OCTOBER 6-12
MLALIKI 5-6
Nyimbo 42 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
Aisiraeli akumvetsela mwachelu pamene wansembe akuwafotokozela mawu a m’Cilamulo
1. Mmene Timaonetsela Ulemu Waukulu kwa Mulungu Wathu Wamkulu
(Mph. 10)
Timaonetsa ulemu pamisonkhano yathu mwa kumvetsela komanso kuvala ndi kudzikongoletsa moyenela (Mla. 5:1; w08-CN 8/15 15-16 ¶17-18)
Tikamapeleka pemphelo pamisonkhano, mapemphelo athu azikhala oonetsa ulemu osati ongoculukitsa mawu (Mla. 5:2; w09-CN 11/15 11 ¶21)
Timakwanilitsa lonjezo lathu la kudzipatulila (Mla. 5:4-6; w17.04 6 ¶12)
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
Mla. 5:8—Kodi lembali lingatilimbikitse bwanji tikamacitilidwa zinthu zopanda cilungamo? (w20.09 31 ¶3-5)
Pa kuwelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuwelenga Baibo
(Mph. 4) Mla. 5:1-17 (th phunzilo 12)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 1) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Munthuyo akungofuna kukangana nanu. (lmd phunzilo 4 mfundo 5)
5. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 2) ULALIKI WAMWAYI. Kambilanani naye imodzi mwa “Mfundo za m’Baibo Zimene Timafunitsitsa Kuphunzitsa Anthu” zopezeka pa zakumapeto A m’kabuku ka Kondani Anthu. (lmd phunzilo 1 mfundo 3)
6. Kubwelelako
(Mph. 3.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Muonetseni vidiyo ya m’thuboksi yathu. (lmd phunzilo 7 mfundo 3)
7. Kupanga Ophunzila
Nyimbo 160
8. Kodi Mumagwilitsa Nchito Mbali Yakuti “Mfundo za m’Baibo Zimene Timafunitsitsa Kuphunzitsa Anthu”?
(Mph. 15) Kukambilana.
Kungocokela pamene kabuku kakuti Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila kanatulutsidwa, katithandiza kuonjezela luso lathu lokambilana ndi anthu. Mbali ya zakumapeto A inapangidwa kuti izitithandiza kuuzako ena coonadi ca m’Baibo cosavuta kumva pamene tikuceza ndi anthu. (Ahe. 4:12) Kodi mumaidziwa bwino mitu yonse 9 yopezeka pa mbali yakuti “Mfundo za m’Baibo Zimene Timafunitsitsa Kuphunzitsa Anthu”?
Tikamaceza ndi anthu, kodi tingacite ciyani kuti tiwauzeko coonadi ca m’Baibo cosavuta kumva pa nthawi yoyenela?—lmd zakumapeto A
Ndi nkhani ziti zimene anthu a m’gawo lanu amacita nazo cidwi kwambili?
Mungacite ciyani kuti muwadziwe bwino Malemba amene ali pa zakumapeto A?
Tikamagwilitsa nchito Malemba amenewa kawilikawili mu utumiki, m’pamenenso tidzawadziwa bwino. Koma kuti tigwilitse nchito malembawa mu utumiki coyamba tifunika kukambilana ndi anthu a m’gawo lathu.
Onetsani VIDIYO yakuti “Citsulo Cimanola Citsulo Cinzake”—Kufikila Anthu Ambili. kenako funsani omvela kuti:
N’ciyani cingatithandize kuti tizikambilana ndi anthu oculuka m’gawo lathu?
9. Phunzilo la Baibo la Mpingo
(Mph. 30) rr mutu 4 ¶10-17