MAY 19-25
MIYAMBO 14
Nyimbo 89 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. Muzicita Zinthu Mosamala Panthawi ya Tsoka
(Mph. 10)
Musamakhulupilile “mawu alionse” amene mwamva (Miy. 14:15; w23.02 22-23 ¶10-12)
Musamangodalila maganizo anu kapena zimene zinakucitikilam’poni kale (Miy. 14:12)
Musamamvele anthu amene amakana malangizo a gulu la Yehova (Miy. 14:7)
ZOFUNIKA KUZISINKHASINKHA: Inu akulu, kodi ndinu okonzeka kutsatila malangizo komanso kudalila Yehova pa nthawi ya tsoka?—w24.07 5 ¶11.
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
Miy 14:17—Kodi “munthu amene amaganiza bwino” angadedwe m’njila ziti? (w05-CN 7/15 19 5-6)
Pa kuwelenga Baibulo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuwelenga Baibulo
(Mph. 4) Miy. 14:1-21 (th phunzilo 11)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 3) ULALIKI WA POYELA. Kambilanani mfundo ya m’Baibulo ndi munthu amene wakuuzani kuti ali ndi nkhawa cifukwa ca mavuto azacuma. (lmd phunzilo 3 mfundo 3)
5. Kubwelelako
(Mph. 4) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Gawilani magazini yokhala ndi nkhani imene munthu anacita nayo cidwi pa makambilano apita. (lmd phunzilo 9 mfundo 4)
6. Kupanga Ophunzila
(Mph. 5) Limbikitsani wophunzila wanu kuti aziwelenga Baibulo tsiku lililonse, ndipo muonetseni mmene angacitile zimenezo. (th phunzilo 19)
Nyimbo 126
7. Khalanibe Okonzeka Kukumana Ndi Masoka
(Mph. 15) Kukambilana.
Ikambidwe ndi mkulu. Fotokozani zikumbutso zocokela ku ofesi ya nthambi komanso ku bungwe la akulu ngati zilipo.
Popeza tikukhala ‘m’masiku otsiliza,’ tikuyembekezela kuti mavuto aziwonjezeka. (2 Tim. 3:1) Nthawi zambili tsoka lisanacitike kapena likacitika, anthu a Yehova amalandila malangizo a panthawi yake komanso owathandiza kuti apulumuke. Kuti tikapulumuke pa nthawiyo, tiyenela kukhala omvela pali pano mwa kukhala okonzekela kuuzimu komanso kuthupi.—Miy. 14:6, 8.
Konzekelani Mwauzimu: Khalani ndi pulogilamu yabwino yocita zinthu zauzimu. Nolani maluso anu mwa kuphunzila njila zosiyanasiyana zocitila ulaliki. Musade nkhawa kwambili kapena kucita mantha ngati kwa kanthawi simutha kukumana ndi anthu a mumpingo wanu pa nthawi ya tsoka. (Miy. 14:30) Yehova Mulungu komanso Yesu Khristu sadzakusiyani ngakhale pang’ono.—od 176 ¶15-17
Konzekelani Kuthupi: Kuonjezela pa kukhala ndi kacola ka zofunikila, banja lililonse liyenela kusungako cakudya, madzi, mankhwala komanso zinthu zina zofunikila, kucitila kuti mwina angafunike kusacoka pa nyumba kwa nthawi ndithu. —Miy. 22:3; g17.5-CN 4
Tambitsani VIDIYO yakuti Kodi Mwaikonzekela Nthawi ya Tsoka? Kenako funsani omvela kuti:
Kodi Yehova angatithandize bwanji pa nthawi ya tsoka?
Kodi tingacite ciyani palipano kuti tikhale okonzeka?
Kodi tingawathandize bwanji anthu amene akumana ndi masoka?
8. Phunzilo la Baibo la Mpingo
(Mph. 30) bt mutu 26 ¶18-22, bokosi pa tsa. 209