JULY 21-27
MIYAMBO 23
Nyimbo 97 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. Malangizo Anzelu pa Nkhani ya Mowa
(Mph. 10)
Ngati mwasankha kumwa mowa, pewani kumwa kwambili (Miy. 23:20, 21; w04-CN 12/1 19 ¶5-6)
Muziganizila zotulukapo zoipa za kuledzela (Miy. 23:29, 30, 33-35; w10-CN 1/1 4 ¶7-5 ¶3)
Musapusitsidwe n’kumaganiza kuti kumwa mowa mwaucidakwa kulibe vuto lililonse (Miy. 23:31, 32)
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
Miy. 23:21—Kodi ngati munthu ndi wonenepa kwambili ndiye kuti ndi wosusuka? Fotokozani. (w04-CN 11/1 31 ¶2)
Pa kuwelenga Baibo kwa Mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuwelenga Baibo
(Mph. 4) Miy. 23:1-24 (th phunzilo 5)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 2) ULALIKI WAPOYELA. (lmd phunzilo 3 mfundo 5)
5. Kubwelelako
(Mph. 5) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Muonetseni mmene phunzilo la Baibo limacitikila. (lmd phunzilo 9 mfundo 5)
6. Kupanga Ophunzila
(Mph. 5) Limbikitsani wophunzila wanu amene akuvutika kusiya khalidwe lina lake limene silikondweletsa Yehova. (lmd phunzilo 12 mfundo 4)
Nyimbo 35
7. Kodi Ndikaikepo Mowa Kapena Ayi?
(Mph. 8) Kukambilana.
Kodi munthu amene wakonza zokhala ndi maceza kapena phwando lina lake, monga la ukwati, ayenela kuikapo mowa? Pambuyo pakuti munthuyo waganizila mosamala mfundo za m’Baibo ndi zinthu zina zofunika, monga cikhalidwe ca kwawo ndi zikumbumtima za anthu ena, ayenela kusankha yekha zocita pa nkhaniyi.
Tambitsani VIDIYO yakuti Kodi Niikeponso Mowa? Kenako funsani omvela kuti:
Kodi mfundo za m’Baibo zotsatilazi, zingathandize bwanji munthu amene akufuna kuitanila anthu kumaceza kudziwa ngati angaikepo mowa kapena ayi?
Yoh. 2:9—Yesu anasandutsa madzi kukhala vinyo pa phwando la ukwati.
1 Akor. 6:10—‘Zidakwa . . . sizidzalowa mu ufumu wa Mulungu.’
1 Akor. 10:31, 32—“Kaya mukudya kapena kumwa . . . , muzicita zinthu zonse kuti zibweletse ulemelelo kwa Mulungu. Muzipewa kukhumudwitsa” ena.
Kodi ndi zinthu ziti zimene muyenela kuganizila?
N’cifukwa ciyani tiyenela kusewenzetsa “luso la kuganiza” kuti tione mmene tingagwilitsile nchito mfundo zosiyanasiyana za m’Baibo?—Aroma 12:1; Mlal. 7:16-18
8. Zofunikila za Mpingo
(Mph. 7)
9. Phunzilo la Baibo la Mpingo
(Mph. 30) rr mutu 1 ¶1-7 ndi vidiyo ya zimene zili mmutu 1.a
Mawu Othela (Mph. 3) | ndi Pemphelo
a Ngati pa phunzilo paikidwa vidiyo yofotokoza zimene zili mmutuwo, coyamba onetsani vidiyoyo musanayambe kukambilana ndime.