LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb24 May masa. 6-7
  • May 27–June 2

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • May 27–June 2
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2024
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2024
mwb24 May masa. 6-7

MAY 27–JUNE 2

MASALIMO 42-44

Nyimbo 86 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Pindulani Kwathunthu na Maphunzilo Ocokela kwa Mulungu

(Mph. 10)

Muzilambila Yehova pamodzi na anthu ena, maka-maka pamasom’pamaso ngati n’zotheka (Sal. 42:​4, 5; w06-CN 6/1 9 ¶4)

Muzipemphela musanayambe kuphunzila mawu a Mulungu (Sal. 42:8; w12-CN 1/15 15 ¶2)

Muzilola coonadi ca m’Baibo kukutsogolelani mu zinthu zonse pa umoyo wanu (Sal. 43:3)

Alongo akumvetsela mwachelu pa msonkhano wa cigawo komanso akulemba manotsi.

Maphunzilo ocokela kwa Mulungu amatipatsa mphamvu zopilila mayeso, komanso amatithandiza kusunga lumbilo la kudzipatulila kwathu.—1 Pet. 5:10; w16.09 5 ¶11-12.

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal. 44:19—Kodi mawu akuti “kumalo amene mimbulu imakhala” ayenela kuti atanthauza ciyani? (it-1-E 1242)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutigaŵilako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal. 44:​1-26 (th phunzilo 11)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 4) KU NYUMBA NA NYUMBA. M’pempheni kuti muyambe kuphunzila naye Baibo. (lmd phunzilo 5 mfundo 5)

5. Kubwelelako

(Mph. 5) KU NYUMBA NA NYUMBA. Muitanileni ku nkhani ya anthu onse yotsatila. Tambitsani vidiyo yakuti N’ciani Cimacitika ku Nyumba ya Ufumu? (lmd phunzilo 7 mfundo 5)

6. Nkhani

(Mph. 3) lmd zakumapeto A mfundo 4—Mutu: Munthu Aliyense Adzakhala na Thanzi Langwilo. (th phunzilo 2)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 21

7. Pangani Zisankho Zanzelu pa Nkhani ya Nchito na Maphunzilo

(Mph. 15) Kukambilana.

Zithunzi: M’bale wacinyamata akuŵelenga Baibo na kuganizila adzacita akatsiliza sukulu. 1. Akukambilana na mlangiza wa ku sukulu. 2. Ali ku Sukulu ya Alengezi a Ufumu. 3. Akulalikila ku dziko lina.

Inu acinyamata, kodi mukuganizila zimene mudzacita mukatsiliza sukulu? Mwina munaganizilapo kale za nchito imene ingadzakuthandizeni kucita upainiya. Kapena mukuganizila kucitako maphunzilo owonjezela okuthandizani kukhala na luso lina lake, kupeza laisensi, kapena dipuloma imene ingakuthandizeni kupeza nchito yotelo. Imeneyi ni nthawi yokondweletsa kwambili pa umoyo wanu! Koma pamakhala zoculuka zimene mungasankhe, moti simungadziŵe kuti musankha ciyani. Mwinanso mungavutike kusankha cifukwa cofuna kukondweletsa anthu ena. N’ciyani cingakuthandizeni kupanga zisankho zanzelu?

Ŵelengani Mateyu 6:​32, 33. Kenako funsani omvela kuti:

  • N’cifukwa ciyani n’cinthu canzelu kukhala na zolinga zauzimu zotsimikizika musanapange cisankho cofunika pa nkhani ya nchito na maphunzilo?

  • Kodi makolo angaŵathandize bwanji ana awo kugwilitsa nchito mfundo ya pa Mateyu 6:​32, 33?—Sal. 78:​4-7

Musalole kuti mtima wofuna kukhala na ndalama zambili kapena kufuna wofuna kuchuka ukusonkhezeleni popanga zisankho. (1 Yoh. 2:​15, 17) Kumbukilani kuti kungokhala na cuma cambili kungalepheletse munthu kumvetsela uthenga wa Ufumu. (Luka 18:​24-27) Ngati munthu akufuna-funa cuma cakuthupi cimakhala covuta kuti akule kuuzimu.—Mat. 6:24; Maliko 8:36.

Tambitsani VIDIYO YAKUTI Samalani Kuti Musadalile Zinthu Zosakhalitsa—Cuma. Kenako funsani omvela kuti:

  • Kodi Miyambo 23:​4, 5 ingakuthandizeni bwanji kupanga zisankho zanzelu?

ZIMENE MUNGACITE

  • Dziikileni zolinga zauzimu zing’ono-zing’ono komanso zikulu-zikulu

  • Onetsetsani kuti zimene mudzasankha pa nkhani ya maphunzilo komanso nchito zisakulepheletseni kukwanilitsa zolinga zanu zauzimu

  • Sankhani maphunzilo othandizadi ndipo khalani okonzeka kusintha. Ngati mwasankha kucitako maphunzilo owonjezela, onetsetsani kuti nchito zimene mukufunila maphunzilowo zimapezekadi.

8. Phunzilo la Baibo la Mpingo

(Mph. 30) bt mutu 10 ¶5-12

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 47 na Pemphelo

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani