SEPTEMBER 15-21
MIYAMBO 31
Nyimbo 135 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. Zimene Tingaphunzilepo pa Malangizo Acikondi a Mayi
(Mph. 10)
Phunzitsani ana anu maganizo a Yehova pa nkhani ya kugonana komanso ukwati (Miy. 31:3, 10; w11-CN 2/1 19 ¶7-8)
Phunzitsani ana anu kuona mowa mmene Yehova amauonela (Miy. 31:4-6; ijwhf-CN nkhani 4 ¶11-13)
Phunzitsani ana anu kuti azithandiza anthu potengela Yehova (Miy. 31:8, 9; g17.6-CN 9 ¶5)
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
Miy. 31:10-31—N’ciyani cinali kuthandiza Aisiraeli kuloweza mavesi a m’Malemba Aciheberi? (w92-CN 11/1 11 ¶7-8)
Pa kuwelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuwelenga Baibo
(Mph. 4) Miy. 31:10-31 (th phunzilo 10)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 3) ULALIKI WAMWAYI. Yambitsani makambilano pambuyo pakuti munthu wakamba kapena kucita zinthu zoonetsa kukoma mtima. (lmd phunzilo 5 mfundo 3)
5. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 4) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Kambilanani naye imodzi mwa “Mfundo za m’Baibo Zimene Timafunitsitsa Kuphunzitsa Anthu” zopezeka pa zakumapeto A m’kabuku ka Kondani Anthu. (lmd phunzilo 1 mfundo 4)
6. Kubwelelako
(Mph. 5) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Itanilani munthu amene analandila Nsanja ya Mlonda Na. 1 2025 ku nkhani yapadela yotsatila. (lmd phunzilo 7 mfundo 4)
Nyimbo 121
7. Thandizani Ana Anu Kuti Azigwilitsa Nchito Zipangizo Zamakono Mwanzelu
(Mph. 8) Kukambilana.
Kodi mumaona mmene ana amagwilitsa nchito zipangizo zamakono monga foni kapena tabuleti? Nthawi zambili iwo savutika kuzigwilitsa nchito. Ngakhale kuti ana savutika kucita zimenezo, nthawi zonse iwo amafunika thandizo kuti adziwe mmene angazigwilitse nchito mwanzelu. Ngati ndinu kholo, kodi mungamuphunzitse bwanji mwana wanu kuti azigwilitsa nchito mwanzelu zipangizo zamakono?
Onetsani VIDIYO yakuti Kuseŵenzetsa Bwino Nthawi. Kenako funsani omvela kuti:
N’cifukwa ciyani n’kofunika kudziikila malile pa nthawi imene timagwilitsa nchito zipangizo zathu zamakono?
Kodi ndi zinthu zina ziti zimene tingafunike kuzipezela nthawi?
Pamene mukuika malamulo oti banja lanu lizitsatila, muzidalila mfundo za m’Baibo m’malo motsatila zimene makolo ena amacita. (Aga. 6:5) Mwacitsanzo, dzifunseni kuti:
Kodi mwana wanga waonetsa kuti ndi wodziletsadi? Kodi waonetsa kuti angapange zisankho zanzelu ngati angamagwilitse nchito cipangizo canga kapena atakhala ndi cake?—1 Akor. 9:25
Kodi ndiyenela kumulola mwana wanga kugwilitsa nchito zipangizo zamakono pamene ali yekha?—Miy. 18:1
Ndi mapulogilamu komanso mawebusaiti ati amene ndingalole mwana wanga kugwilitsa nchito? Nanga ndi ati amene sindingamulole?—Aef. 5:3-5; Afil. 4:8, 9
Kodi ndingamupatse nthawi yoculuka motani yoti azigwilitsa nchito zipangizo zamakono n’colinga coti azikhala ndi nthawi yocita zinthu zofunika?—Mla. 3:1
8. Zofunikila za Mpingo
(Mph. 7)
9. Phunzilo la Baibo la Mpingo
(Mph. 30) rr mutu 3 ¶11-20