DECEMBER 22-28
YESAYA 11-13
Nyimbo 14 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. Kodi Maulosi Ananenelatu Zotani Zokhudza Mesiya?
(Mph. 10)
Adzakhala mbadwa ya Jese kudzela mwa mwana wake Davide (Yes. 11:1; ip-1-CN 159 ¶4-5)
Mzimu wa Mulungu udzakhazikika pa iye komanso adzakhala woopa Yehova (Yes. 11:2, 3a; ip-1-CN 159 ¶6; 160 ¶8)
Adzakhala woweluza wacilungamo komanso wacifundo (Yes. 11:3b-5; ip-1-CN 160 ¶9; 161 ¶11)
ZOYENELA KUSINKHASINKHA: Kodi n’ciyani cimene cimapangitsa Yesu kukhala wolamulila wabwino kwambili kuposa olamulila aumunthu?
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
Yes. 11:10—Kodi ulosi umenewu wakhala ukukwanilitsidwa motani? (ip-1-CN 165-166 ¶16-18)
Pa kuwelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuwelenga Baibo
(Mph. 4) Yes. 11:1-12 (th phunzilo 11)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 3) KUNYUMBA NDI NYUMBA. (lmd phunzilo 2 mfundo 5)
5. Kubwelelako
(Mph. 4) ULALIKI WAPOYELA. Gwilitsani nchito webusaiti ya jw.org poyankha funso limene munthuyo wakufunsani. (lmd phunzilo 8 mfundo 3)
6. Kupanga Ophunzila
(Mph. 5) Thandizani wophunzila wanu kukonzekela kukalalikila nanu kunyumba ndi nyumba. (lmd phunzilo 11 mfundo 4)
Nyimbo 57
7. Kodi ‘Mumaweluza Ena Mwacilungamo’?
(Mph. 15) Kukambilana.
Tsiku lililonse timaweluza anthu ena ndipo nthawi zina timacita zimenezi mosazindikila. Nthawi zambili timaweluza ena potengela zimene timaona. Koma Yesu saweluza ena potengela maonekedwe. Conco iye ndi citsanzo cabwino kwa ife. (Yes. 11:3, 4) Yesu amaona zamumtima mwa munthu ndipo amadziwa zimene akuganiza komanso zolinga zake. Koma ife sitingathe kucita zimenezi. Ngakhale n’conco, tingathe kucita zilizonse zotheka kuti titengele citsanzo ca Yesu. Iye anati: “Siyani kuweluza potengela maonekedwe akunja, koma muziweluza ndi ciweluzo colungama.”—Yoh. 7:24.
Tikamaweluza ena potengela maonekedwe awo, cangu cathu mu utumiki cingacepe ndiponso ulaliki wathu ungakhale wosagwila mtima. Mwacitsanzo, kodi mumazengeleza kulalikila m’dela limene muli anthu a mtundu wina kapena a cipembedzo cina cake? Kodi mumazengeleza kulalikila kudela limene kuli anthu olemela kapena osauka? Kodi mumaganiza kuti munthu sangacite cidwi ndi uthenga wathu cifukwa ca mmene akuonekela? Mulungu amafuna kuti “anthu osiyanasiyana apulumuke n’kukhala odziwa coonadi molondola.”—1 Tim. 2:4.
Onetsani VIDIYO yakuti Zimene Tinaphunzila mu Nsanja ya Mlonda—Musamaweluze Poona Maonekedwe Akunja. Kenako funsani omvela kuti:
Muvidiyo iyi, kodi anthu anali kusankhana pa zifukwa ziti?
Ngati timayang’ana nkhope pocita zinthu ndi abale ndi alongo athu, kodi zimenezi zingakhudze bwanji mpingo?
N’ciyani cimene cinathandiza Akhristu amene taona muvidiyo iyi kupewa kuweluza ena potengela maonekedwe akunja?
Kodi inuyo munaphunzila ciyani m’nkhani ya m’Nsanja ya Mlonda imeneyi?
8. Phunzilo la Baibo la Mpingo
(Mph. 30) rr cigao 3, mutu 8 ¶1-7, ndi vidiyo yofotokoza zimene zili mʼmutu 8