NOVEMBER 17-23
NYIMBO YA SOLOMO 6-8
Nyimbo 34 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. Khalani Khoma, Osati Citseko
(Mph. 10)
Alongo ake a mtsikana wa Cisulami anali kufuna kuti iye akhalebe woyela (Nyimbo 8:8, 9; w15 1/15 32 ¶15-16)
Iye anapeza mtendele cifukwa cakuti anakhalabe woyela (Nyimbo 8:10; yp-E 188 ¶2)
Pankhani yokhalabe woyela, mtsikanayu ndi citsanzo cabwino kwa acinyamata (yp2-CN 33)
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ndingathandize bwanji Akhristu a mumpingo mwathu amene ndi mbeta kukhala khoma, osati citseko?’
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
Nyimbo 8:6—N’cifukwa ciyani cikondi ceniceni cimachedwanso “lawi la Ya”? (w15 1/15 29 ¶3)
Pa kuwelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuwelenga Baibo
(Mph. 4) Nyimbo 7:1-13 (th phunzilo 12)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 2) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Gwilitsani nchito kakhadi kolowela pawebusaiti ya jw.org poyambitsa makambilano. (lmd phunzilo 4 mfundo 4)
5. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 2) ULALIKI WAPOYELA. Gwilitsani nchito thilakiti poyambitsa makambilano m’gawo la malonda. (lmd phunzilo 1 mfundo 4)
6. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 2) ULALIKI WAMWAYI. Yambani kukambilana naye mwaubwenzi, koma makambilanowo athe musanamulalikile. (lmd phunzilo 2 mfundo 4)
7. Kufotokoza Zimene Mumakhulupilila
(Mph. 5) Citsanzo. ijwfq nkhani 43—Mutu: Kodi a Mboni za Yehova Amatsatila Mfundo Ziti pa Nkhani Yokhala ndi Cibwenzi? (th phunzilo 7)
Nyimbo 121
8. Thawani Ciwelewele
(Mph. 15) Kukambilana.
M’buku la Nyimbo ya Solomo, m’busa anaitana mtsikana wa Cisulami kuti apite naye kokayenda. (Nyimbo 2:10-14) Ngakhale kuti zolinga za m’busa wacinyamatayo zinali zabwino, alongo ake a mtsikana wa Cisulami anacita zinthu mwanzelu. Anamupatsa nchito yoti agwile n’colinga coti asapite kokayendako. (Nyimbo 2:15) Alongo akewo anadziwa kuti akanamulola kupita kokayenda ndi wokondedwa wake kumalo kwaokha, zikanawacititsa kuti agwele m’mayeselo.
Baibo imalangiza Akhristu kuti ayenela ‘kuthawa ciwelewele.’ (1 Akor. 6:18) Tiyenela kupewa zilizonse zimene zingatigwetsele m’chimo la ciwelewele. Wolemba buku la Nyimbo ya Solomo analembanso kuti: “Munthu wocenjela akaona tsoka amabisala, koma wosadziwa zinthu amangopitabe ndipo amakumana ndi mavuto.”—Miy 22:3.
Onetsani VIDIYO yakuti Mulungu “Amadziwa Zinsinsi za Mumtima.” Kenako funsani omvela kuti:
Kodi mwaphunzila ciyani mu vidiyo iyi?
9. Phunzilo la Baibo la Mpingo
(Mph. 30) rr mutu 6 ¶14-19