LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb25 March tsa. 7
  • March 31–April 6

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • March 31–April 6
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2025
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2025
mwb25 March tsa. 7

MARCH 31–APRIL 6

MIYAMBO 7

Nyimbo 34 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Mzimayi wa m’nthawi yakale yemwe ndi hule, waimilila pakhomo la nyumba yake pamene mnyamata akudutsa.

1. Pewani Zinthu Zimene Zingakugwetseleni M’mayeselo

(Mph. 10)

Mnyamata wosadziwa zinthu wasankha kupita ku malo kumene kumadziwika kuti kumapezeka anthu aciwelewele (Miy. 7:​7-9; w00-CN 11/15 29 ¶5)

Mkazi amene ndi hule akumunyengelela kuti agone naye (Miy. 7:​10, 13-21; w00-CN 11/15 30 ¶4-6)

Akukumana ndi mavuto cifukwa codzigwetsela m’mayeselo (Miy. 7:​22, 23; w00-CN 11/15 31 ¶2)

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Miy. 7:3​—Kodi kumanga malamulo a Mulungu ku zala zathu ndi kuwalemba pa mtima pathu kutanthauza ciyani?(w00-CN 11/15 29 ¶1)

  • Pa kuwelenga Baibulo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?

3. Kuwelenga Baibulo

(Mph. 4) Miy. 7:​6-20 (th phunzilo 2)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kubwelelako

(Mph. 4) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Pa ulendo wapita, munthuyo analandila kapepala komuitanila ku Cikumbutso ndipo anaonetsa cidwi. (lmd phunzilo 9 mfundo 5)

5. Kubwelelako

(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. Pa makambilano apita, munthuyo analandila kapepala komuitanila ku Cikumbutso ndipo anaonetsa cidwi. (lmd phunzilo 9 mfundo 4)

6. Kubwelelako

(Mph. 4) ULALIKI WAPOYELA. Pa makambilano apita, munthuyo analandila kapepala komuitanila ku Cikumbutso ndipo anaonetsa cidwi. (lmd phunzilo 9 mfundo 3)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 13

7. Nthawi Ina Yabwino (Luka 4:6)

(Mph. 15) Kukambilana.

Tambitsani VIDIYO Kenako funsani omvela kuti:

  • Kodi Yesu anayesedwa motani? Nanga ifeyo tingayesedwe bwanji m’njila yofananayo?

  • Kodi tingatani kuti tisagonje ku mayeselo a Mdyelekezi?

8. Phunzilo la Baibulo la Mpingo

(Mph. 30) bt mutu 24 ¶13-21

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 70 ndi Pemphelo

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani