LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb24 July masa. 10-16
  • August 5-11

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • August 5-11
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2024
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2024
mwb24 July masa. 10-16

AUGUST 5-11

MASALIMO 70-72

Nyimbo 59 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. ‘Uzani M’badwo Wotsatila’ za Mphamvu za Mulungu

(Mph. 10)

Ali mnyamata, Davide anaona thandizo la Yehova (Sal. 71:5; w99-CN 9/1 18 ¶17)

Mu ukalamba wake, Davide anaona thandizo la Yehova (Sal. 71:9; g04-CN 10/8 23 ¶3)

Davide analimbikitsa acinyamata mwa kuwauzako zocitika za pa umoyo wake (Sal. 71:​17, 18; w14 1/15 23 ¶4-5)

Banja limene tinaona mlungu watha m’nkhani yakuti “Mfundo Zothandiza Pocita Kulambila kwa Pabanja.” Laitana banja lacikulile pa kulambila kwawo kwa pabanja ndipo akumvetsela mosangalala pamene banjalo likuwaonetsa zithunzi na kuwafotokozela zocitika mu umoyo wawo.

DZIFUNSENI KUTI, ‘Mu mpingo mwathu, n’ndani amene wakhala akutumikila Yehova kwa zaka zambili amene ningakonde kumufunsa mafunso pa kulambila kwathu kwa pabanja?’

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal. 72:8—Kodi zimene Yehova analonjeza Abulahamu pa Genesis 15:18 zinakwanilitsika bwanji mu ulamulilo wa Mfumu Solomo? (it-1-E 768)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal. 71:​1-24 (th phunzilo 5)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) KUNYUMBA NA NYUMBA. Ngati munthu wayambitsa mkangano, thetsani makambilanowo mwamtendele. (lmd phunzilo 4 mfundo 5)

5. Kubwelelako

(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. Pitilizani kukambilana na wacibale amene akuwayawaya kuyamba kuphunzila Baibo. (lmd phunzilo 8 mfundo 4)

6. Kufotokoza Zimene Mumakhulupilila

(Mph. 5) Nkhani. ijwfq 49—Mutu: N’cifukwa Ciyani a Mboni za Yehova Anasintha Zinthu Zina Zomwe Anali Kukhulupilila? (th phunzilo 17)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 76

7. Zimene Mungacite pa Kulambila kwa Pabanja

(Mph. 15) Kukambilana.

Banja limodzimodzilo laimilila ndipo likuyeseza nyimbo ya Ufumu.
Banjalo likutamba JW Broadcasting.
Mmodzi wa anawo akuyankha mayi ake pamene akuyeseza zocita pa Kulambila kwa Pabanja.

Nthawi ya kulambila kwa pabanja ni nthawi yofunika kuti ana ‘apatsidwe malangizo komanso kuphunzitsidwa mogwilizana ndi zimene Yehova amanena.’ (Aef. 6:4) Kuphunzila kumafuna khama, koma kungakhale kosangalatsa, maka-maka pamene ana akulitsa cikhumbo cawo cofuna kudziŵa coonadi ca m’Baibo. (Yoh. 6:27; 1 Pet. 2:2) Fotokozani mfundo zili m’bokosi lakuti “Zimene Mungacite pa Kulambila kwa Pabanja,” zimene zingathandize makolo kuti kulambila kwawo kwa pabanja kuzikhala kothandiza komanso kokondweletsa. Kenako kambilanani mafunso awa:

  • Pa zimene takambilanazi, kodi mungafune kuyesako ziti?

  • Kodi mwapeza cina cake cothandiza?

