JUNE 16-22
MIYAMBO 18
Nyimbo 90 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. Muzilankhula Mawu Olimbikitsa kwa Amene Akudwala
(Mph. 10)
Muzilola nzelu za Mulungu kukuthandizani kudziwa zoyenela kukamba (Miy. 18:4; w22.10 22 ¶17)
Muziyesa kumvetsa zimene munthuyo akukumana nazo (Miy. 18:13; mrt-CN nkhani 19 bokosi)
Khalani bwenzi lothandiza komanso loleza mtima (Miy. 18:24; wp23.1 14 ¶3–15 ¶1)
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ndingatani kuti ndithandize mnzanga wa mu ukwati ngati akudwala kapena ali ndi matenda a maganizo?’
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
Miy. 18:18—N’cifukwa ciyani m’nthawi za m’Baibulo anthu anali kugwilitsa nchito maele? (it-2-E 271-272)
Pa kuwelenga Baibulo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuwelenga Baibulo
(Mph. 4) Miy. 18:1-17 (th phunzilo 11)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 1) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Munthuyo akulankhula cinenelo cina. (lmd phunzilo 2 mfundo 5)
5. Kubwelelako
(Mph. 3) ULALIKI WAPOYELA. Munthuyo wakuuzani kuti mukambe mwacidule. (lmd phunzilo 7 mfundo 4)
6. Kubwelelako
(Mph. 3) ULALIKI WAMWAYI. Phunzitsani munthuyo mfundo yofunika ya coonadi cokhudza Ufumu wa Mulungu (lmd phunzilo 9 mfundo 5)
7. Kufotokoza Zimene Mumakhulupilila
(Mph. 4) Citsanzo. Ijwfq-CN nkhani 29—Mutu: Kodi Mumakhulupilila Kuti Dziko Linalengedwa m’Masiku 6 Enieni? (lmd phunzilo 5 mfundo 5)
Nyimbo 144
8. Thandizani Okondedwa Anu Kuyandikila Yehova Popanda Mawu
(Mph. 15) Kukambilana.
Ambili a ife tidziwako munthu wina wake amene pali pano sakutumikila Yehova. Munthuyo angakhale mnzathu wa mu ukwati, mwana wathu, kapena mnzathu wapamtima amene anasiya kutumikila Yehova. Kodi munakakamizapo munthu, ngakhale kufika pomukalipila, kuti ayambe kutumikila Yehova? Ngakhale kuti zolinga zathu n’zabwino, mawu athu angapangitse kuti zinthu ziipileipile. (Miy. 12:18) Kodi njila yabwino yothandizila anthu otelo ndi iti?
1 Petulo 3:1 imakamba kuti mwamuna wosakhulupilila angakopeke popanda mawu. Ngakhale kuti mwamuna wa mlongo angakane kukambilana naye coonadi ca m’Baibulo, mlongoyo angapitilize kumuthandiza kudziwa Yehova. Makhalidwe ake abwino omwe amaphatikizapo cikondi, kukoma mtima, komanso nzelu, angafewetse mtima wa mwamuna wake. (Miy. 16:23) Khalidwe lathu labwino komanso kukoma mtima kwathu zingacititse kuti okondedwa athu amene satumikila Yehova pali pano akopeke.
Tambitsani VIDIYO yakuti Omenya Nkhondo ya Cikhulupililo Mwacipambano—Aja Amene Mnzawo wa m’Cikwati si Mboni. Kenako funsani omvela kuti:
Kodi mwaphunzila ciyani kwa mlongo Sasaki?
Kodi mwaphunzila ciyani kwa mlongo Ito?
Kodi mwaphunzila ciyani kwa mlongo Okada?
9. Phunzilo la Baibulo la Mpingo
(Mph. 30) bt mutu 27 ¶23-26, mabokosi pa masamba 214, 217