DECEMBER 15-21
YESAYA 9-10
Nyimbo 77 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. Ulosi Wonena za “Kuwala Kwakukulu”
(Mph. 10)
Ulosi unanenelatu kuti “kuwala kwakukulu” kudzaonekela mu Galileya (Yes. 9:1, 2; Mat. 4:12-16; ip-1-CN 125-126 ¶16-17)
Ulosiwo unanenanso kuti mtundu umene udzalandile kuwalako udzakula ndiponso kuti mbadwa zake zidzasangalala (Yes. 9:3; ip-1-CN 126-128 ¶18-19)
Mapindu a kuwala kwakukuluko anali kudzakhalapo mpaka kalekale (Yes. 9:4, 5; ip-1-CN 128-129 ¶20-21)
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph 10)
Yes. 9:6—Kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti anali “Mlangizi Wodabwitsa”? (ip-1-CN 130 ¶23-24)
Pa kuwelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuwelenga Baibo
(Mph. 4) Yes. 10:1-14 (th phunzilo 11)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 3) ULALIKI WAMWAYI. Munthuyo si wacipembedzo ca Cikhristu. (lmd phunzilo 1 mfundo 4)
5. Kubwelelako
(Mph 4) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Pitilizani kukambilana za m’thilakiti imene munamusiyila pa ulendo wapita. (lmd phunzilo 9 mfundo 3)
6. Kufotokoza Zimene Mumakhulupilila
(Mph. 5) Citsanzo. ijwfq nkhani 35—Mutu: Kodi a Mboni za Yehova Anasintha Zina N’zina m’Baibulo Kuti Zigwilizane ndi Zimene Amakhulupilila? (th phunzilo 12)
Nyimbo 95
7. Kuwala Kukuwonjezeleka
(Mph. 5) Kukambilana.
Gulu la Yehova likupitabe patsogolo. Kodi mukuyendela nalo limodzi? Tiyeni tikambilane mbali zitatu za mmene gulu la Yehova likupitila patsogolo komanso mapindu amene akhalapo.
Lembani citsanzo ca mmene gulu lathu lapitila patsogolo pa kamvedwe ka coonadi ca m’Baibo komanso mmene tapindulila.—Miy. 4:18
Lembani citsanzo ca mmene nchito yolalikila yapitila patsogolo komanso mmene yathandizila kukwanilitsa nchito imene Yesu anatipatsa.—Mat. 28:19, 20
Lembani citsanzo ca masinthidwe a kayendetsedwe ka zinthu m’gulu, komanso mmene tapindulila ndi masinthidwewo.—Yes. 60:17
8. Vidiyo ya Zimene Gulu Lakwanitsa Kucita ya December
(Mph. 10) Onetsani VIDIYO.
9. Phunzilo la Baibo la Mpingo
(Mph. 30) rr mutu 7 ¶24-30 ndi bokosi 7B