ZIMENE MUNGACITE PA KULAMBILA KWA PABANJA

BAIBO:

  • Mvetselani mawu ojambulidwa a kuŵelenga Baibo kwa mlungu na mlungu, kapena muzipatsana mipata yoŵelenga mokweza. Aliyense m’banja angamaŵelenge mawu a munthu wina wake wa m’Baibo

  • Konzani mafunso ocokela pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu na mlungu. Aliyense m’banja asankhepo funso limodzi ndipo akalifufuze. Kenako mungadzakambilane zimene anaphunzila

  • Chulani funso kapena fotokozani cocitika, kenako fufuzani mfundo za m’Baibo zothandiza m’buku lakuti Malemba Othandiza pa Umoyo Wathu wa Cikhristu

  • Citani seŵelo la nkhani ina yake ya m’Baibo

  • Mlungu uliwonse, muzipanga kakhadi kokhala na vesi ya m’Baibo ndipo muziyesetsa kuloŵeza vesilo pamtima. Mungaseŵenzetse mavesi monga opezeka ku zakumapeto A m’bulosha yakuti Kondani Anthu—Kuti Mupange Ophunzila. Bwelezani zimene zili pa makhadi a milungu yapita

  • Ŵelengani mfundo zingapo kapena phunzilo limodzi m’buku la Kondwelani na Moyo Kwamuyaya!

  • Uzani aliyense m’banja lanu kuti akafotokoze nkhani imodzi yopezeka pa mbali yakuti “Kuyankha Mafunso a m’Baibo” kapena “Kufotokoza Mavesi a m’Baibo,” yopezeka pa cigawo cakuti “ZIMENE BAIBO IMAPHUNZITSA” pa jw.org

MISONKHANO:

  • Konzekelani mbali ya msonkhano wa mpingo

  • Konzekelani mayankho na kuwayeseza. Muziyang’ana pa nthawi

  • Yesezani nyimbo za Ufumu

  • Kambilanani na kuyeseza zimene mungakambe polimbikitsa munthu wina msonkhano wotsatila usanayambe komanso ukatha

  • Yesezani nkhani ya m’sukulu pamaso pa a m’banja lanu

ULALIKI:

  • Konzekelani ulaliki wa kunyumba na nyumba

  • Konzekelani maulendo obwelelako

  • Yelekezelani kuti mukucita zinthu zina zake, ndiyeno yesezani mmene mungayambitsile makambilano mwaubwenzi

  • Kambilanani zolinga zimene mungadziikile kuti muwonjezele utumiki wanu pa nyengo ya Cikumbutso kapena panthawi imene simupita ku nchito kapena kusukulu

ZOFUNIKILA ZA M’BANJA:

  • Yesezani zimene mungacite polimbana na cocitika cina cake monga nkhani yokhudza kusakhalila mbali m’zandale, kuvutitsidwa, kukhala pa cibwenzi, kapena kukondwelela maholide

  • Nthawi zina muzisinthanako zocita na ana anu. Ana azifufuza nkhani ina yake kenako azikuuzani inu makolo zimene anapeza

ZINANSO ZIMENE MUNGACITE:

  • Onelelani na kukambilana pulogilamu ya JW Broadcasting®

  • Ŵelengani nkhani kapena tambani vidiyo pa jw.org, ndiyeno kambilanani zimenezo

  • Kambilanani nkhani ina yake yopezeka pa mbali yakuti “Acinyamata” kapena “Ana” pa cigawo cakuti “ZIMENE BAIBO IMAPHUNZITSA” pa jw.org

  • Bwelelamoni m’manotsi anu a pa msonkhano wa cigawo kapena wa dela

  • Yang’anani kapena fufuzani cinthu cina cake m’cilengedwe, ndiyeno kambilanani zimene mwaphunzilapo zokhudza Yehova

  • Nthawi zina muziitanilako munthu wina, na kumufunsa mafunso

  • Dziikileni zolinga zauzimu, na kukambilana zimene mungacite kuti muzikwanilitse

  • Muziseŵenzela pamodzi pogwila nchito ina yake, monga kupanga cingalawa, kuona ma mapu, kapena machati opezeka m’zofalitsa zathu

Tambitsani VIDIYO yakuti Pitilizani Kupangitsa Kulambila kwa Pabanja Kukhala Kopindulitsa. Kenako funsani omvela kuti:

  • Kodi mwamuna angacite ciyani kuti mkazi wake azikondwela na kulambila kwa pabanja ngakhale kuti pa nyumba palibe ana?

8. Phunzilo la Baibo la Mpingo

(Mph. 30) bt mutu 13 ¶17-24

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 123 na Pemphelo

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani