LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb25 July masa. 11-16
  • August 11-17

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • August 11-17
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2025
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2025
mwb25 July masa. 11-16

AUGUST 11-17

MIYAMBO 26

Nyimbo 88 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Pewani Kugwilizana ndi “Anthu Opusa”

(Mph. 10)

“Munthu wopusa” sayenela kulemekezedwa (Miy. 26:1; it-2-E 729 ¶6)

“Anthu opusa” nthawi zambili amafunika kupatsidwa cilango camphamvu (Miy. 26:3; w87-CN 10/1 19 ¶12)

“Munthu wopusa” ndi wosadalilika (Miy. 26:6; it-2-E 191 ¶4)


TANTHAUZO: M’Baibo, mawu akuti “munthu wopusa” amakamba za munthu amene amakana kutsatila malangizo ndipo amacita zinthu zosagwilizana ndi mfundo za Mulungu.

M’bale wacinyamata ali kusukulu ndipo molimba mtima akucoka pamene pali anzake amene akuona zina zake pa foni.

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Miy. 26:​4, 5​—N’cifukwa ciyani sitinganene kuti miyambi iwili iyi ikutsutsana? (it-1-E 846)

  • Pa kuwelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?

3. Kuwelenga Baibo

(Mph. 4) Miy. 26:​1-20 (th phunzilo 5)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Gwilitsani nchito thilakiti poyambitsa makambilano. (lmd phunzilo 1 mfundo 5)

5. Kubwelelako

(Mph. 4) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Pitilizani kukambilana za thilakiti imene munamusiyila pa ulendo wapita. (lmd phunzilo 7 mfundo 4)

6. Kupanga Ophunzila

(Mph. 5) Thandizani wophunzila wanu kukonzekela kuti akalalikile wacibale wake. (lmd phunzilo 11 mfundo 5)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 94

7. Pezani Nzelu Zokuthandizani Kuti Mudzapulumuke mwa Kucita Phunzilo la Munthu Mwini

(Mph. 15) Kukambilana.

Zithunzi: 1. Mlongo akuwelenga m’nyumba yake. Akuonelela vidiyo ya cinenelo camanja pa jw.org pa kompyuta yake. 2. M’bale waika mahediseti ndipo akugwilitsa nchito foni powelenga pa nthawi yopuma. 3. Mlongo wacikulile akugwilitsa nchito “JW Library” pa tabuleti yake. 4. Mayi ndi mwana wake akugwilitsa nchito “JW Library” pa tabuleti pamene ali ku misonkhano.

Mtumwi Paulo anakumbutsa Timoteyo za kufunika kwa Malemba oyela omwe anawaphunzila kuyambila ali khanda. Cifukwa cophunzila Malembawo, Timoteyo anapeza ‘nzelu zomuthandiza kuti akapulumuke.’ (2 Tim. 3:15) Popeza kuti coonadi ca m’Baibo n’camtengo wapatali, m’pofunika kuti Mkhristu aliyense azipatula nthawi yowelenga Baibo. Nanga bwanji ngati simumakonda kuwelenga?

Welengani 1 Petulo 2:2. Kenako funsani omvela kuti:

  • Kodi n’zotheka kuyamba kukonda kuwelenga Baibo?

  • Kodi tingacite ciyani kuti “tizilakalaka” Mawu a Mulungu?​—w18.03 29 ¶6

  • Kodi zida za pa zipangizo zimene gulu lathu lakonza, monga JW Library®, zingatithandize bwanji kuti tizipindula kwambili powelenga Baibo?

Tambitsani VIDIYO yakuti Zimene Gulu Likukwanilitsa​—Mfundo Zothandiza Posewenzetsa JW Library. Kenako funsani omvela kuti:

  • Kodi ndi mapindu otani amene mwapeza pogwilitsa nchito JW Library®?

  • Kodi ndi mbali iti yomwe mwapeza kuti ndi yothandiza pa JW Library?

  • Nanga ndi mbali iti yomwe mufuna kuiphunzila ndi kuyamba kuigwilitsa nchito?

8. Phunzilo la Baibo la Mpingo

(Mph. 30) rr mutu 2 ¶1-9 ndi vidiyo ya zimene zili mmutu 2

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 28 ndi Pemphelo

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani