LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • bh nkhani 12 nkhani 115-124
  • Kukhala ndi Moyo Wokondweletsa Mulungu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kukhala ndi Moyo Wokondweletsa Mulungu
  • Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • YEHOVA AMALIMBIKITSA MABWENZI AKE
  • ZIMENE SATANA ANATSUTSA
  • YOBU AYESEDWA
  • KODI INU MULOŴETSEDWAMO BWANJI M’NKHANI IMENEYI?
  • KUMVELA MALAMULO A YEHOVA
  • KUKHALA NDI MAKHALIDWE AMENE AMAKONDWELETSA MULUNGU
  • Mmene Mungakhalile Bwenzi La Mulungu
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • “Yembekezela Yehova”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
  • Yobu Anakhalabe Wokhulupilika Pamene Anali Kuyesedwa
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
  • Kodi Yobu Anali Ndani?
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
Onaninso Zina
Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
bh nkhani 12 nkhani 115-124

NKHANI 12

Kukhala ndi Moyo Wokondweletsa Mulungu

  • Kodi muyenela kucita ciani kuti mukhale bwenzi la Mulungu?

  • Kodi nkhani imene Satana anayambitsa imakuloŵetsanimo bwanji?

  • Kodi ndi makhalidwe ati amene sakondweletsa Yehova?

  • Nanga mungakhale bwanji ndi moyo wokondweletsa Mulungu?

1, 2. Chulani zitsanzo za anthu amene anakhala mabwenzi a pamtima a Yehova.

KODI mungasankhe munthu wa mtundu wanji kukhala mnzanu? Mosakaikila, mungafune munthu amene mumafanana naye maganizo, zocita ndi zimene mumakonda. Mungakonde munthu amene ali ndi makhalidwe abwino monga kukhulupilika ndi kukoma mtima.

2 M’mbili yonse ya anthu, Mulungu wasankha anthu ena kukhala mabwenzi ake a pamtima. Mwacitsanzo, Yehova anachula Abulahamu kukhala bwenzi lake. (Yesaya 41:8; Yakobo 2:23) Mulungu anakamba za Davide kuti, “munthu wa pamtima panga,” cifukwa anali mtundu wa anthu amene Yehova amakonda. (Machitidwe 13:22) Ndiponso, Yehova anali kuona mneneli Danieli monga “munthu wokondedwa kwambili.”—Danieli 9:23.

3. N’cifukwa ciani Yehova amasankha anthu ena kuti akhale mabwenzi ake?

3 N’cifukwa ciani Yehova anasankha Abulahamu, Davide, ndi Danieli kukhala mabwenzi ake a pamtima? Cifukwa cimene anacitila zimenezi n’cimene Iye anauza Abulahamu kuti: “Wamvela mau anga.” (Genesis 22:18) Conco, Yehova amayandikila anthu amene modzicepetsa amacita zimene iye awauza kucita. Yehova anauza Aisiraeli kuti: “Muzimvela mau anga, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu, inuyo mudzakhala anthu anga.” (Yeremiya 7:23) Ngati mumvela Yehova, inunso mudzakhala bwenzi lake!

YEHOVA AMALIMBIKITSA MABWENZI AKE

4, 5. Kodi Yehova amaonetsa bwanji mphamvu zake kaamba ka anthu ake?

4 Ganizilani cabe zabwino zimene mungapeze mukakhala paubwenzi ndi Mulungu. Baibo imakamba kuti Yehova amafuna-funa mipata yakuti “aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wao uli wathunthu kwa iye.” (2 Mbiri 16:9) Kodi Yehova angaonetse bwanji mphamvu zake kaamba ka inu? Njila imodzi imene angacitile zimenezi imapezeka pa Salimo 32:8, pamene Iye amati: “Ndidzakupatsa nzelu ndi kukulangiza njila yoti uyendemo. Ndidzakupatsa malangizo ndi kukuyang’anila.”

5 Mau amenewa amaonetsadi cisamalilo cacikondi cimene Yehova amapeleka kwa anthu ake. Iye adzakupatsani malangizo ofunikila, ndipo adzakucilikizani pamene muwagwilitsila nchito. Mulungu amafuna kukuthandizani kuti muzipilila mavuto ndi mayeselo. (Salimo 55:22) Conco, mukayamba kutumikila Yehova ndi mtima wanu wonse, mudzakhala ndi cidalilo monga cimene wamasalimo anali naco pamene anati: “Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse. Popeza kuti ali kudzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.” (Salimo 16:8; 63:8) Zoona, Yehova angakuthandizeni kukhala ndi moyo wocita zinthu zimene zimam’kondweletsa. Koma monga mmene mudziŵila, pali mdani wa Mulungu amene angafune kukulepheletsani kucita zimenezi.

ZIMENE SATANA ANATSUTSA

6. Kodi Satana anakaikila ciani ponena za anthu?

6 Nkhani 11 ya m’buku lino inafotokoza mmene Satana Mdyelekezi anatsutsila ulamulilo wa Mulungu. Satana ananeneza Yehova Mulungu kuti anakamba zabodza. Anam’nenezanso kuti sanacite cilungamo posalola Adamu ndi Hava kuti adzisankha okha cabwino ndi coipa. Pambuyo pakuti Adamu ndi Hava acimwa, ndipo pamene dziko lapansi linayamba kudzala ndi ana ao, Satana anakaikila colinga ca anthu onse cotumikilila Mulungu. Kukamba kwina, Satana ananeneza kuti: “Anthu samatumikila Mulungu cifukwa cakuti amamukonda.” Ndipo anapitiliza kuti: “Ndipatseni mpata cabe, ndidzapandutsa munthu aliyense kwa Mulungu.” Nkhani ya Yobu imaonetsa kuti izi n’zimene Satana anakhulupilila. Koma kodi Yobu anali ndani? Nanga analoŵetsedwamo bwanji m’nkhani yaikulu imene Satana anayambitsa?

7, 8. (a) N’ciani cinapangitsa Yobu kukhala wosiyana ndi anthu a m’nthawi yake? (b) Nanga Satana anakaikila bwanji colinga ca Yobu?

7 Yobu anakhalako pafupi-fupi zaka 3,600 zapitazo. Anali munthu wabwino, popeza Yehova anakamba kuti: “Palibe wina wokhala ngati iyeyo padziko lapansi? Iyetu ndi munthu wopanda colakwa ndi woongoka mtima, woopa Mulungu ndi wopewa zoipa.” (Yobu 1:8) Yobu anali munthu wokondweletsa Mulungu.

8 Satana anakaikila colinga ca Yobu cotumikilila Mulungu. Mdyelekezi anauza Yehova kuti: “Kodi inuyo simwam’chinga iyeyo? Mwachingilanso nyumba yake ndi ciliconse cimene ali naco. Mwadalitsa nchito ya manja ake ndipo ziŵeto zake zaculuka kwambili padziko lapansi. Koma tsopano tatambasulani dzanja lanu ndi kukhudza zonse zimene ali nazo, ndipo muona, akutukwanani m’maso muli gwa!”—Yobu 1:10, 11.

9. N’ciani cimene Yehova anacita pa zimene Satana ananeneza Yobu? Ndipo n’cifukwa ciani?

9 Conco, Satana ananeneza Yobu kuti anatumikila Mulungu cabe cifukwa ca zabwino zimene anali kupeza. Mdyelekezi anakambanso kuti ngati Yobu angayesedwe, angapandukile Mulungu. Nanga Yehova anayankha bwanji pa zimene Satana anakamba? Popeza kuti Satana anakaikila colinga ca Yobu cotumikilila Mulungu, Yehova analola Satana kuti ayese Yobu. Mwa njila imeneyi, zikanadziŵika bwino kaya Yobu anali kukonda Mulungu kapena ayi.

YOBU AYESEDWA

10. Kodi Yobu anakumana ndi mayeselo ati? Ndipo anacita bwanji?

10 Posapita nthawi, Satana anayesa Yobu m’njila zosiyana-siyana. Ziŵeto zina za Yobu zinabedwa, ndipo zina zinaphedwa. Anchito ake ambili anaphedwa. Zimenezi zinabweletsanso mavuto a zacuma. Tsoka linanso limene linagwa n’lakuti ana 10 a Yobu anaphedwa ndi cimphepo. Mosasamala kanthu za mavuto amenewa, “Yobu sanacimwe, kapena kunena kuti Mulungu wacita zosayenela.”—Yobu 1:22.

11. (a) Kodi ndi cinenezo caciŵili citi cimene Satana anakamba ponena za Yobu? (b) Ngakhale kuti Yobu anadwala matenda ozunza kwambili, kodi molimba mtima anati ciani?

11 Satana sanalekele pamenepa. Ayenela anaganiza kuti, ngakhale Yobu wapilila kutaikilidwa katundu, anchito ndi ana ake, ndiye kuti ngati angadwale matenda oopsa angam’pandukile Mulungu. Yehova analola Satana kudwalitsa Yobu ndi matenda onyansa ndi ozunza. Koma ngakhale zimenezi sizinataitse Yobu cikhulupililo cake mwa Mulungu. M’malo mwake, iye molimba mtima anati: “Mpaka ine kumwalila, sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagaŵanika.”—Yobu 27:5.

Job living happily with his wife and ten children

Yehova anadalitsa Yobu cifukwa ca kukhala wokhulupilika

12. Kodi mmene Yobu anacitila zinthu zinaonetsa ciani pa zimene Mdyelekezi anakamba?

12 Yobu sanadziŵe kuti Satana ndi amene anali kubweletsa mavuto pa iye. Posadziŵa nkhani imene inalipo, yakuti Mdyelekezi anali kutsutsa ulamulilo wa Yehova, Yobu anaganiza kuti Mulungu ndi amene anali kubweletsa mavutowo pa iye. (Yobu 6:4; 16:11-14) Ngakhale ndi conco, Yobu anakhalabe wokhulupilika kwa Yehova. Ndiponso, kukhulupilika kwake kunaonetsa poyela bodza la Satana lakuti Yobu anali kutumikila Mulungu cifukwa ca zabwino zimene anali kupeza.

13. Kodi kukhulupilika kwa Yobu kunapangitsa Yehova kucita ciani?

13 Kukhulupilika kwa Yobu kunapangitsa Yehova kukhala ndi coyankhapo pa mau onyoza a Satana. Yobu analidi bwenzi la Yehova, ndipo Mulungu anam’dalitsa cifukwa ca kukhala wokhulupilika.—Yobu 42:12-17.

KODI INU MULOŴETSEDWAMO BWANJI M’NKHANI IMENEYI?

14, 15. N’cifukwa ciani tingakambe kuti cinenezo ca Satana cokhudza Yobu cimaloŵetsamo anthu onse?

14 Nkhani ya kukhala wokhulupilika kwa Mulungu imene Satana anayambitsa sinali pa Yobu yekha. Inunso mumaloŵetsedwamo. Lemba la Miyambo 27:11, limaonetsa bwino zimenezi. Palembali Mau a Yehova amati: “Mwana wanga, khala wanzelu ndi kukondweletsa mtima wanga, kuti ndimuyankhe amene akunditonza.” Mau amenewa, amene analembedwa zaka zambili pambuyo pa imfa ya Yobu, amaonetsa kuti Satana anali akali kutonza Mulungu ndi kuneneza atumiki ake. Ngati tikhala ndi moyo wokondweletsa Yehova, timaonetsa kuti zimene Satana anakamba ndi zabodza, ndipo timakondweletsa mtima wa Mulungu. Kodi inu mungamve bwanji ngati mungacite zimenezi? Kodi sicingakhale cinthu cokondweletsa ngati inunso mungaonetse kuti zokamba za Mdyelekezi n’zabodza, ngakhale kuti zimenezi zingafune kuti musinthe zinthu zina pa umoyo wanu?

15 Onani kuti Satana anakamba kuti: “Munthu angalolele kupeleka ciliconse cimene ali naco kuti apulumutse moyo wake.” (Yobu 2:4) Mwa kukamba kuti “munthu,” Satana anaonetsa poyela kuti cinenezo cake sicinali pa Yobu yekha koma kwa anthu onse. Mfundo imeneyi ndi yofunika kuidziŵa. Satana amakaikila ngakhale kukhulupilika kwanu kwa Mulungu. Iye angafune kukulepheletsani kumvela Mulungu, ndi kuti muleke kutsatila njila ya cilungamo pamene mukumana ndi mavuto. Kodi Satana angacite bwanji zimenezi?

16. (a) Kodi Satana amagwilitsila nchito njila ziti pofuna kupandutsa anthu kwa Mulungu? (b) Kodi Mdyelekezi angagwilitsile nchito bwanji njila zimenezi pa inu?

