Malifalensi a Kabuku ka Umoyo ndi Utumiki
© 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
JULY 7-13
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 21
Malangizo Anzelu Othandiza Kuti Ukwati Ukhale Wacimwemwe
w03-CN 10/15 4 ¶5
Kodi Mungatani Kuti Muzisankha Zochita Mwanzeru?
Sitingasankhe zochita mwanzeru ngati tisankha mopupuluma. Miyambo 21:5 imachenjeza kuti: “Zoganizira za wakhama zichulukitsadi katundu; koma yense wansontho angopeza umphaŵi.” Mwachitsanzo, achinyamata amene ali m’chikondi chongotengeka maganizo sayenera kupupuluma kumanga banja. Apo phuluzi, adzaona zimene William Congreve, wolemba maseŵero achingelezi m’zaka za m’ma 1700 ananena, kuti: “Ukafulumira kuloŵa m’banja, umadzanong’oneza bondo pambuyo pake.”
g-CN 7/08 7 ¶2
Zimene Mungachite Kuti Banja Lanu Liziyenda Bwino
Dzichepetseni. “Musachite kanthu kalikonse ndi mzimu wandewu kapena wodzikuza, koma modzichepetsa, mukumaona ena kukhala okuposani.” (Afilipi 2:3) Kawirikawiri, mikangano m’banja imayamba chifukwa chakuti pakabuka vuto, kudzikuza kumachititsa kuti wina aziimba mlandu mnzake m’malo modzichepetsa n’kupeza njira zothetsera vutolo mokomera aliyense. Koma kudzichepetsa kungakuthandizeni kuchotsa maganizo odziona kuti olakwa siinu.
w06-CN 9/15 28 ¶13
‘Ukondwere ndi Mkazi Wokula Naye’
13 Kodi zingakhale bwanji ngati banja likukumana ndi mavuto chifukwa cha zimene mwamuna ndi mkazi amachitirana? Zikatero, m’pofunika khama kuti apeze njira yothetsera mavutowo. Mwachitsanzo, n’kutheka kuti m’banja mwawomo munalowa mzimu wosalankhulana bwino ndipo tsopano kulankhulana kotero kwakhala chizolowezi chawo. (Miyambo 12:18) Monga momwe taonera m’nkhani yapitayi, zimenezi zingathe kusokoneza kwambiri banja. Mwambi wina m’Baibulo umati: “Kukhala m’chipululu kufunika kuposa kukhala ndi mkazi wolongolola ndi wong’ung’udza.” (Miyambo 21:19) Ngati ndinu mkazi m’banja loterolo, dzifunseni kuti, ‘Kodi khalidwe langa limapangitsa mwamuna wanga kuvutika kucheza nane?’ Baibulo limauza amuna kuti: “Kondani akazi anu, ndipo musawawire mtima iwo.” (Akolose 3:19) Ngati ndinu mwamuna, dzifunseni kuti, ‘Kodi sindisonyeza chikondi, moti mpaka mkazi wanga amaganiza zofuna kulimbikitsidwa ndi anthu ena?’ N’zoona kuti palibe chifukwa chomveka chochitira chiwerewere. Komabe, popeza kuti n’zotheka kuti zimenezi zichitike, ndi bwino kuti mabanja azikambirana mosapita m’mbali za mavuto awo.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w05-CN 1/15 17 ¶9
Masomphenya a Ufumu wa Mulungu Asanduka Zenizeni
9 Yesu tsopano si munthu wamba wokwera pa mwana wa bulu, koma ndi Mfumu yamphamvu. Baibulo limafotokoza kuti wakwera pa kavalo, chomwe m’Baibulo chili chizindikiro cha nkhondo. (Miyambo 21:31) “Taonani, kavalo woyera,” likutero lemba la Chivumbulutso 6:2, “ndipo wom’kwerayo anali nawo uta; ndipo anam’patsa korona; ndipo anatulukira wolakika kuti alakike.” Komanso ponena za Yesu, wamasalmo Davide analemba kuti: “Yehova adzatumiza ndodo ya mphamvu yanu kuchokera ku Ziyoni; Chitani ufumu pakati pa adani anu.”—Salmo 110:2.
JULY 14-20
CUMA COPEZA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 22
Malangizo Anzelu Othandiza Polela Ana
Kodi Ana Anu Adzatumikilabe Yehova Akakula?
7 Ngati ndimwe okwatilana, ndipo mufuna kukhala ndi ana, dzifunseni kuti: ‘Kodi ndife odzicepetsa, komanso okonda zinthu zauzimu cakuti Yehova angatisankhe kusamalila mwana wakhanda?’ (Sal. 127:3, 4) Ngati ndimwe kholo, dzifunseni kuti: ‘Kodi nimaphunzitsa ana anga za kufunika kolimbikila nchito?’ (Mlal. 3:12, 13) ‘Kodi nimayesetsa kuteteza ana anga ku zinthu zoipa za m’dziko la Satanali?’ (Miy. 22:3) Simungathe kuchingiliza ana anu ku mavuto onse amene iwo angakumane nawo. N’zosatheka zimenezo. Koma mungawakonzekeletse mmene angacitile nawo mavuto pa umoyo, mwa kupitilizabe kuwaphunzitsa mwacikondi kudalila Mawu a Mulungu. (Ŵelengani Miyambo 2:1-6) Mwacitsanzo, ngati wacibululu wanu waleka kutumikila Yehova, thandizani ana anu kucokela m’Mawu a Mulungu, kuona kufunika kokhalabe okhulupilika kwa Yehova. (Sal. 31:23) Kapena ngati munthu amene mumam’konda wamwalila, onetsani ana anu mmene angaseŵenzetsele Mawu a Mulungu kuti apeze citonthozo na mtendele wa maganizo.—2 Akor. 1:3, 4; 2 Tim. 3:16.
