LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • bh nkhani 5 nkhani 47-56
  • Dipo la Yesu—Mphatso ya Mulungu Yopambana Zonse

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Dipo la Yesu—Mphatso ya Mulungu Yopambana Zonse
  • Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KODI DIPO LA YESU N’CIANI?
  • MMENE YEHOVA ANAPELEKELA DIPO
  • MMENE DIPO LINGAKUPINDULITSILENI
  • KODI MUNGAONETSE BWANJI KUTI MUMAYAMIKILA?
  • Dipo Ni Mphatso Ya Mulungu Yopambana Zonse
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Pitilizani Kuyamikila Dipo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • Ni Mphatso Iti Yoposa Zonse?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
  • Dipo—‘Mphatso Yangwilo’ Yocokela kwa Atate
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
bh nkhani 5 nkhani 47-56

NKHANI 5

Dipo la Yesu—Mphatso ya Mulungu Yopambana Zonse

  • Kodi dipo la Yesu n’ciani?

  • Nanga linapelekedwa bwanji?

  • Kodi dipo la Yesu lingakupindulitseni bwanji?

  • Nanga mungaonetse bwanji kuti mumaliyamikila?

1, 2. (a) Kodi n’ciani cingapangitse mphatso kukhala yofunika kwambili kwa inu? (b) N’cifukwa ciani tingakambe kuti dipo la Yesu ndiyo mphatso yopambana imene mungalandile?

KODI mungaganizile mphatso imene munapatsidwapo paumoyo wanu yopambana zonse? Kuti mphatso ikhale yofunika kwambili, sifunika kucita kukhala yodula, cifukwa kufunika kwa mphatso sikukhala pa kuculuka kwa ndalama zimene anaigulila. M’malo mwake, mphatso imene imakhala yofunika kopambana ndi imene imakupatsani cimwemwe ceni-ceni, kapena imene imakuthandizani pa cinthu cofunika kwambili paumoyo wanu.

2 Pa mphatso zonse zimene mungafune kulandila, pali imodzi yokha imene imapambana zonse. Imeneyi ndi mphatso imene Mulungu anapatsa anthu. Yehova watipatsa zinthu zambili. Koma mphatso yopambana zonse imene anatipatsa ndiyo Mwana wake amene analola ndi mtima wonse kudzatifela. (Aroma 6:23) Monga tidzaonela m’nkhani ino, dipo la Yesu ndiyo mphatso yopambana ina iliyonse imene mungalandile. Zili conco cifukwa mphatso imeneyi ingakubweletseleni cimwemwe ceni-ceni, ndipo ingakupangitseni kupeza zinthu zofunika koposa paumoyo wanu. Conco, dipo ndiyo njila yopambana zina zonse imene Yehova anaonetsela kuti amakukondani.

KODI DIPO LA YESU N’CIANI?

3. Kodi dipo la Yesu n’ciani? Ndipo tiyenela kumvetsetsa ciani kuti tiimvetse bwino mphatso yamtengo wapatali imeneyi?

3 Mwacidule, dipo la Yesu ndi njila imene Yehova anagwilitsila nchito kupulumutsa anthu ku ucimo ndi imfa. (Aefeso 1:7) Kuti timvetsetse ciphunzitso ca m’Baibo cimeneci, tiyenela kuganizila zimene zinacitika kale m’munda wa Edeni. Tikamvetsetsa zimene Adamu anataya pamene anacimwa m’pamenenso tingamvetse bwino cifukwa cake dipo lili mphatso yamtengo wapatali kwa ife.

4. Kodi umoyo wa Adamu unali wotani pokhala munthu wangwilo?

4 Pamene Yehova analenga Adamu, anam’patsa cinthu cina cake camtengo wapatali—moyo wangwilo. Ganizilani mmene moyo wangwilo unalili kwa Adamu. Popeza analengedwa ndi thupi ndi maganizo angwilo, iye sakanadwala, kukalamba, kapena kufa. Pokhala munthu wangwilo, anali paubwenzi wapadela ndi Yehova. Baibo imakamba kuti Adamu anali “mwana wa Mulungu.” (Luka 3:38) Conco, anali pa mgwilizano wabwino kwambili ndi Yehova Mulungu, monga mmene zimakhalila kwa tate ndi mwana wake amene amam’konda kwambili. Yehova anali kukambitsana ndi mwana wake wa padziko lapansi nthawi zonse. Anali kum’patsa nchito zokondweletsa ndi kum’dziŵitsa zimene anali kufunikila kucita.—Genesis 1:28-30; 2:16, 17.

