JUNE 9-15
MIYAMBO 17
Nyimbo 157 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba(Mph. 10)
Mwamuna ndi mkazi wake mu Isiraeli akudyela cakudya pamodzi ndipo akukhala mwamtendele
1. Khalani Mwamtendele mu Ukwati Wanu
(Mph. 10)
Kukhala mwamtendele kumafuna khama, koma mukatelo ukwati wanu udzakhala wacimwemwe (Miy. 17:1; onani cithunzi pacikuto)
Pewani kukangana pa nkhani zing’onozing’ono (Miy. 17:9; g-CN 9/14 11 ¶2)
Musalole kuti mkwiyo uzikulamulilani (Miy. 17:14; w08-CN 5/1 10 ¶6–11 ¶1)
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
Miy. 17:24—Kodi “maso a munthu wopusa amangoyendayenda mpaka kumalekezelo a dziko lapansi” m’lingalilo lotani? (it-1-E 790 ¶2)
Pa kuwelenga Baibulo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuwelenga Baibulo
(Mph. 4) Miy. 17:1-17 (th phunzilo 10)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 3) ULALIKI WAMWAYI. (lmd phunzilo 3 mfundo 5)
5. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 4) ULALIKI WAPOYELA. M’pempheni kuti muziphunzila naye Baibulo. (lmd phunzilo 6 mfundo 4)
6. Nkhani
(Mph. 5) ijwbv nkhani 60—Mutu: Kodi Miyambo 17:17 itanthauza ciyani? (th phunzilo 13)
Nyimbo 113
7. Kulitsani Makhalidwe Othandiza Kuti Muzikambilana Bwino
(Mph. 15) Kukambilana.
Kukambilana bwino n’kofunika kuti banja likhale lacimwemwe. Ngati anthu m’banja amakambilana momasuka angathandizane kukwanilitsa zolinga zawo, komanso angamathandizane panthawi ya mavuto (Miy. 15:22) Kodi mungacite ciyani kuti muthandize aliyense m’banja lanu kukhala womasuka kuti afotokoze maganizo ake komanso mmene akumvela?
Muzicitila zinthu pamodzi. (Deut. 6:6, 7) Mabanja akamagwilila nchito pamodzi, kucitila zauzimu pamodzi, komanso kucita zosangalatsa pamodzi, cikondi cawo cimakula komanso amakhulupililana kwambili. Kucita izi kumawapatsanso mipata yokambilana momasuka. Nthawi zina, mungafunike kucita zinthu zimene a m’banja lanu akufuna m’malo mocita zimene inu mufuna. Koma kucita izi kumakhala ndi zotulukapo zabwino kwambili! (Afil. 2:3, 4) Kodi mungacite ciyani kuti muzigwilitsa nchito bwino nthawi imene mumacitila zinthu limodzi ndi a m’banja lanu?—Aef. 5:15, 16.
Tambitsani VIDIYO yakuti Zofunikila Kuti M’banja Mukhale Mtendele—Kukambilana Momasuka. Kenako funsani omvela kuti:
Kodi kugwilitsa nchito zipangizo zamakono molakwika kungalepheletse bwanji anthu m’banja kulankhulana momasuka?
Kodi mwaphunzila ciyani mu vidiyo iyi pa nkhani ya kulankhulana bwino?
Muziwamvetsela. (Yak. 1:19) Nthawi zambili ana amakhala omasuka kufotokoza maganizo awo ngati akudziwa kuti makolo awo adzawamvetsela ndipo sadzakwiya. Conco, muziyesetsa kukhala wodekha ngati mwana wanu wakamba cina cake cimene cakudetsani nkhawa. (Miy. 17:27) Muzimumvetsela mokoma mtima. Yesani kumvetsela maganizo ake komanso mmene akumvela kuti mumuthandize komanso kumulimbikitsa mwacikondi.
8. Phunzilo la Baibulo la Mpingo
(Mph. 30) bt mutu 27 ¶19-22, bokosi patsamba 212