fcafotodigital/E+ via Getty Images
Kusala Nyama olo Ciliconse Cocokela ku Zamoyo—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?
Pa dziko lonse, anthu oculukila-culukila akuyamba umoyo wosala nyama olo ciliconse cocokela ku zamoyo.
“Kusala nyama kwa mtundu umenewu kwafika pokhala ciphunzitso. Anthu a cikhulupililo cimeneci amadana nako kuvutitsa nyama kwa mtundu uliwonse, monga kuzicita nkhanza, kudya nyama, zovala zopangidwa na zinthu zocokela ku nyama, kapena kuzivutitsa mwa mtundu uliwonse.”—Inatelo bungwe la The Vegan Society.
Kuonjezela pa kufuna kuteteza nyama, anthu ena amasala nyama kothelatu pofuna kusamalila zacilengedwe, thanzi lawo, komanso pa zifukwa zina.
“Mosiyana na munthu amene wasankha kusala zakudya zina, anthu ambili amaona kuti kusala nyama kothelatu ni nkhani ya cikhulupililo komanso makhalidwe abwino, ndipo amaonanso kuti ni njila imene munthu aliyense angathandizile kuti dziko likhale labwino.”—Inatelo Britannica Academic.
Kodi kusala nyama kothelatu ndiyo njila yothetsela mavuto pa dziko? Kodi Baibo imakambapo ciyani?
Mmene Mlengi wathu amaonela anthu na nyama
Baibo imaonetsa kuti Mlengi wathu, Yehova Mulungu,a amaona anthu kukhala ofunika kwambili kuposa nyama, ndipo anaŵapatsa mphamvu zolamulila nyama. (Genesis 1:27, 28) M’kupita kwa nthawi, Mulungu analola anthu kuyamba kudya nyama. (Genesis 9:3) Ngakhale n’telo, salekelela anthu kucitila nkhanza nyama.—Miyambo 12:10.
Malinga na Baibo, kudya nyama kapena kusala nyama ni nkhani ya munthu mwini.b Zimene munthu wasankha pa nkhaniyi si zimam’pangitsa kukhala wofunika kwa Mulungu. (1 Akorinto 8:8) Palibe ayenela kuweluza mnzake cifukwa ca zimene wasankha kudya.—Aroma 14:3.
Njila Yokapezela Umoyo Wabwino
Baibo imaonetsa kuti zimene timasankha pa umoyo wathu sizingathetse mavuto a m’dziko lino. Mavuto ambili amayamba cifukwa ca zandale, cikhalidwe ca anthu, komanso kayendetsedwe ka cuma m’dziko, ndipo palibe amene angazikonze zimenezi. Baibo imati:
“Cinthu cokhota sicingawongoledwe.”—Mlaliki 1:15.
Mlengi wathu ndiye adzacotsepo mavuto omwe timakumana nawo. Baibo imaseŵenzetsa mawu ophiphilitsa pofotokoza zimene iye adzacite.
“Tsopano ndinaona kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano, pakuti kumwamba kwakale ndi dziko lapansi lakale zinali zitacoka, ndipo kulibenso nyanja.”—Chivumbulutso 21:1.
Maboma a anthu, kapena kuti “kumwamba kwakale,” adzalowedwa m’malo na “kumwamba kwatsopano,” kapena kuti boma la Kumwamba la Mulungu. Ufumu wake udzacotsapo “dziko lapansi lakale,” amene ni anthu oipa, Ndipo udzalamulila “dziko lapansi latsopano,” kapena kuti anthu amene adzagonjele ulamulilo wake.
Anthu adzakhala mwamtendele na nyama komanso zacilengedwe kokha mu ulamulilo wa Ufumu wa Mulungu.—Yesaya 11:6-9.
a Yehova ndilo dzina la Mulungu.—Salimo 83:18.
b Baibo imatilamula kuti tiyenela “kupitiliza kupewa . . . magazi.” (Machitidwe 15:28, 29) Izi zitanthauza kuti sitiyenela kumwa magazi kapena kudya nyama yosakhetsa, ndipo sitiyenela kudya cakudya ciliconse cosakanizidwa na magazi.