OCTOBER 13-19
MLALIKI 7-8
Nyimbo 39 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. ‘Muzipita Kunyumba ya Malilo’
(Mph. 10)
Muzipeza nthawi yotonthoza amene anafeledwa (Mla. 7:2; w17.07 14 ¶12)
Muzitonthoza ofeledwa mwa kukamba za makhalidwe abwino amene munthu yemwe anamwalila anali nawo (Mla. 7:1; w19.06 23 ¶15)
Muzipemphela nawo limodzi anthu amene anafeledwa (w17.07 16 ¶16)
KUMBUKILANI KUTI: Nthawi zambili, anthu ofeledwa amafunika kulimbikitsidwa ndi Akhristu anzawo kwa nthawi ndithu pambuyo pa imfa ya okondedwa wawo.—w17.07 16 ¶17-19.
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
Mla. 7:20-22—Kodi lembali lingatithandize bwanji kuona ngati tingafunike kukambilana ndi munthu amene anatilakwila? (w23.03 31 ¶18)
Pa kuwelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuwelenga Baibo
(Mph. 4) Mla. 8:1-13 (th phunzilo 10)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 2) ULALIKI WAPOYELA. Pambuyo pokambilanako naye, onani nkhani imene ingamucititse cidwi munthuyo ndipo panganani kuti mukakambilanenso naye pa nthawi ina. (lmd phunzilo 2 mfundo 4)
5. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 2) ULALIKI WAMWAYI. (lmd phunzilo 2 mfundo 3)
6. Kubwelelako
(Mph. 2) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Muonetseni zinazake pa webusaiti yathu ya jw.org. (lmd phunzilo 9 mfundo 4)
7. Kufotokoza Zimene Mumakhulupilila
(Mph. 5) Citsanzo. ijwfq nkhani 50—Mutu: Kodi N’ciyani Cimacitika pa Malilo a Mboni za Yehova? (th phunzilo 17)
Nyimbo 151
8. Limbitsani Cikhulupililo Canu Cakuti Akufa Adzauka
(Mph. 15) Kukambilana.
Lonjezo lakuti akufa adzauka ndi limodzi mwa mphatso zamtengo wapatali zimene Yehova anatipatsa. Lonjezo limeneli limaonetsa kuti Yehova ali ndi mphamvu, nzelu, komanso cifundo. Koma koposa zonse, limaonetsa kuti Yehova amatikonda aliyense payekha.—Yoh. 3:16.
Tikakhala ndi cikhulupililo colimba cakuti akufa adzauka, tidzatha kupilila mavuto amene tingakumane nawo. (2 Akor. 4:16-18) Cifukwa ca ciyembekezo cimeneci timakhala ndi mtendele wa mumtima ndipo timalimbikitsidwa tikamakumana ndi cizunzo, matenda, kapena okondedwa athu akamwalila. (1 Ates. 4:13) Sitingakhale ndi cimwemwe ceniceni ngati sitimakhulupilila kuti akufa adzauka. (1 Akor. 15:19) Bwanji osadziikila colinga kuti mulimbitse cikhulupililo canu cakuti akufa adzaukitsidwa?
Welengani Yohane 11:21-24. Kenako funsani omvela kuti:
Kodi Marita anaonetsa bwanji kuti anali ndi cikhulupililo colimba cakuti akufa adzauka?
Kodi anadalitsidwa bwanji cifukwa ca cikhulupililo cake?—Yoh. 11:38-44
Onetsani VIDIYO yakuti Tengelani Citsanzo ca Akazi a Cikhulupililo Colimba!—Marita. Kenako funsani omvela kuti:
N’cifukwa ciyani ciyembekezo cakuti akufa adzauka n’cofunika kwambili kwa inu?
Kodi mungacite ciyani kuti mukhalebe ndi cikhulupililo colimba cakuti akufa adzaukitsidwa?
9. Phunzilo la Baibo la Mpingo
(Mph. 30) rr cigao 2, mutu 5 ¶1-8 ndi vidiyo ya zimene zili m’mutu 5