MAY 26–JUNE 1
MIYAMBO 15
Nyimbo 102 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. Thandizani Ena Kukhala Acimwemwe
(Mph. 10)
Abale athu akamakumana ndi mavuto aakulu, angamaone monga masiku onse a moyo wawo ndi oipa (Miy. 15:15)
Muzikhala oceleza kwa anthu amene akukumana ndi mavuto (Miy. 15:17; w10-CN 11/15 31 ¶16)
“Kuyang’ana munthu ndi nkhope yacimwemwe” komanso kumuuza mawu ocepa olimbikitsa kungakhale kothandiza kwambili (Miy. 15:23, 30, mawu a m’munsi; w18.04 23-24 ¶16-18)
DZIFUNSENI KUTI: ‘Kodi ndi ndani mumpingo mwathu amene ndingamulimbikitse? Nanga ndingamuthandize bwanji?’
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
Miy. 15:22—Kodi mfundo ya palembali ingatithandize bwanji kupanga zisankho zabwino pa nkhani ya cithandizo ca mankhwala? (ijwbq-CN nkhani 39 ¶3)
Pa kuwelenga Baibulo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuwelenga Baibulo
(Mph. 4) Miy. 15:1-21 (th phunzilo 2)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 3) KUNYUMBA NDI NYUMBA. (lmd phunzilo 1 mfundo 5)
5. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. M’pempheni kuti muziphunzila naye Baibulo. (lmd phunzilo 2 mfundo 4)
6. Kupanga Ophunzila
(Mph. 5) Limbikitsani wophunzila Baibulo amene akutsutsidwa ndi a m’banja lake. (th phunzilo 4)
Nyimbo 155
7. Tingakhalebe Acimwemwe Ngakhale Pamene Tikukumana ndi Mavuto
(Mph. 15) Kukambilana.
Tambitsani VIDIYO yakuti Tingakhalebe Okondwela Ngakhale pa Zowawa, Njala, Komanso pa Usiwa. Kenako, funsani omvela kuti:
Kodi mwaphunzilapo ciyani pa zocitika za mu vidiyo iyi?
8. Phunzilo la Baibulo la Mpingo
(Mph. 30) bt mutu 27 ¶1-9