JUNE 3-9
MASALIMO 45-47
Nyimbo 27 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
Yesu na mkwatibwi wake, amene ni a 144,000
1. Nyimbo ya Ukwati wa Mfumu
(Mph. 10)
Salimo 45 imakamba za ukwati wa Mfumu Mesiya (Sal. 45:1, 13, 14; w14-CN 2/15 9-10 ¶8-9)
Ukwati wa Mfumu udzakhalako Aramagedo ikadzacitika (Sal. 45:3, 4; w22.05 17 ¶10-12)
Anthu onse adzadalitsidwa cifukwa ca ukwati umenewu (Sal. 46:8-11; it-2-E 1169)
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ‘mtima wanga umasangalala kwambili’ kulengeza uthenga wabwino wonena za Mfumu yathu, Yesu Khristu?’—Sal. 45:1.
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
Sal. 45:16—Kodi vesiyi itiphunzitsa kuti umoyo udzakhala wotani m’Paradaiso? (w17.04 11 ¶9)
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutigaŵilako?
3. Kuŵelenga Baibo
(Mph. 4) Sal. 45:1-17 (th Phunzilo 5)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 3) ULALIKI WAMWAYI. (lmd phunzilo 1 mfundo 3)
5. Nkhani
(Mph. 5) ijwbv 26—Mutu: Kodi Salimo 46:10 itanthauzanji? (th phunzilo 18)
6. Kufotokoza Zimene Mumakhulupilila
(Mph. 4) Citsanzo. g 12/10 22-23—Mutu: Kodi Mumauona Bwanji Mcitidwe wa Mathanyula? (lmd phunzilo 6 mfundo 5)
Nyimbo 131
7. Musaleke Kuonetsana Cikondi mu Ukwati Wanu
(Mph. 10.) Kukambilana.
Phwando la ukwati limakhala cocitika cosangalatsa kwambili. (Sal. 45:13-15) Kambili, tsiku la cikwati limakhala losangalatsa kwambili kwa okwatilanawo. Koma kodi n’ciyani cingathandize anthu okwatilana kukhalabe acimwemwe pa umoyo wawo wonse?—Mlal. 9:9.
Kuonetsana cikondi ndiye cinsinsi ca ukwati wacimwewe. Anthu okwatilana ayenela kutengela citsanzo ca Isaki na Rabeka. Baibo imatiuza kuti ngakhale patapita zaka 30 mu ukwati wawo, iwo anali kuonetsanabe cikondi cacikulu. (Gen. 26:8) N’ciyani cingathandize anthu ali pa banja kuonetsana cikondi cotelo?
Tambitsani VIDIYO YAKUTI Kuti Banja Likhale Lacimwemwe: Onetsani Cikondi. Kenako funsani omvela kuti:
Kodi n’ciyani cingapangitse kuti cikondi pakati pa anthu okwatilana ciyambe kucepekela?
Kodi mungatani kuti mnzanu wa mu ukwati azimva kuti mumam’konda na kum’samalila?—Mac. 20:35
8. Zofunikila za Mpingo
(Mph. 5)
9. Phunzilo la Baibo la Mpingo
(Mph. 30) bt mutu. 10 ¶13-21