LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • my nkhani 71
  • Mulungu Walonjeza Paladaiso

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mulungu Walonjeza Paladaiso
  • Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Nkhani Zofanana
  • “Tidzaonana M’Paradaiso!”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2018
  • Kodi Cifunilo ca Mulungu Kwa Anthu N’ciani?
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Mmene Anataila Malo Ao Okhalako
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Kodi Mulungu Ali Nalo Colinga Canji Dziko Lapansi?
    Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu
Onaninso Zina
Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
my nkhani 71

Nkhani 71

Mulungu Walonjeza Paladaiso

CITHUNZI-THUNZI ici ni ca paladaiso imene Mulungu ayenela kuti anaonetsa mneneli wake Yesaya. Yesaya anakhalako pamene Yona anangomwalila.

Paladaiso imatanthauza “munda” kapena “paki.” Kodi paladaiso imeneyi ikukumbutsa cina cake cimene tinaona m’buku lino? Paladaiso imeneyi ifanana kwambili ndi munda wokongola umene Yehova Mulungu anapangila Adamu ndi Hava, si conco? Koma kodi n’zoona kuti dziko lonse lapansi lidzakakhala paladaiso?

Yehova anauza mneneli wake Yesaya kulemba za kubwela kwa paladaiso yatsopano ya anthu a Mulungu. Iye anati: ‘Mimbulu ndi nkhosa zidzakhala pamodzi mu mtendele. Mwana wa ng’ombe ndi mwana wa mkango adzadyela pamodzi, ndipo ana ang’ono adzazisamalila. Ngakhale khanda silidzavulazidwa pamene lidzaseŵela pafupi ndi njoka yapoizoni.’

Anthu ambili angakambe kuti: ‘Zimenezi sizingacitike iyai, cifukwa nthawi zonse padziko lapansi pali mavuto, ndipo mavuto amenewa adzapitilizabe. Koma ganizila izi: Kodi Mulungu anapatsa Adamu ndi Hava malo abwanji okhalamo?

Mulungu anaika Adamu ndi Hava m’paladaiso. Koma cifukwa cakuti sanamvele Mulungu, io anataya malo ao okongola ndi kuyamba kukalamba ndi kufa. Mulungu analonjeza kupatsa anthu amene amamukonda zinthu zokongola zimene Adamu ndi Hava anataya.

Mu paladaiso yatsopano imene idzabwela, palibe cimene cidzakhala covulaza kapena coononga. Mudzakhala mtendele weni-weni. Anthu onse adzakhala okondwela ndi athanzi. Zinthu zidzakhala monga mmene Yehova anafunila paciyambi. Koma za mmene Mulungu adzacitila zimenezi tidzaphunzila nthawi ina.

Yesaya 11:6-9; Chivumbulutso 21:3, 4.

Mafunso Ophunzilila

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani