SEPTEMBER 22-28
MLALIKI 1-2
Nyimbo 103 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. Pitilizani Kuphunzitsa M’badwo Wotsatila
(Mph. 10)
[Onetsani VIDIYO yakuti Mfundo Zokhudza Buku la Mlaliki.]
M’badwo uliwonse uli ndi udindo wophunzitsa m’badwo wotsatila (Mla. 1:4; w17.01 27-28 ¶3-4)
Pamene tiphunzitsa ena ndi kuwagawilako zocita, timawapatsa mwayi wolawako cimwemwe cimene timapeza tikamatumikila Yehova mwakhama (Mla. 2:24)
Musalephele kuphunzitsako abale acinyamata nchito poopa kuti angakulandeni maudindo amene mumakonda
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
Mla. 1:1—Kodi Baibo imatanthauza ciyani ikamanena kuti Solomo anali “wosonkhanitsa”? (it-E “Wosonkhanitsa” ¶1)
Pa kuwelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuwelenga Baibo
(Mph. 4) Mla. 1:1-18 (th phunzilo 11)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 2) ULALIKI WAMWAYI. Pambuyo pokambilanako naye, onani nkhani imene ingamucititse cidwi munthuyo ndipo panganani kuti mukakambilanenso pa nthawi ina. (lmd phunzilo 3 mfundo 5)
5. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 2) ULALIKI WAPOYELA. Kambilanani naye imodzi mwa “Mfundo za m’Baibo Zimene Timafunitsitsa Kuphunzitsa Anthu” pogwilitsa nchito njila yofotokozedwa pa zakumapeto A m’kabuku ka Kondani Anthu. (lmd phunzilo 2 mfundo 3)
6. Kubwelelako
(Mph. 2) ULALIKI WAMWAYI. Yankhani funso imene munthuyo anafunsa pa makambilano apita. (lmd phunzilo 9 mfundo 5)
7. Kupanga Ophunzila
(Mph. 5) ULALIKI WAPOYELA. Muonetseni mmene phunzilo la Baibo limacitikila ndipo panganani naye kuti mukapitilize kuphunzila. (lmd phunzilo 10 mfundo 3)
Nyimbo 84
8. Mfundo Zitatu Zofunika pa Nkhani Yophunzitsa Ena
(Mph. 15) Kukambilana.
Cikondi n’cimene cimatilimbikitsa kuphunzitsako ena kugwila nchito imene Yehova watipatsa
M’Baibo muli zitsanzo zabwino zimene zimatithandiza kudziwa mmene tingaphunzitsile ena. Tingaphunzile zambili tikaona mmene Samueli anaphunzitsila Sauli, mmene Eliya anaphunzitsila Elisa, mmene Yesu anaphunzitsila ophunzila ake, komanso mmene Paulo anaphunzitsila Timoteyo. Komabe, Yehova ndiye mphunzitsi wabwino kuposa onsewo. Kodi tingaphunzile ciyani kwa iye?
Onetsani VIDIYO yakuti Tengelani Citsanzo ca Yehova mwa Kuphunzitsako Ena (Yoh. 5:20)—Kambali Kake. Kenako funsani omvela kuti:
Kodi ndi mfundo zitatu ziti zimene tingaphunzile kwa Yehova pa nkhani yophunzitsa ena?
9. Phunzilo la Baibo la Mpingo
(Mph. 30) rr mutu 3 ¶21-30