani Yehova Pakati pa Mpingo” pa mbali yakuti “Fufuzani,” na wophunzila amene amadodoma kuyankhako pa misonkhano. (th phunzilo 19)
Nyimbo 138
7. Muzicitila Zabwino Anthu Okalamba
(Mph. 15) Kukambilana.
Yehova amayamikila zonse zimene okalamba okhulupilika amacita mumpingo, nafenso timaŵayamikila. (Aheb. 6:10) Kwa zaka, iwo akhala akucita zambili pophunzitsa mawu a Mulungu, pophunzitsa ena nchito komanso polimbikitsa alambili anzawo. Mosakayikila inunso mungakumbukile mmene anakuthandizilani. Kodi mungaonetse bwanji kuti mumayamikila zonse zimene anacita, komanso zimene akucita pali pano mumpingo?
Tambitsani VIDIYO YAKUTI ‘Kucitila Zabwino Abale ndi Alongo Athu.’ Kenako funsani omvela kuti:
Kodi Ji-Hoon anaphunzila ciyani kwa m’bale Ho-jin Kang?
N’ciyani cimakupangitsani kuŵakonda okalamba a mumpingo mwanu?
Kodi titengapo phunzilo lanji pa fanizo la Msamariya wacifundo?
N’cifukwa ciyani muona kuti Ji-Hoon anacita bwino kuitanako ena kudzathandiza m’bale Ho-jin Kang?
Tikamaganizila kwambili zosoŵa za okalamba a mumpingo mwathu, tingapeze njila zambili zoŵathandizila. Mukaona kuti akusoŵa cina cake, ganizilani mmene mungaŵathandizile.—Yak. 2:15, 16.
Ŵelengani Agalatiya 6:10. Kenako funsani omvela kuti:
Kodi ni zabwino ziti zimene mungacitile okalamba mumpingo mwanu?
8. Phunzilo la Baibo la Mpingo
(Mph. 30) bt mutu 10 ¶1-4, bokosi pa tsa. 79