JULY 28–AUGUST 3
MIYAMBO 24
Nyimbo 38 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. Konzekelani Pasadakhale Kulimbana ndi Zovuta
(Mph. 10)
Muziphunzila Baibo kuti muwonjezele cidziwitso canu (Miy. 24:5; w23.07 18 ¶15)
Mukakumana ndi zolefula musaleke kucita zinthu zauzimu (Miy. 24:10; w09-CN 10/15 12)
Kukhala wolimba mwauzimu kudzatithandiza kupezanso mphamvu tikakumana ndi zovuta (Miy. 24:16; w20.12 15)
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
Miy. 24:27—Kodi mwambi uwu utiphunzitsa ciyani? (w09-CN 12/15 18 ¶12-13)
Pa kuwelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuwelenga Baibo
(Mph. 4) Miy. 24:1-20 (th phunzilo 11)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 2) ULALIKI WAMWAYI. Makambilano atha musanamulalikile n’komwe. (lmd phunzilo 2 mfundo 4)
5. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 3) KUNYUMBA NDI NYUMBA. (lmd phunzilo 3 mfundo 4)
6. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 3) ULALIKI WAPOYELA. Muuzeni za pulogilamu yathu yophunzitsa Baibo ndi kumusiyila kakhadi kopemphela phunzilo la Baibo. (lmd phunzilo 4 mfundo 3)
7. Nkhani
(Mph. 3) lmd zakumapeto A mfundo 11—Mutu: Mulungu Anatipatsa Uthenga Wofunika Kwambili. (th phunzilo 6)
Nyimbo 99
8. Tizithandizana pa Nthawi ya Mavuto
(Mph. 15) Kukambilana.
Mwadzidzidzi kungabuke matenda ena ake, kungacitike masoka azacilengedwe, cipolowe, nkhondo kapena tingayambe kuzunzidwa. Zaconco zikacitika, abale ndi alongo athu amene akumana ndi mavuto amenewa amathandizana ndi kulimbikitsana. Komabe, ngakhale zitakhala kuti mavutowa sanacitikile ife, timakhudzidwa ndi zimene zacitikila Akhristu anzathu, ndipo timacita zilizonse zotheka kuti tiwathandize.—1 Akor. 12:25, 26.
Welengani 1 Mbiri 13:6 ndi Yakobo 5:16b. Kenako funsani omvela kuti:
N’cifukwa ciyani mapemphelo amene atumiki a Mulungu amapeleka popemphelela ena amakhala amphamvu?
Welengani Maliko 12:42-44 ndi 2 Akorinto 8:1-4. Kenako funsani omvela kuti:
Ngakhale titakhala ndi ndalama zocepa ndipo tilibe zambili zopeleka pa nchito ya padziko lonse yothandiza abale athu amene akukumana ndi mavuto, n’cifukwa ciyani sitiyenela kuleka kucita zopeleka?
Tambitsani VIDIYO yakuti Kulimbikitsa Abale pa Nthawi ya Ciletso. Kenako funsani omvela kuti:
Kodi abale anadzimana ciyani kuti athandize Akhristu anzawo omwe anali kukhala kudela komwe nchito yathu inali yoletsedwa?
Pa nthawi ya ciletso, kodi abale anacita ciyani kuti atsatile lamulo loti azisonkhana pamodzi komanso kulimbikitsana?—Aheb. 10:24, 25
9. Phunzilo la Baibo la Mpingo
(Mph. 30) rr mutu 1 ¶8-14 ndi bokosi 1A