16 Monga mmene tinaonela m’Nkhani 10, Satana amagwilitsila nchito njila zosiyana-siyana pofuna kupandutsa anthu kwa Mulungu. Iye amaukila “ngati mkango wobangula, wofunitsitsa kuti umeze winawake.” (1 Petulo 5:8) Conco, mphamvu ya Satana imaoneka pamene mabwenzi athu, acibanja, kapena anthu ena amatitsutsa pamene tiphunzila Baibo ndi kugwilitsila nchito zimene tiphunzila.a (Yohane 15:19, 20) Kumbali ina, Satana “amadzisandutsa mngelo wa kuwala.” (2 Akorinto 11:14) Mdyelekezi angagwilitsile nchito njila za macenjela kuti akusoceletseni ndi kukunyengelelani kuti muleke kucita zinthu zokondweletsa Mulungu. (Miyambo 24:10) Kaya Satana acite zinthu monga “mkango wobangula” kapena monga “mngelo wa kuwala,” cinenezo cake sicisintha, cakuti: Mukakumana ndi mavuto ndi mayeselo, mudzaleka kutumikila Mulungu. Kodi mungaonetse bwanji kuti Satana ni wabodza ndi kukhalabe wokhulupilika kwa Mulungu, monga mmene Yobu anacitila?

KUMVELA MALAMULO A YEHOVA

17. Kodi cifukwa cacikulu cimene tiyenela kumvelela malamulo a Yehova n’ciani?

17 Mungaonetse kuti Satana ndi wabodza mwa kukhala ndi umoyo wokondweletsa Mulungu. Kodi zimenezi zimafuna kuti ticite ciani? Baibo imayankha kuti: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse.” (Deuteronomo 6:5) Cikondi canu pa Mulungu cikamakula, mudzakhala ndi mtima wofuna kucita zimene iye amafuna. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake.” Ngati mukonda Yehova ndi mtima wanu wonse, mudzaona kuti ‘malamulo ake ndi osalemetsa.’—1 Yohane 5:3.

18, 19. (a) Kodi malamulo ena a Yehova ndi ati? (Onani bokosi papeji 122.) (b) Kodi timadziŵa bwanji kuti Mulungu samatipempha kucita zimene sitingakwanitse?

18 Kodi malamulo a Yehova amakamba za ciani? Ena amakamba za makhalidwe amene tiyenela kupewa. Mwacitsanzo, onani bokosi limene lili papeji 122, la mutu wakuti “Pewani Zimene Yehova Amadana Nazo.” Pamenepo mudzapeza mndandanda wa makhalidwe amene Baibo imatsutsa. Poyamba, makhalidwe ena amene ali pa mndandandapo angaoneke ngati abwino-bwino. Koma mukaganizilapo pa malemba amene aikidwa pamenepo, mudzaona nzelu imene ili m’malamulo a Yehova. Kusintha makhalidwe anu kungakhale cinthu covuta kwambili kupambana zinthu zonse zimene munacitapo. Komabe, kukhala ndi umoyo wokondweletsa Mulungu kumabweletsa cimwemwe ceni-ceni. (Yesaya 48:17, 18) Izi n’zotheka ngakhale kwa inu. Kodi tidziŵa bwanji zimenezi?

19 Yehova samatipempha kucita zinthu zimene sitingakwanitse. (Deuteronomo 30:11-14) Iye amadziŵa zimene tingakwanitse kucita ndi zimene tingalephele, kuposa ngakhale mmene ife eni timadziŵila. (Salimo 103:14) Ndiponso, Yehova angatipatse mphamvu zakuti tikwanitse kucita zimene iye amafuna. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mulungu ndi wokhulupilika ndipo sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapilile, koma pamene mukukumana ndi mayeselowo iye adzapeleka njila yopulumukila kuti muthe kuwapilila.” (1 Akorinto 10:13) Kuti Yehova akuthandizeni kupilila, angakupatseni ngakhale “mphamvu yoposa yacibadwa.” (2 Akorinto 4:7) Pambuyo popilila mayeselo, Paulo anakamba kuti: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kucokela kwa iye amene amandipatsa mphamvu.”—Afilipi 4:13.

KUKHALA NDI MAKHALIDWE AMENE AMAKONDWELETSA MULUNGU

20. Kodi ndi makhalidwe a Mulungu ati amene inu muyenela kukhala nao? Ndipo n’cifukwa ciani ali ofunika?

20 Kukondweletsa Yehova kumaloŵetsamo kucita zambili osati cabe kupewa zimene amadana nazo. Mufunikilanso kukonda zimene amakonda. (Aroma 12:9) Kodi sim’makonda anthu amene mumafanana nao maganizo, zocita ndi zimene mumakonda? Yehova nayenso n’cimodzi-modzi. Conco, phunzilani kukonda zinthu zimene Yehova amakonda. Zina mwa zimenezi azifotokoza pa Masalimo 15:1 mpaka 5, pamene timaŵelenga za anthu amene Mulungu amawaona kukhala mabwenzi ake. Mabwenzi a Yehova amaonetsa makhalidwe amene Baibo imacha kuti “cipatso ca mzimu.” Cipatso cimeneci cimaphatikizapo “cikondi, cimwemwe, mtendele, kuleza mtima, cifundo, kukoma mtima, cikhulupililo, cifatso, ciletso.”—Agalatiya 5:22, 23, Buku Lopatulika.

