LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb24 November masa. 10-11
  • December 16-22

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • December 16-22
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2024
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2024
mwb24 November masa. 10-11

DECEMBER 16-22

SALIMO 119:​57-120

Nyimbo 129 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Zimene Zingatithandize Kupilila Mavuto

(Mph. 10)

Pitilizani kuŵelenga na kuphunzila mawu a Mulungu (Sal. 119:61; w06-CN 6/15 20 ¶2; w00-CN 12/1 14 ¶3)

Lolani mayeso amene mukukumana nawo kukuyengani (Sal. 119:71; w06-CN 9/1 14 ¶4)

Yang’anani kwa Yehova kuti akuthandizeni (Sal. 119:76; w17.07 13 ¶3, 5)

M’bale wodwala ali khale pa bedi ndipo akupemphela na mkazi wake.

DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi Yehova wanithandiza bwanji kupilila mavuto amene nikukumana nawo?’

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal. 119:96—Kodi vesili liyenela kuti litanthauza ciyani? (w06-CN 9/1 14 ¶5)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal. 119:​57-80 (th phunzilo 12)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) KUNYUMBA NA NYUMBA. Onetsani mwininyumba webusaiti yathu, na kum’patsa kakhadi kolowela pa jw.org. (lmd phunzilo 2 mfundo 5)

5. Kubwelelako

(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. Muitanileni ku nkhani ya onse yotsatila. Seŵenzetsani vidiyo yakuti N’ciyani Cimacitika ku Nyumba ya Ufumu? (lmd phunzilo 8 mfundo 3)

6. Kufotokoza Zimene Mumakhulupilila

(Mph. 5) Citsanzo. ijwbq 157—Mutu: Kodi Baibulo Limanena Chiyani pa Nkhani ya Ngozi Zadzidzidzi? (lmd phunzilo 3 mfundo 3)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 128

7. Yehova Amatithandiza Kupilila

(Mph. 15) Kukambilana.

Kupilila kumatanthauza kupitiliza kuyang’anizana na zovuta popanda kufooka. Kumaphatikizaponso kukhala wolimba komanso kusataya mtima podziŵa kuti mavutowo ni akanthawi cabe. Ngati ndife opilila, sitidzabwelela m’mbuyo kapena kucepetsa liŵilo pa utumiki wathu wa Cikhristu tikakumana na zovuta. (Aheb. 10:​36-39) Yehova ni wofunitsitsa kutithandiza kuti tipilile mavuto.—Aheb. 13:6.

Pansi pa lemba lililonse, lembam’poni mmene Yehova amatithandizila kupilila.

  • Luka 11:13

  • Aroma 8:25

  • 1 Ates. 5:11

  • Yak. 1:5

Zithunzi za m’vidiyo yakuti “Muzipemphelela Anthu Amene Akupilila Mavuto.” 1. Banja la M’bale Wilson likuphunzila nkhani yakuti “Khala Bwenzi la Yehova​—Uzipemphelela Ena.” 2. Glynis akupemphela.

Tambitsani VIDIYO yakuti Muzipemphelela Anthu Amene Akupilila Mavuto. Kenako funsani omvela mafunso awa:

  • Kodi tingaiseŵenzetse bwanji jw.org kuti tidziŵe za abale athu amene akukumana na mavuto?

  • Kodi makolo angawaphunzitse bwanji ana awo kuti azipemphelelako anthu ena? Nanga pamakhala mapindu otani?

  • N’cifukwa ciyani n’kofunika kupempha Yehova kuti athandize Akhristu anzathu kupilila?

  • Kodi kupemphelela ena kungatithandize bwanji kupilila mavuto?

8. Phunzilo la Baibo la Mpingo

(Mph. 30) bt mutu 19 ¶14-20, bokosi pa tsa. 152

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 32 na Pemphelo

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani