OCTOBER 20-26
MLALIKI 9-10
Nyimbo 30 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. Muziwaona Moyenela Mavuto Anu
(Mph. 10)
Tidziwa kuti mavuto si cizindikilo cakuti Yehova sakondwela nafe (Mla. 9:11; w13 8/1 14 ¶20-21)
Popeza tikukhala m’dziko la Satanali sitingayembekezele kuti zinthu zizicitika mwacilungamo nthawi zonse (Mla. 10:7; w19.09 5 ¶10)
Ngakhale pamene tikukumana ndi mavuto, tizipatula nthawi kuti tisangalale ndi zinthu zabwino zimene Yehova watipatsa (Mla. 9:7, 10; w11 10/15 8 ¶1-2)
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
Mla. 10:12-14—Kodi lembali lipeleka cenjezo lotani pa nkhani yokhudza mijedo? (lv 137 ¶11, 12)
Pa kuwelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuwelenga Baibo
(Mph. 4) Mla 10:1-20 (th phunzilo 11)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 3) ULALIKI WAPOYELA. Yambani kukambilana ndi munthu amene akuoneka kuti wakhumudwa. (lmd phunzilo 3 mfundo 4)
5. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. Uzan’koni munthu amene wakuuzani kuti ali ndi nkhawa cifukwa ca mavuto a zacuma mfundo imodzi yopezeka pa mbali yakuti “Mfundo Zimene Timafunitsitsa Kuphunzitsa Anthu” pa zakumapeto A m’kabuku ka Kondani Anthu (lmd phunzilo 4 mfundo 4)
6. Kupanga Ophunzila
Nyimbo 47
7. Yehova Adzakuthandizani pa Nthawi ya Mavuto
(Mph. 15) Kukambilana.
Tsiku lililonse timakumana ndi mavuto osiyanasiyana. Komabe mavuto ena amacitika mwadzidzidzi ndipo amakhala aakulu moti amatisowetsa cocita. Timaona kuti sitingakwanitse kuwapilila. Kodi ndani angatithandize tikakumana ndi mavuto?
Mosasamala kanthu za mavuto amene timakumana nawo, nthawi zonse Yehova amatithandiza kudzimva kuti ‘ndife otetezeka.’ (Yes. 33:6) Kuti Yehova atithandize, tiyenela kukhala odzicepetsa, oganiza bwino, komanso kukhala okonzeka kulandila thandizo iliyonse imene angatipatse. (Miy. 11:2) Ngati takumana ndi mavuto, tiyenela kucita zinthu modekha kuti tisankhe zinthu mwanzelu. Tiyenelanso kupatula nthawi yoti tidzisamalile tokha ndi kusamalila okondedwa athu. Tidzafunika kudzipatsanso nthawi kuti cisoni cathu cicepeko pambuyo pa imfa ya wokondedwa wathu.—Mla. 4:6
Popeza Yehova amagwilitsa nchito okhulupilila anzathu potilimbikitsa, tiyenela kulandila thandizo locokela kwa abale athu kapena kuwapempha kuti atithandize. Muzikumbukila kuti okhulupilila anzanu amakukondani kwambili ndipo ndi ofunitsitsa kukuthandizani cifukwa kucita zimenezi kumawabweletsela cimwemwe.
Welengani 2 Akorinto 4:7-9. Kenako funsani omvela kuti:
N’cifukwa ciyani tiyenela kuyesetsa kupitiliza kucita zinthu zauzimu ngakhale pamene zingaoneke zovuta kutelo?
Onetsani VIDIYO yakuti Yehova Ali Pafupi Ndi Anthu a Mtima Osweka. Kenako funsani omvela kuti:
Kodi Yehova anathandiza bwanji m’bale ndi mlongo Septer?
Kodi okhulupilila anzawo anawathandiza bwanji?
Mwaphunzilapo ciyani pa citsanzo ca m’bale ndi mlongo Septer?
8. Phunzilo la Baibo la Mpingo
(Mph. 30) rr mutu 5 ¶9-16