21. N’ciani cingakuthandizeni kukhala ndi makhalidwe amene Mulungu amakonda?

21 Kuŵelenga ndi kuphunzila Baibo nthawi zonse kudzakuthandizani kukhala ndi makhalidwe amene Mulungu amakonda. Ndipo kuphunzila zimene Mulungu amafuna kudzakuthandizani kukhala ndi maganizo ogwilizana ndi a Mulungu. (Yesaya 30:20, 21) Pamene mukulitsa cikondi canu pa Yehova, m’pamenenso mudzafuna kwambili kukhala ndi umoyo wokondweletsa Mulungu.

22. Kodi mukakhala ndi umoyo wokondweletsa Mulungu cidzacitika n’ciani?

22 Kukhala ndi umoyo wokondweletsa Yehova kumafuna kulimbikila. Baibo imaonetsa kuti kusintha umoyo kuli ngati kuvula umunthu wakale ndi kuvala watsopano. (Akolose 3:9, 10) Koma ponena za malamulo a Yehova, wamasalimo analemba kuti: ‘Munthu wowasunga amapeza mphoto yaikulu.’ (Salimo 19:11) Inunso mudzaona kuti kukhala ndi umoyo wokondweletsa Mulungu kumabweletsa madalitso ambili. Mukacita zimenezi, mudzaonetsa kuti Satana ndi wabodza, ndipo mudzakondweletsa mtima wa Yehova!

PEWANI ZIMENE YEHOVA AMADANA NAZO

People choosing lifestyles of stealing, crime, violence, drunkenness, and immorality
  • Kupha munthu.—Ekisodo 20:13; 21:22, 23.

  • Ciwelewele.—Levitiko 20:10, 13, 15, 16; Aroma 1:24, 26, 27, 32; 1 Akorinto 6:9, 10.

  • Kukhulupilila za mizimu.—Deuteronomo 18:9-13; 1 Akorinto 10:21, 22; Agalatiya 5:20.

  • Kupembedza mafano.—1 Akorinto 10:14.

  • Kukolewa.—1 Akorinto 5:11.

  • Kuba.—Levitiko 6:2, 4; Aefeso 4:28.

  • Kunama.—Miyambo 6:16, 19; Akolose 3:9; Chivumbulutso 22:15.

  • Umbombo.—1 Akorinto 5:11.

  • Ciwawa.—Salimo 11:5;—Miyambo 22:24, 25; Malaki 2:16; Agalatiya 5:20, 21.

  • Kukamba zosayenela.—Levitiko 19:16; Aefeso 5:4; Akolose 3:8.

  • Kugwilitsila nchito magazi molakwa.—Genesis 9:4; Machitidwe 15:20, 28, 29.

  • Kusafuna kusamalila banja.—1 Timoteyo 5:8.

  • Kutenga mbali pa nkhondo kapena pa nkhani za ndale za dziko lino.—Yesaya 2:4; Yohane 6:15; 17:16.

  • Fodya kapena mankhwala osokoneza ubongo.—Maliko 15:23; 2 Akorinto 7:1.

a Apa sititanthauza kuti aliyense amene angakutsutseni ndiye kuti amatsogoleledwa ndi Satana mwacindunji. Koma Satana ndiye Mulungu wa dongosolo lino la zinthu, ndipo dziko lonse lili m’manja mwake. (2 Akorinto 4:4; 1 Yohane 5:19) Mwa ici, anthu ena sadzatikonda cifukwa cokhala ndi umoyo wokondweletsa Mulungu, ndipo ena adzatitsutsa.

ZIMENE BAIBO IMAPHUNZITSA

  • Mungakhale bwenzi la Mulungu mwa kumvela malamulo ake.—Yakobo 2:23.

  • Satana anakaikila kukhulupilika kwa anthu onse.—Yobu 1:8, 10, 11; 2:4; Miyambo 27:11.

  • Tiyenela kupewa makhalidwe amene Mulungu sakondwela nao.—1 Akorinto 6:9, 10.

  • Tingakondweletse Yehova ngati tidana ndi zimene iye amadana nazo ndi kukonda zimene amakonda.—Aroma 12:9.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani