NOVEMBER 24-30
YESAYA 1-2
Nyimbo 44 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. Ciyembekezo kwa Anthu “Olemedwa ndi Zolakwa”
(Mph. 10)
[Onetsani VIDIYO yakuti Mfundo Zokhudza Buku la Yesaya.]
Anthu a Yehova anali “olemedwa ndi zolakwa” (Yes. 1:4-6; ip-1-CN 14 ¶8)
Iwo akanalapa, Yehova anali wokonzeka kuwakhululukila ndi mtima wonse (Yes. 1:18; ip-1-CN 28-29 ¶15-17)
ZOYENELA KUSINKHASINKHA: Kodi ciitano ca Yehova ku mtundu wa Isiraeli, cingatilimbikitse bwanji ngati timaona kuti macimo athu ndi aakulu kwambili moti iye sangatikhululukile?
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
Yes. 2:2—Kodi “phiri la nyumba la Yehova” limaimila ciyani? (ip-1-CN 39 ¶9)
Pa kuwelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuwelenga Baibo
(Mph. 4) Yes. 2:1-11 (th phunzilo 11)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 3) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Kambilanani naye imodzi mwa mfundo za coonadi zopezeka pa zakumapeto A m’kabuku ka Kondani Anthu. (lmd phunzilo 3 mfundo 3)
5. Kubwelelako
(Mph. 4) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Munthuyo waonetsa cidwi ndi nkhani inayake yosiyana ndi imene munakonzekela. (lmd phunzilo 7 mfundo 4)
6. Nkhani
(Mph. 5) ijwbq nkhani 96—Mutu: Kodi Chimo N’ciyani? (th phunzilo 20)
Nyimbo 38
7. Khala Bwenzi la Yehova—Yehova Amakhululuka
(Mph. 15) Kukambilana.
Onetsani VIDIYOYI. Ndiyeno, ngati n’zotheka pemphani ana amene munawasankhilatu kuti abwele ku pulatifomu ndi kuwafunsa zimene aona mu vidiyo komanso zimene aphunzilapo.
8. Phunzilo la Baibo la Mpingo
(Mph. 30) rr mutu 7 ¶1-7, vidiyo yofotokoza zimene zili mu mutu 7