SEPTEMBER 29–OCTOBER 5
MLALIKI 3-4
Nyimbo 93 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
Muzipeza nthawi yoceza komanso yolimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova
1. Limbitsani Ukwati Wanu
(Mph. 10)
Muzipatula nthawi yokambilana zinthu zofunika ndi mnzanu wa mu ukwati (Mla. 3:1; ijwhf-CN nkhani 10 ¶2-8)
Muzicitila zinthu pamodzi (Mla. 4:9; w23.05 23-24 ¶12-14)
Muzilimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova (Mla. 4:12; w23.05 21 ¶3)
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi kukhala kutali ndi mnzanga wa mu ukwati kwa nthawi yaitali, mwina cifukwa ca nchito kapena pa zifukwa zina, kungakhudze bwanji ukwati wathu?’
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
Mla. 3:7—Kodi mfundo ya pa lembali tingaigwilitse nchito bwanji pa nthawi ya ciletso? (w19.07 11 ¶14)
Pa kuwelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuwelenga Baibo
(Mph. 4) Mla. 4:1-16 (th phunzilo 2)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 3) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Gwilitsani nchito Nsanja ya Mlonda Na. 1 2025 poyambitsa makambilano. Sinthani ulaliki wanu ngati munthuyo waonetsa kuti ali ndi cidwi ndi nkhani inayake yosiyana ndi imene inuyo munakonzekela. (lmd phunzilo 2 mfundo 5)
5. Kubwelelako
(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. Pemphani munthu amene analandila Nsanja ya Mlonda Na. 1 2025 kuti muyambe kuphunzila naye Baibo. (lmd phunzilo 9 mfundo 4)
6. Nkhani
(Mph. 5) lmd zakumapeto A mfundo 12—Mutu: Mulungu Sakondela, Alibe Tsankho. (th phunzilo 19)
Nyimbo 131
7. Muzidalila Malangizo a Yehova m’Banja Mukabuka Mavuto
(Mph. 15) Kukambilana.
Yehova wapeleka zinthu zonse zofunikila kwa Akhristu okwatilana kuti akhale ndi banja lacimwemwe. Ngakhale n’conco, anthu amene ali pabanja amakumanabe ndi mavuto. (1 Akor. 7:28) Iwo akapanda kuthetsa mavutowo, cimwemwe cingayambe kucepa m’banjamo ndipo angaganize kuti n’zosatheka kukhalanso ndi banja lacimwemwe. Kodi mungatani ngati mukukumana ndi mavuto mu ukwati wanu?
Vidiyo yakuti Chikondi Chenicheni inaonetsa banja lacinyamata limene linakumana ndi mavuto aakulu mu ukwati wawo. Kodi mukumbukila malangizo amene tate anapeleka kwa mwana wake wamkazi pamene anali kufuna kupanga cisankho popanda kuganizila zimene Yehova anali kufuna kuti acite?
Onetsani VIDIYO yakuti Chikondi Chenicheni—Kambali Kake. Kenako funsani omvela kuti:
N’cifukwa ciyani tiyenela kudalila malangizo a Yehova tikakumana ndi mavuto mu ukwati?—Yes. 48:17; Mat. 19:6
Ngati mukukumana ndi mavuto mu ukwati wanu, musaleke kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova mwa kupitiliza kucita zinthu zauzimu. Muziyesetsa kugwilitsa nchito mfundo za m’Baibo pothetsa mavuto anu, ndipo muzifufuza malangizo m’zofalitsa zathu amene angakuthandizeni kuona zinthu mmene Yehova akuzionela. Mukatelo Yehova adzakuthandizani ndi kukudalitsani.—Miy. 10:22; Yes. 41:10.
Onetsani VIDIYO yakuti Musasoceletsedwe na Mtendele Wabodza!—Darrel na Deborah Freisinger. Kenako funsani omvela kuti:
Kodi zimene mwaphunzila pa citsanzo ca mbale ndi mlongo Freisinger zingakuthandizeni bwanji pothana ndi mavuto aakulu m’banja lanu?
8. Phunzilo la Baibo la Mpingo
(Mph. 30) rr mutu 4 ¶1-9, vidiyo ya zimene zili m’mutu 4, ndi bokosi 4A