Makolo—Phunzitsani Ana Anu Kukonda Yehova
17 Muziyamba kuphunzitsa ana akali aang’ono. Ana amakula bwino ngati makolo ayamba kuwaphunzitsa akali aang’ono. (Miy. 22:6) Ganizilani citsanzo ca Timoteyo, amene m’kupita kwa nthawi anayamba kuyenda na mtumwi Paulo. Amayi ake, a Yunike, na ambuye ake aakazi a Loisi anamuphunzitsa malemba oyela ‘kuyambila pamene anali wakhanda.’—2 Tim. 1:5; 3:15.
18 M’bale Jean-Claude na mkazi wake Peace, amene amakhala ku Côte d’Ivoire, anakwanitsa kuphunzitsa ana awo onse 6 kukonda Yehova na kuyamba kum’tumikila. Kodi n’ciani cinawathandiza? Anatengela citsanzo ca Yunike na Loisi. Iwo anati, “Tinali kuyesetsa kukhomeleza Mawu a Mulungu mwa ana athu kuyambila ali akhanda, akangobadwa.”—Deut. 6:6, 7.
19 Kodi ‘kukhomeleza’ Mawu a Yehova mwa ana kutanthauza ciani? ‘Kukhomeleza’ kutanthauza “kuphunzitsa na kugogomeza zinthu mobweleza-bweleza.” Kuti makolo acite izi, amafunika kupatula nthawi yoceza ndi ana awo kaŵili-ŵili. Amafunikanso kupeleka malangizo mobweleza-bweleza kwa anawo, ndipo nthawi zina izi zingakhale zolefula. Koma makolo afunika kuona kuti umenewu ni mwayi wawo wothandiza anawo kumvetsetsa Mawu a Mulungu na kuwaseŵenzetsa.
w06-CN 4/1 9 ¶4
Makolo—Khalani Chitsanzo Chabwino kwa Ana Anu
Inde, ana ndi ana basi, ndipo ena n’ngosamva ndipo mwinanso amatha kulowerera. (Genesis 8:21) Kodi makolo angatani? Baibulo limati: “Utsiru umangidwa mumtima mwa mwana; koma ntyole yom’langira idzauingitsira kutali.” (Miyambo 22:15) Anthu ena amaona kuti kulanga mwana m’njira imeneyi ndi nkhanza ndipo kuti n’kwachikale. N’zoona kuti Baibulo limadana ndi zachiwawa ndiponso kuzunza munthu m’njira ina iliyonse. Komano nthawi zina mawu akuti “ntyole” amatanthauza udindo umene makolo ali nawo womwe amaugwiritsa ntchito mosalekerera koma mwachikondi komanso moyenerera pofuna kuti ana awo adzakhale ndi moyo wosatha.—Ahebri 12:7-11.
Kufufuza Cuma Cauzimu
Muzikondwela na Mwayi Wanu wa Utumiki
11 Mofananamo, tingawonjezele cimwemwe cathu ngati tiikilapo mtima pa nchito iliyonse imene tingapatsidwe m’gulu la Yehova. Muzikhala ‘otanganidwa kwambili’ na nchito yolalikila, komanso kutengako mbali mokwanila pa zocitika za pa mpingo. (Mac. 18:5; Aheb. 10:24, 25) Muzikonzekelanso bwino misonkhano kuti mukapelekepo ndemanga zolimbikitsa. Musamaione mopepuka mbali ya wophunzila imene angakupatseni pa misonkhano ya mkati mwa mlungu. Akakupemphani kugwila nchito inayake mu mpingo, osazengeleza ndipo khalani wodalilika. Musamatenge mopepuka nchito iliyonse imene mungapatsidwe, moti n’kungoicita mwa mwambo cabe. Muziyesetsa kukulitsa maluso anu. (Miy. 22:29) Mukamaikilapo mtima pa zinthu zauzimu komanso pa nchito zina, mudzapita patsogolo mofulumila, ndipo mudzakhala na cimwemwe cowilikiza. (Agal. 6:4) Cina, cidzakhala copepuka kukondwela na ena amene alandila utumiki umene inu munali kuufuna.—Aroma 12:15; Agal. 5:26.
JULY 21-27
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 23
Malangizo Anzelu pa Nkhani ya Mowa
w04-CN 12/1 19 ¶5-6
Mowa Umafunika Kusamala Nawo
5 Bwanji ngati munthu amamwa mowa koma mosamala moti ena sangam’zindikire kuti waledzera? Anthu ena sadziwika kwenikweni kuti aledzera ngakhale atamwa mowa wambiri. Koma, kuganizira kuti palibe vuto lililonse ngati achita zimenezi, n’kudzinyenga chabe. (Yeremiya 17:9) M’kupita kwanthawi ndiponso pang’ono ndi pang’ono, munthu akhoza kufika mpaka pomadwala akapanda kumwa mowa ndiponso angathe ‘kukodwa nacho chikondi cha pavinyo.’ (Tito 2:3) Ponenapo za mmene munthu amakhalira chidakwa, mayi wina wolemba mabuku, dzina lake Caroline Knapp, anati: “Chizolowezichi chimayamba pang’onopang’ono, mosadziwika bwinobwino ndiponso moti munthu sangathe kufotokoza.” Kumwa kwambiri ndi msampha woopsadi kwambiri.
6 Komanso, taganizirani chenjezo la Yesu lakuti: “Koma mudziyang’anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha; pakuti lidzatero ndi kufikira anthu onse akukhala pankhope padziko lonse lapansi.” (Luka 21:34, 35) Munthu amaodzera ndiponso kufooka ndi mowa asanafike poledzera nawo, ndipo izi zingasokonezenso moyo wake wauzimu. Kodi zingakhale bwanji tsiku la Yehova litam’peza ali choncho?
w10-CN 1/1 4 ¶7-5 ¶3
Maganizo a Mulungu Pankhani ya Kumwa Mowa
Kungachititse kuti munthu asamadziletse. Baibulo limatichenjeza kuti: “Vinyo ndi chimera zichotsa nzeru.” (Hoseya 4:11, Malembo Oyera) N’chifukwa chiyani zili choncho? N’chifukwa chakuti munthu akamwa mowa, zinthu zoipa amayamba kuziona ngati zabwino. Kumwa mowa mwauchidakwa kungachititse kuti munthu azilephera kuchita zinthu zabwino. Mowa ungasokoneze khalidwe lathu labwino ndipo zimenezi zingawononge moyo wathu wauzimu.
Mwachitsanzo, John atakangana ndi mkazi wake, anatuluka m’nyumba atakwiya n’kupita komwa mowa. Atamwa mabotolo angapo kuti mtima ukhale pansi, mkazi wina anafika pamene iye anali. Atamwanso mabotolo ena angapo, John anatengana ndi mkaziyo kukachita chiwerewere. Kenako John anadandaula kwambiri kuti anachita chinthu chimene sakanachita n’komwe akanakhala kuti sanaledzere.
Kungachititsenso kuti munthu azilankhula ndiponso kuchita zinthu motayirira. Baibulo limafunsa kuti: “Ndani amakhala m’mavuto nthawi zonse? Ndani amakonda kukangana komanso kumenyana?” Kenako limayankha kuti: “Ndi amene amachezera kumwa mowa n’kumanena kuti, ‘Ndingomwako botolo limodzi lokha.’” (Miyambo 23:29, 30, Contemporary English Version) Kumwa mowa mwauchidakwa kungachititse munthu ‘kufanana ndi munthu wogona pakati panyanja, komanso munthu wogona tulo pamwamba pa mzati wa bwato.’ (Miyambo 23:34, Malembo Oyera) Munthu amene waledzera kwambiri angadzuke “atasupukasupuka, koma osakumbukira kuti chinachitika n’chiyani.”—Miyambo 23:35, CEV.
Kungachititse kuti munthu adwale kwambiri. Baibulo limati: ‘Pa chitsiriziro chake mowa umaluma ngati njoka, nujompha ngati mamba.’ (Miyambo 23:32) Madokotala amavomereza kuti mawu amenewa ndi oona. Kumwa mowa kwambiri n’koopsa chifukwa kungachititse kuti munthu adwale matenda osiyanasiyana monga khansa, kutupa kwa chiwindi, kutupa kwa kapamba, matenda a shuga ndiponso kungachititse kuti mayi adzabereke mwana wozerezeka. Kumwa mowa kwambiri kungachititsenso matenda ofa ziwalo kapena amtima. Ndipo kumwa kwambiri mowa, ngakhale kamodzi kokha, kungachititse kuti munthu akomoke kapena kufa kumene. Komabe, pali chifukwa chachikulu chimene chimapangitsa kumwa mowa mwauchidakwa kukhala koopsa. Chifukwa chimenechi sichikukhudzana ndi matenda amene amayamba chifukwa chomwa mowa mwauchidakwa.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w04-CN 11/1 31 ¶2
Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Mwachitsanzo, kunenepa mopyola muyeso kungathe kukhala chizindikiro cha kususuka, koma sikuti ndi mmene zimakhalira nthaŵi zonse. Munthu angathe kunenepa kwambiri chifukwa cha matenda. Mwinanso zingakhale zotengera kwa makolo. Tiyeneranso kukumbukira kuti tikamanena kuti munthu ndi wonenepa mopyola muyeso timakhala tikunena za thupi lake, pamene tikanena za kususuka timakhala tikunena za maganizo ake. Kunenepa mopyola muyeso amati ndi “kuchuluka mafuta m’thupi,” pamene kususuka ndi “umbombo kapena kudya mosadziletsa.” Motero, kukula kwa thupi la munthu sichizindikiro cha kususuka. Chizindikiro chake ndi mmene munthuyo amaonera chakudya. Munthu angathe kukhala wathupi labwinobwino kapena wochepa thupi koma ali wosusuka. Komanso, mmene anthu a m’dera lina amaonera nkhani ya kunenepa moyenerera kapena kuumbika kwabwino kwa thupi zimasiyana kwambiri ndi mmene anthu a m’dera linanso angaonere nkhanizi.
JULY 28–AUGUST 3
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 24
Konzekelani Pasadakhale Kulimbana Ndi Zovuta
“Khalani Olimba, Osasunthika”
Muziŵelenga Mawu a Mulungu na kuwasinkhasinkha. Mtengo umakhala wolimba ngati mizu yake inazikika pansi mozama. Mofananamo, tingakhalebe olimba ngati cikhulupililo cathu n’cozikika mozama m’Mawu a Mulungu. Mtengo ukamakula, mizu yake imaloŵa pansi kwambili na kutambalala. Tikamaŵelenga Baibo na kusinkhasinkha, timalimbitsa cikhulupililo cathu, komanso timakhala otsimikiza kothelatu kuti mfundo za Yehova ndizo zabwino koposa. (Akol. 2:6, 7) Ganizilani mmene malangizo a Yehova, citsogozo, na citetezo cake, cinathandila atumiki ake akale. Mwacitsanzo, Ezekieli anayang’anitsitsa pamene mngelo anali kuyesa kacisi m’masomphenya. Masomphenya amenewo anam’limbikitsa Ezekieli. Ndipo amatiphunzitsa mmene tingatsatilile miyeso ya Yehova pa nkhani ya kulambila koyela. (Ezek. 40:1-4; 43:10-12) Nafenso timapindula tikamapatula nthawi yoŵelenga na kusinkhasinkha zinthu zozama za m’Mawu a Mulungu.
w09-CN 12/15 18 ¶12-13
Khalanibe ndi Chimwemwe Mukamakumana ndi Mavuto
12 Lemba la Miyambo 24:10 limanena kuti: “Ukalefuka tsiku la tsoka mphamvu yako ichepa.” Mwambi winanso umati: “Moyo umasweka ndi zowawa za m’mtima.” (Miy. 15:13) Akhristu ena amakhumudwa kwambiri mpaka kusiya kuwerenga Baibulo ndi kusinkhasinkha Mawu a Mulungu. Mapemphero awo amangokhala amwambo ndipo amasiya kucheza ndi olambira anzawo. N’zoonekeratu kuti kukhala wokhumudwa kwanthawi yaitali kungativulaze.—Miy. 18:1, 14.
13 Komabe kukhala ndi maganizo abwino kungatithandize kuika maganizo athu pa zinthu zimene zingatichititse kukhala osangalala pa moyo wathu. Davide analemba kuti: “Kuchita chikondwero chanu kundikonda, Mulungu wanga.” (Sal. 40:8) Tikamakumana ndi mavuto, tisamayerekeze n’komwe kusiya kuchita zinthu zauzimu. Ndipotu njira yabwino yothetsera kukhumudwa ndiyo kuchita zinthu zimene zingatithandize kukhala osangalala. Yehova amatiuza kuti tingakhale osangalala mwa kuwerenga Mawu ake ndi kuwasinkhasinkha nthawi zonse. (Sal. 1:1, 2; Yak. 1:25) M’Baibulo ndiponso pamisonkhano yachikhristu timalandira “mawu okoma” amene angatilimbikitse komanso kutithandiza kukhala osangalala.—Miy. 12:25; 16:24.
Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga
Miyambo 24:16 imati: “Wolungama akhoza kugwa ngakhale nthawi 7 ndipo ndithu adzadzukanso.” Kodi lembali limakamba za munthu amene amagwela m’chimo mobweleza-bweleza koma Mulungu n’kumamukhululukila?
Si zimene vesiyi imatanthauza. M’malomwake, imakamba za munthu amene wagwa m’lingalilo lakuti wakumana na mavuto mobweleza-bweleza, ndipo amadzukanso m’lingalilo lakuti wakwanitsa kuwapilila mavutowo.
Inde, zimenezi zionetsa kuti Miyambo 24:16 siitanthauza kugwela m’chimo, komabe itanthauza kukumana na mavuto ngakhale mobweleza-bweleza. M’dziko loipali, munthu wolungama angadwale kapena kukumana na mavuto ena. Cina, iye angamazunzidwe kwambili na boma cifukwa ca cikhulupililo cake. Ngakhale n’telo, amakhulupilila kuti Mulungu adzam’cilikiza komanso kum’thandiza kupilila na kupambana. Dzifunseni kuti, ‘Kodi si zoona kuti zinthu nthawi zambili zimawayendela bwino atumiki a Mulungu?’ Cifukwa ciani? Cifukwa timakhulupilila kuti “Yehova amacilikiza amene ali pafupi kugwa, ndipo amawelamutsa onse amene awelama cifukwa ca masautso.”—Sal. 41:1-3; 145:14-19.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w09 10/15 12
Mafunso Ochokera kwa Owerenga
M’nthawi za m’Baibulo, ngati munthu akufuna “kumanga nyumba” yake kapena kuti kukhazikika pokwatira n’kukhala ndi ana, anayenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndine wokonzeka kusamalira ndi kuthandiza mkazi ndiponso ana amene tingakhale nawo?’ Asanakhale ndi banja, anayenera kugwira kaye ntchito kumunda. N’chifukwa chake Baibulo la Today’s English Version linamasulira vesili motere: “Usamange nyumba yako n’kukhala ndi banja pamene sunakonzeke kumunda kwako, ndipo sunatsimikize kuti uzidzapeza zofunika pa moyo.” Kodi mfundo imeneyi imagwiranso ntchito masiku ano?
Inde. Mwamuna amene akufuna kukwatira ayenera kukonzekera bwino udindo umenewo. Ngati angathe, ayenera kugwira ntchito. N’zoona kuti ntchito imene mwamuna ayenera kuchita posamalira banja lake, siyenera kukhala yongodyetsa kapena kuveka banjalo basi. Mawu a Mulungu amasonyeza kuti mwamuna amene sakonda banja lake ndiponso salisamalira mwakuthupi ndi mwauzimu, amaipa kuposa munthu wopanda chikhulupiriro. (1 Tim. 5:8) Motero, pokonzekera ukwati ndiponso moyo wabanja, mwamuna ayenera kudzifunsa mafunso monga akuti: ‘Kodi ndine wokonzeka kupezera banja langa zinthu zofunikira mwakuthupi? Kodi ndine wokonzeka kukhala mutu wa banja pa nkhani zauzimu? Kodi ndidzakwanitsa udindo wochita phunziro la Baibulo mokhazikika ndi mkazi komanso ana anga?’ Mawu a Mulungu amagogomezera kwambiri maudindo amenewa.—Deut. 6:6-8; Aef. 6:4.
Motero mnyamata amene akufuna kukwatira ayenera kuganizira bwino mfundo ya pa Miyambo 24:27. Mtsikananso ayenera kudzifunsa ngati ali wokonzeka kukwaniritsa udindo wokhala mkazi ndiponso mayi. Komanso achinyamata amene angokwatirana kumene ayenera kudzifunsa mafunso omwewa ngati akuganiza zokhala ndi ana. (Luka 14:28) Anthu a Mulungu akatsatira malangizo amenewa, amapewa mavuto ambiri ndipo amasangalala ndi moyo wabanja.
AUGUST 4-10
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 25
Malangizo Anzelu Otithandiza Kulankhula Bwino
Muzigwiritsa Ntchito Bwino Lilime Lanu
6 Lemba la Miyambo 25:11 limasonyeza kufunika kosankha bwino nthawi yolankhula. Limati: “Mawu olankhulidwa pa nthawi yoyenera ali ngati zipatso za maapozi agolide m’mbale zasiliva.” Zinthu zagolide zimakhala zokongola ndipo mukaziika m’mbale zasiliva zimaoneka bwino kwambiri. Choncho lembali likusonyeza kuti tikasankha mawu abwino n’kuwalankhulanso pa nthawi yoyenera, tingalimbikitse amene tikulankhula naye. Koma kodi tingachite bwanji zimenezi?
7 Zimene tikufuna kunena zikhoza kukhala zolimbikitsa, komabe ngati sitinazilankhule pa nthawi yoyenera sizingathandize. (Werengani Miyambo 15:23.) Mwachitsanzo mu March 2011, ku Japan kunachitika chivomerezi komanso kunasefukira madzi ndipo mizinda yambiri inawonongeka. Anthu oposa 15,000 anafa. Ngakhale kuti abale ndi alongo akuderali nawonso anakhudzidwa ndi vutoli, anayesetsa kulimbikitsa anzawo pogwiritsa ntchito Baibulo. Komabe anthu ambiri akumeneko ndi achipembedzo chachibuda moti sadziwa mfundo za m’Baibulo ndipo amakhulupirira zosiyana kwambiri ndi zimene limaphunzitsa. Choncho abale anadziwa kuti nthawiyi sinali yabwino kuti auze anthu amene anaferedwa zoti Mulungu adzaukitsa akufa. M’malomwake anangowalimbikitsa n’kuwauza kuchokera m’Baibulo chifukwa chake anthu abwino nawonso amakumana ndi mavuto.
Muzigwiritsa Ntchito Bwino Lilime Lanu
15 Tikafuna kulankhula zinazake, tiyeneranso kuganizira mmene tingalankhulire. Pamene Yesu ankalankhula m’sunagoge wa kwawo ku Nazareti, anthu ambiri ‘anadabwa ndi mawu ake ogwira mtima.’ (Luka 4:22) Tikamalankhula mwaulemu, mawu athu amakhala ogwira mtima ndipo anthu savutika kutsatira zimene tanena. (Miy. 25:15) Tingatsanzire Yesu polankhula mokoma mtima ndiponso kuchita zinthu moganizira ena. Pa nthawi ina, anthu anayesetsa kupita kumene kunali Yesu, n’cholinga choti akamve mawu ake. Iye atawaona, anawamvera chifundo ndipo “anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.” (Maliko 6:34) Ngakhale pamene anthu ankamunyoza, sanabwezere ndi mawu achipongwe.—1 Pet. 2:23.
16 Nthawi zina zimakhala zovuta kulankhula mwaulemu kwa achibale kapena anzathu mu mpingo chifukwa choti tinawazolowera. Tingaganize kuti tikhoza kuwalankhula mawu alionse ndipo sangakhumudwe. Koma kodi Yesu ankaona kuti akhoza kulankhula mawu alionse kwa ophunzira ake chifukwa choti anali anzake? Ayi. Mwachitsanzo, atumwi ake atakangana pa nkhani yakuti wamkulu ndani, Yesu anawathandiza mokoma mtima pogwiritsa ntchito chitsanzo cha mwana wamng’ono. (Maliko 9:33-37) Nawonso akulu angachite bwino kutsanzira Yesu popereka malangizo “ndi mzimu wofatsa.”—Agal. 6:1.
w95-CN 4/1 17 ¶8
Fulumizanani ku Chikondano ndi Ntchito Zabwino—MotanI??
8 Potumikira Mulungu wathu, tonsefe tingafulumizane mwa kupereka chitsanzo. Yesu anafulumizadi omvetsera ake. Anakonda ntchito ya utumiki Wachikristu ndipo analemekeza utumiki. Iye anati unali ngati chakudya chake. (Yohane 4:34; Aroma 11:13) Changu chotero chingakhale choyambukira. Kodi nanunso mungachititse chisangalalo chanu cha mu utumiki kuonekera? Uzani ena za zokumana nazo zanu zabwino mumpingo, pamene mukupeŵa mosamala kachitidwe ka kudzitamandira. Pamene mupempha ena kukagwira nanu ntchito, onani ngati mungawathandize kupeza chisangalalo chenicheni cha kulankhula ndi ena za Yehova, Mlengi wathu Wamkulu.—Miyambo 25:25.
Kufufuza Cuma Cauzimu
KUFATSA Kodi Khalidweli Limatipindulitsa Bwanji?
Kufatsa kumathandiza ngati anthu asemphana maganizo m’banja. M’bale Robert wa ku Australia anati: “N’nakambapo mawu ambili okhumudwitsa kwa mkazi wanga cifukwa cokwiya. Koma vuto n’lakuti ukakamba mawu okhumudwitsa, sungawabweze. Cinaniŵaŵa ngako kuona mmene mawuwo anakhumudwitsila mkazi wanga.”
“Tonsefe timapunthwa nthawi zambili” pa mawu, ndipo mawu okambidwa mosaganiza bwino angasokoneze mtendele m’banja. (Yak. 3:2) Zaconco zikacitika, kufatsa kumatithandiza kukhalabe odekha na kulamulila lilime lathu.—Miy. 17:27.
M’bale Robert anayesetsa kuphunzila kucita zinthu modekha ndiponso modziletsa. Kodi pakhala zotulukapo zotani? M’baleyo anati: “Masiku ano, nikasemphana maganizo na mkazi wanga, nimayesetsa kumumvetsela mosamala, kukamba modekha, na kupewa kukhumudwa. Tsopano ine na mkazi wanga timagwilizana kwambili.”
Kufatsa kumatithandiza kukhala bwino na ena. Anthu amene amakonda kukwiya msanga amakhala na mabwenzi ocepa. Koma kufatsa kumatithandiza “kusunga umodzi wathu . . . mwamtendele monga comangila cotigwilizanitsa.” (Aef. 4:2, 3) Mlongo Cathy amene tam’gwilapo kale mawu, anati: “Kufatsa kwanithandiza kuti nizicita zinthu mwamtendele na munthu aliyense, ngakhale anthu amene ni ovuta kucita nawo zinthu.”
Kufatsa kumatithandiza kukhala na mtendele wa mumtima. Baibo imagwilizanitsa “nzelu yocokela kumwamba” na khalidwe la kufatsa komanso mtendele. (Yak. 3:13, 17) Munthu wofatsa amakhala na “mtima wodekha.” (Miy. 14:30) Martin amene anayesetsa kukulitsa khalidwe la kufatsa, anati: “Tsopano ndine wololela, ndipo nili na mtendele waukulu wa mumtima na cimwemwe coculuka.”
Kukamba zoona, si copepuka munthu kukhala wofatsa. Pamafunika khama. Mwacitsanzo, m’bale wina anati: “Kukamba moona mtima, mpaka lomba nimapsa mtima kwambili nthawi zina.” Koma Yehova, amene amatilangiza kukhala ofatsa, adzatithandiza kukulitsa khalidwe limeneli. (Yes. 41:10; 1 Tim. 6:11) Iye ‘adzamalizitsa kutiphunzitsa,’ ndiponso ‘adzatilimbitsa.’ (1 Pet. 5:10) Monga Paulo, m’kupita kwa nthawi, tidzatengela “kufatsa ndi kukoma mtima kwa Khristu.”—2 Akor. 10:1.
AUGUST 11-17
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 26
Pewani Kugwilizana ndi “Anthu Opusa”
it-2-E 729 ¶6
Mvula
Nyengo. Nyengo zina ziwiri zomwe zinali ku Dziko Lolonjezedwa, zomwe ndi nyengo yotentha ndi yozizira, zingatchulidwenso kuti nyengo ya dzuwa ndi ya mvula. (Yerekezerani ndi Sl 32:4; Nym 2:11) Kuyambira chapakati pa mwezi wa April kufika chapakati pa mwezi wa October, sikunkagwa mvula yambiri. Mvula inkagwa yochepa pa nthawi imeneyi, yomwenso anthu ankakolola. Lemba la Miyambo 26:1, limasonyeza kuti anthu ankadabwa akaona mvula ikugwa munyengo yokolola. (Yerekezerani ndi 1Sa 12: 17-19.) Munyengo ya mvula, sikuti mvulayo inkangokhalira kugwa ayi, koma nthawi zina kunkakhala kopanda mitambo n’komwe. Chifukwa choti imeneyi inkakhalanso nthawi yozizira, munthu akanyowa ndi mvula ankazizidwa kwambiri. (Eza 10:9, 13) Choncho anthu ankafunikira kukhala ndi malo abwino okhala.—Yes 4:6; 25:4; 32:2; Yob 24:8.
w87-CN 10/1 19 ¶12
Chilango Chimabala Chipatso cha Mtendere
12 Ndi anthu ena kachitidwe kokulira kangafunikire, monga mmene Miyambo 26:3 ikusonyezera: “Chikoti chiyenera kavalo, ndi cham’kamwa chiyenera buru, ndi nthyole iyenera pamsana pa zitsiru.” Nthaŵi zina Yehova analola mtundu wake wa Israyeli kugonjetsedwa ndi mavuto omwe anadzibweretsera iwo eni: “Popeza anapikisana nawo mawu a Mulungu; napeputsa uphungu wa Wam’mwambamwamba. Kotero kuti anagonjetsa mtima wawo ndi chovuta; iwowa anakhumudwa koma panalibe mthandizi. Pamenepo anafuulira kwa Yehova mumsauko mwawo; ndipo anawapulumutsa m’kupsyinjika kwawo.” (Masalmo 107:11-13) Opusa ena, ngakhale kuli tero, amadzilimbitsa iwo eni kupyola kufikirika kwa mtundu uliwonse wa chilango chochiritsa: “Yemwe aumitsa khosi atadzudzulidwa kwambiri, adzasweka modzidzimutsa, palibe chomchiritsa.”—Miyambo 29:1.
it-2-E 191 ¶4
Kulemala, Ulemali
Kugwilitsa Nchito Mawuwa m’Miyambi. Mfumu ya nzelu Solomo anati: “Munthu amene amasiya ntchito yake mʼmanja mwa munthu wopusa ali ngati munthu amene wapundula mapazi ake [zimene zingamulemalitse] nʼkudzivulaza yekha.” Kunena zoona munthu amene akupatsa munthu wopusa kuti amugwilile nchito inayake ndiye kuti sakudzifunila zabwino. Iye adzaona nchito yake ikulephela ndipo idzamubweletsela mavuto.—Miy. 26:6.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-1-E 846
Wopusa
Mawu akuti kuyankha munthu wopusa mogwilizana ndi ucitsilu wake amatanthauza kuyankha munthu wopusa pogwilitsa nchito njila zake zonyoza. Kucita izi kumapangitsa kuti woyankhayo azikhala ngati citsilu. Kuti tisakhale ngati wopusa mwa njila imeneyi mwambiwu umatilangiza kuti “usayankhe aliyense wopusa mogwilizana ndi ucitsilu wake” koma pamene Miyambo 26:4,5. Imakamba kuti “ukamayankha munthu wopusa uziganizila ucitsilu wake” imaonetsa kuti nthawi zina nkothandiza kuganizila zolinga zake ndi kuonetsa kuti nzopusa komanso kuti zokamba zake nzolakwika.
AUGUST 18-24
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 27
Mene Timapindulila Tikakhala ndi Mabwenzi Enieni
Yehova Amaona Atumiki Ake Odzicepetsa Kukhala Amtengo Wapatali
12 Munthu wodzicepetsa amayamikila akapatsidwa uphungu. Tiyelekezele motele: Tinene kuti muli pa msonkhano. Ndiyeno, pambuyo pokamba na abale na alongo angapo, mmodzi wa iwo wakutengelani pa mbali na kukuuzani kuti m’maso mwanu muli manthongo. Mwacionekele, mungacite manyazi na zimenezi. Koma mungam’yamikile munthuyo cifukwa cokuuzani zimenezi. Ndipo mungaone kuti zikanakhala bwino munthu wina akanakuuzani zimenezi mwamsanga. Mofananamo, ngati m’bale kapena mlongo walimba mtima kubwela kudzatipatsa uphungu umene tikufunikila, tiyenela kuyamikila na kukhala wodzicepetsa. Tiyenela kuona munthuyo monga bwenzi lathu, osati mdani wathu.—Ŵelengani Miyambo 27:5, 6; Agal. 4:16.
it-2 491 ¶3
Munthu Woyandikana Naye Nyumba
Buku la Miyambo limaonetsa kuti n’canzelu kupempha thandizo kwa mabwenzi amene timadalila ndi kuwakhulupilila tikakumana ndi mavuto. Limati: “Usasiye mnzako kapena mnzawo wa bambo ako, ndipo usalowe mʼnyumba ya mchimwene wako pa tsiku limene tsoka lakugwela. Munthu woyandikana naye nyumba amene ali pafupi ali bwino kuposa mchimwene wako amene ali kutali.” Miy 27:10. Wolemba mwambi uyu ayenela kuti anali kutanthauza kuti bwenzi lapafupi n’lofunika kwambili komanso n’kumene tingapeze thandizo kuposa wacibale wathu cifukwa cakuti iye angakhale kuti ali kutali komanso kuti ndi wosakonzeka kutithandiza.
Acinyamata—Kodi Mudzakhala na Tsogolo Lotani?
7 Phunzilo limodzi limene tingatengepo pa cisankho coipa ca Yehoasi n’lakuti tiyenela kusankha mabwenzi amene amakonda Yehova, komanso amene amafuna kumukondweletsa. Mabwenzi aconco angatithandize kucita zinthu mwanzelu. Sitiyenela kusankha anthu a msinkhu wathu okha-okha kukhala mabwenzi athu. Kumbukilani kuti Yehoasi anali wamng’ono kwambili poyelekezela na mnzake Yehoyada. Ponena za mabwenzi anu, dzifunseni kuti: ‘Kodi amanithandiza kulimbikitsa cikhulupililo canga mwa Yehova? Kodi amanilimbikitsa kutsatila miyeso ya Yehova? Kodi amakonda kukamba za Yehova na coonadi cake ca mtengo wapatali? Kodi amalemekeza miyeso ya Mulungu? Kodi amangoniuza zonikomela m’khutu, kapena amalimba mtima na kuniwongolela nikalakwitsa?’ (Miy. 27:5, 6, 17) Kunena zoona, ngati mabwenzi anu sakonda Yehova, pezani ena. Koma ngati amakonda Yehova, akangamileni—cifukwa adzakuthandizani ngako!—Miy. 13:20.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w06-CN 9/15 19 ¶12
Mfundo Zazikulu za M’buku la Miyambo
27:21. Zimene timachita akatiyamikira zimasonyeza kuti ndife anthu otani. Kutiyamikira kukatichititsa kudziwa kuti tatha kuchita zimenezo chifukwa cha Yehova ndi kutilimbikitsa kupitiriza kum’tumikira, timasonyeza kuti ndife odzichepetsa. Ngati tayamikiridwa ndiye n’kumadzimva ngati ndife opambana, timasonyeza kuti ndife odzitukumula.
AUGUST 25-31
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 28
Kusiyana Pakati pa Munthu Woipd ndi Munthu Wolungama
w93-CN 5/15 26 ¶2
Kodi Mumatsatira Yehova ndi Mtima Wonse?
“OLUNGAMA alimba mtima ngati mkango.” (Miyambo 28:1) Amasonyeza chikhulupiriro, amadalira Mawu a Mulungu, ndipo amapita patsogolo muutumiki wa Yehova molimba mtima pokumana ndi upandu uliwonse.
it-2-E 1139 ¶3
Kudziwa Zinthu
Amene Amasiya Gwelo Lodalilika. Munthu amene amacita zoipa amaleka kudalila Mulungu akafuna kupanga zisankho kapena mapulani. (Yobu 34:27) Munthu wotelo amalola mtima wake kumusoceletsa ndipo amagwela m’mavuto komanso amakhala wosadziwa zinthu. (Sal. 36:1-4) Ngakhale kuti iye angamanene kuti amalambila Mulungu, amadalila kwambili anthu m’malo modalila Mulungu. (Yes. 29:13, 14) Akamacita khalidwe locititsa manyazi angamapeleke zifukwa zodzikhululukila n’kunena kuti anali ‘kusewelako’ cabe. (Miy. 10:23) Amayamba kupotoza zinthu, kucita zinthu mwankhanza, kusaganiza bwino, ndipo amafika ponena kuti Mulungu sakuona komanso kuti sakudziwa zimene akucita. (Sal. 94:4-10; Yes. 29:15, 16; Yer. 10:21) Pocita izi amaganiza kuti Mulungu walephela kugwilitsa nchito mphamvu zake za kuzindikila. Ndipo mwa zocita zake amakhala ngati akunena kuti “kulibe Yehova” (Sal. 14:1-3) ndipo saganiza n’komwe za Yehovayo. Cifukwa coti satsatila mfundo za Mulungu, sangasankhe zinthu zoyenela, sangaone zinthu moyenela, sangaganizile mfundo zonse za nkhani imene akufunika kusankha kmanso sangasankhe zinthu mwanzeru.—Miy. 28:5.
it-1-E 1211 ¶4
Kukhulupilika kwa Mulungu
N’zotheka kukhala okhulupirika kwa Yehova, osati ndi mphamvu zathu, koma pokhapokha ngati timakhulupirira ndi kudalira mphamvu zake zopulumutsira. (Sal. 25:21) Mulungu amalonjeza kuti adzakhala “chishango” komanso “malo achitetezo” kwa anthu okhulupirika. (Miy. 2:6-8; 10:29; Sl 41:12) Chifukwa choti anthu okhulupirikawa nthawi zonse amayesetsa kuchita zinthu zosangalatsa Yehova, amakhala ndi moyo wosangalala zomwe zimawathandiza kuti azitha kukwaniritsa zolinga zawo. (Sal. 26:1-3; Miy. 11:5; 28:18) Komabe, Yobu anakhumudwa atazindikira kuti anthu abwino amakumana ndi mavuto chifukwa cha zochita za anthu oipa ndipo akhoza kufa pamodzi ndi anthu oipawo. Koma anazindikiranso kuti ngakhale zili choncho, Yehova amakhala akuona zimene munthu wosalakwayo akukumana nazo ndipo amamutsimikizira kuti adzalandira cholowa chake, adzakhala mwamtendere m’tsogolo, komanso adzalandira zinthu zabwino. (Yobu 9: 20-22; Sal. 37:18, 19, 37; 84:11; Miy. 28:10) Monga mmene zinalili ndi Yobu, munthu amaonedwa kuti ndi wofunika kwa Mulungu ngati ali wokhulupirika, osati ngati ali ndi chuma. (Miy. 19:1; 28:6) Ana amene bambo awo ndi okhulupirika chonchi, amakhala ndi mwayi waukulu ndipo amakhala osangalala (Miy. 20:7), komanso amalemekezedwa chifukwa cha chitsanzo chabwino ndi mbiri yabwino ya bambo awo.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w01-CN 12/1 11 ¶3
Mungathe Kupeŵa Matenda a Mtima Wauzimu
Kudzidalira mopambanitsa. Anthu ambiri amene anadwalapo mtima anali kudzidalira kwambiri kuti thanzi lawo linali bwino asanayambe kudwala. Nthaŵi zambiri, ananyalanyaza kukapimitsa ku chipatala ndipo anaona ngati n’kosafunika n’komwe kuti achite zimenezo. N’chimodzimodzinso ndi ena amene amaganiza kuti popeza akhala Mkristu kwa nthaŵi yaitali, palibe chingawachitikire. Mwina anganyalanyaze kuti adzipime mwauzimu mpaka tsoka litawagwera. N’kofunika kwambiri kukumbukira langizo labwino la Paulo lakuti tipeŵe kudzidalira mopambanitsa. Iye anati: “Iye wakuyesa kuti ali chilili, ayang’anire kuti angagwe.” N’kwanzeru kuzindikira kupanda kwathu ungwiro ndi kudzipima mwauzimu nthaŵi zonse.—1 Akorinto 10:12; Miyambo 28:14.