LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb25 November masa. 10-11
  • December 8-14

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • December 8-14
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2025
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku Misonkhano—2025
mwb25 November masa. 10-11

DECEMBER 8-14

YESAYA 6-8

Nyimbo 75 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Yesaya akuyang’ana kumwamba ndipo akudzipeleka kukhala mneneli wa Mulungu.

1. “Ine Ndilipo! Nditumizeni”

(Mph. 10)

Mosazengeleza, Yesaya anadzipeleka kukhala mneneli wa Mulungu (Yes. 6:8; ip-1-CN 93-94 ¶13-14)

Nchito imene Yesaya anapatsidwa inali yovuta (Yes. 6:​9, 10; ip-1-CN 95 ¶15-16)

Nchito ya mneneli Yesaya inali kuimila nchito imene Yesu anali kudzacita (Mat. 13:​13-15; ip-1-CN 99 ¶23)

Yesaya ali kumalo a malo amalonda ndipo akulengeza uthenga wa Yehova kwa Aisiraeli. Aisiraeli ena sakumvetsela uthenga wake ndipo ena akucokapo mwaukali.

ZOYENELA KUSINKHASINKHA: Kodi ndingatani kuti ndipitilize kuonetsa mzimu wodzipeleka?

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Yes. 7:​3, 4​—N’cifukwa ciyani Yehova anapulumutsa mfumu yoipa Ahazi? (w06-CN 12/1 9 ¶4)

  • Pa kuwelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?

3. Kuwelenga Baibo

(Mph. 4) Yes. 8:​1-13 (th phunzilo 5)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Kambilanani naye imodzi mwa mfundo za coonadi zopezeka pa zakumapeto A m’kabuku ka Kondani Anthu. (lmd phunzilo 4 mfundo 5)

5. Kubwelelako

(Mph. 4) KUNYUMBA NDI NYUMBA. M’pempheni kuti muyambe kuphunzila naye Baibo. (lmd phunzilo 9 mfundo 3)

6. Kubwelelako

(Mph. 5) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Muonetseni mmene phunzilo la Baibo limacitikila. (lmd phunzilo 9 mfundo 5)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 83

7. Timadziwika Cifukwa ca Nchito Yathu Yolalikila Kunyumba ndi Nyumba

(Mph. 15) Kukambilana.

Mboni za Yehova zimadziwika kuti ndi anthu amene amalalikila kunyumba ndi nyumba. Zimacita izi potengela citsanzo ca Yesu komanso ca Akhristu oyambilila.​—Luka 10:5; Mac. 5:42.

Ulaliki wa kunyumba ndi nyumba unaimitsidwa pa nthawi ya mlili wa COVID-19. Conco, tinayamba kulalikila uthenga wabwino mwa kucita ulaliki wamwayi, wa makalata komanso wa pafoni. Ndife okondwa kuti tinali ndi mwayi wophunzila njila zatsopano zimenezi za ulaliki! Komabe, kulalikila kunyumba ndi nyumba ndiyo njila yaikulu imene timalalikilila uthenga wabwino. Kodi mungathe kumagwilako nchito yolalikila kunyumba ndi nyumba kawilikawili?

Kodi kulalikila kunyumba ndi nyumba kumatithandiza bwanji kucita zotsatilazi?

  • Kufikila anthu onse a m’gawo lathu

  • Kukulitsa luso lathu la kuphunzitsa komanso kukulitsa makhalidwe monga kulimba mtima, kupanda tsankho ndi kudzimana

  • Kuyambitsa maphunzilo a Baibo

Cithunzi cocokela mu vidiyo yakuti “Kulalikila M’nyengo Iliyonse.” Alongo awili akulalikila mayi pa khoma lake.

Onetsani VIDIYO yakuti Kulalikila M’nyengo Iliyonse. Kenako funsani omvela kuti:

  • Kodi mwaphunzila ciyani kwa alengezi a ufumu odzimana a ku zilumba za Faroe?

8. Phunzilo la Baibo la Mpingo

(Mph. 30) rr mutu 7 ¶16-23

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 129 ndi Pemphelo

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani