MARCH 17-23
MIYAMBO 5
Nyimbo 122 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. Thawani Ciwelewele
(Mph. 10)
Tingakopedwe kuti ticite ciwelewele (Miy. 5:3; w00-CN 7/15 29 ¶1)
Kucita ciwelewele kumakhala ndi zotulukapo zowawa (Miy. 5:4, 5; w00-CN 7/15 29 ¶2)
Muzipewelatu zinthu zomwe zingakugwetseleni m’chimo la ciwelewele (Miy. 5:8; w00-CN 7/15 29 ¶5)
Mlongo wacitsikana akukana kupatsa mnyamata nambala yake ya foni
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
Miy. 5:9—Kodi munthu amene wacita ciwelewele amadzicotsela bwanji “ulemu wake kwa anthu ena”? (w00-CN 7/15 29 ¶7)
Pa kuwelenga Baibulo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuwelenga Baibulo
(Mph. 4) Miy. 5:1-23 (th phunzilo 5)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 3) ULALIKI WAPOYELA. Itanilani ku Cikumbutso munthu amene si wacipembedzo ca Cikhristu, ndipo gwilitsani nchito jw.org kuti mupeze malo a Cikumbutso kufupi ndi kwawo. (lmd phunzilo 6 mfundo 4)
5. Kubwelelako
(Mph. 4) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Pa ulendo wapita, munthuyo analandila kapepala komuitanila ku Cikumbutso ndipo anaonetsa cidwi. (lmd phunzilo 9 mfundo 5)
6. Kupanga Ophunzila
(Mph. 5) lff phunzilo 16 cidule cake, mafunso obweleza, ndi colinga. Wophunzila akakufunsani mmene Yesu anali kuonekela, muonetseni mmene angafufuzile yankho. (lmd phunzilo 11 mfundo 4)
Nyimbo 121
7. Zimene Mungacite Kuti Mukhalebe Woyela Mukakhala Pacibwenzi
(Mph. 15) Kukambilana.
Mwacidule tinganene kuti “kukhala pa cibwenzi kumaphatikizapo kuceza mwa njila ina iliyonse pakati pa anthu awili amene akopeka wina ndi mnzake.” Anthu ambili amacita zimenezi moonetsela, ena mwacinsinsi, pafoni kapena polembelana mameseji. Timaona kuti kukhala pacibwenzi si nkhani ya masewela, koma kuti ndi njila imene imathandiza mwamuna ndi mkazi kudziwana bwino asanakwatilane. Kodi acinyamata kapena acikulile angacite ciyani kuti apewe ciwelewele pamene ali pacibwenzi?—Miy. 22:3.
Tambitsani VIDIYO YAKUTI Kukonzekela Kulowa m’Banja—Mbali 1: Kodi Ndafika Poti N’kukhala ndi Cibwenzi?—Mbali Yake. Kenako funsani omvela kuti:
N’cifukwa ciyani munthu sayenela kukhala pacibwenzi mpaka atafika poti ndi woyenelela kulowa m’banja? (Miy. 13:12; Luka 14:28-30)
Kodi n’ciyani cimene mwakonda poona mmene makolo a mu vidiyo iyi anathandizila mwana wawo?
Welengani Miyambo 28:26. Kenako funsani omvela kuti:
Kodi anthu amene ali pacibwenzi angacite ciyani kuti apewe kukhala awiliwili ku malo kwaokha, zimene zingapangitse kuti acite ciwelewele?
N’cifukwa ciyani n’canzelu kuti anthu amene ali pacibwenzi akambilane pasadakhale zinthu zimene ayenela kucita ndi zimene sayenela kucita poonetsana cikondi, monga kugwilana manja ndi kupsompsonana?
Welengani Aefeso 5:3, 4. Kenako funsani omvela kuti:
Kodi mwamuna ndi mkazi amene ali pacibwenzi ayenela kusamala za ciyani akamakambitsana pafoni kapena pa soshomidiya?
8. Phunzilo la Baibulo la Mpingo
(Mph. 30) bt mutu 24 ¶1-6