5. Kodi Baibo imatanthauza ciani pamene imati Adamu anapangidwa “m’cifanizilo ca Mulungu”?

5 Adamu anapangidwa “m’cifanizilo ca Mulungu.” (Genesis 1:27) Koma si kuti Adamu anali wa maonekedwe ofanana ndi Mulungu. Monga mmene tinaphunzilila mu Nkhani 1 ya buku lino, Yehova ndi mzimu wosaoneka. (Yohane 4:24) Zimenezi zitanthauza kuti Yehova sali ndi thupi la nyama ndi magazi. Pokhala kuti Adamu analengedwa m’cifanizilo ca Mulungu, iyenso anali ndi makhalidwe a Mulungu, monga cikondi, nzelu, cilungamo, ndi mphamvu. Adamu analinso wofanana ndi Atate wake m’njila inanso yofunika, yakuti anali ndi ufulu wodzisankhila zocita. Conco, Adamu sanali ngati makina amene amangocita zimene anthu analinganiza kale kuti azicita. Iye anali ndi ufulu wopanga yekha zosankha, kusiyanitsa cabwino ndi coipa. Akanasankha kumvela Mulungu akanakhala ndi moyo wosatha m’Paladaiso padziko lapansi.

6. Pamene Adamu sanamvele Mulungu, kodi anataya ciani? Ndipo ana ake zinawakhudza bwanji?

6 Conco, n’zoonekelatu kuti pamene Adamu sanamvele Mulungu ndi kuweluzidwa kuti adzafa, anataya cinthu camtengo wapatali kwambili. Ucimo wake unam’tayitsa moyo wake wangwilo pamodzi ndi mapindu ake onse. (Genesis 3:17-19) Comvetsanso cisoni n’cakuti, sanataye moyo wangwilo wake wokha, koma anatayanso wa ana ake a mtsogolo. Mau a Mulungu amati: ‘Monga mmene ucimo unaloŵela m’dziko kudzela mwa munthu mmodzi [Adamu], ndi imfa kudzela mwa ucimo, imfayo inafalikila kwa anthu onse cifukwa onse anacimwa.’ (Aroma 5:12) Inde, tonse tinatengela ucimo kwa Adamu. Ndiye cifukwa cake Baibo imakamba kuti ‘anadzigulitsa’ iye yekha ndi ana ake mu ukapolo ku ucimo ndi imfa. (Aroma 7:14) Panalibenso ciyembekezo ciliconse kwa Adamu ndi Hava cifukwa io anasankha dala kusamvela Mulungu. Nanga bwanji za ana ao, kuphatikizapo ife?

7, 8. Kodi dipo limatanthauza zinthu ziŵili ziti kweni-kweni?

7 Yehova analanditsa anthu mwa kupeleka dipo. Kodi dipo n’ciani? Dipo kweni-kweni limatanthauza zinthu ziŵili. Coyamba, dipo ndi malipilo amene amapelekedwa pofuna kumasula munthu kapena kuombola cinthu. Tingafanizile ndi malipilo amene zigaŵenga zingafune kuti zimasule munthu amene zam’gwila. Caciŵili, dipo ndi ndalama zopelekedwa kulipilila cinthu. Lili ngati ndalama zolipilila cinthu cimene caonongedwa, kapena munthu amene wavulazidwa. Mwacitsanzo, ngati munthu waononga cinthu mwangozi angafunikile kulipila ndalama zolingana ndendende ndi mtengo wa cinthu cimene iye waononga.

8 Kodi zinatheka bwanji kulipilila zimene Adamu anatitayila? Nanga Mulungu anapeleka njila yanji yotimasula mu ukapolo ku ucimo ndi imfa? Tiyeni tione mmene Yehova anacitila zimenezi mwa kupeleka dipo, ndi mmene tingapindulile nalo.

MMENE YEHOVA ANAPELEKELA DIPO

9. Kodi panafunikila dipo la mtundu wanji?

9 Popeza kuti moyo umene unatayika unali wangwilo, moyo wa munthu aliyense wopanda ungwilo sukanatha kuuombola. (Salimo 49:7, 8) Panafunikila dipo la mtengo wolingana ndendende ndi moyo wangwilo umene unatayika. Zimenezi n’zogwilizana ndi lamulo la cilungamo ceni-ceni lochulidwa m’Mau a Mulungu, pamene amati: “Moyo kulipila moyo.” (Deuteronomo 19:21) Conco, n’ciani cikanalipilila moyo wangwilo umene Adamu anataya? Cimene cinafunikila cinali moyo wina wangwilo kuti ukhale “dipo lokwanila ndendende” ndi moyo wangwilo umene unatayika.—1 Timoteyo 2:6.

10. Kodi Yehova anapeleka bwanji dipo?

10 Koma kodi Yehova analipeleka bwanji dipo limenelo? Anatumiza mmodzi wa ana ake angwilo akumwamba kubwela padziko lapansi. Yehova sanangotenga mwana wake aliyense wakumwamba n’kumutumiza. M’malo mwake, anatumiza mwana wake wapamtima. Inde, Mwana wake wobadwa yekha. (1 Yohane 4:9, 10) Mwana ameneyo analola ndi mtima wonse kusiya malo ake kumwamba. (Afilipi 2:7) Monga mmene tinaphunzilila mu Nkhani 4 ya buku lino, Yehova anacita cozizwitsa pamene anasamutsila moyo wa Mwana wake m’mimba mwa Mariya. Mwa mphamvu ya mzimu woyela wa Mulungu, Yesu anabadwa monga munthu wangwilo. Conco, iye sanatengeleko colowa ca ucimo.—Luka 1:35.

Jesus’ agonizing death on a torture stake

Yehova anapeleka Mwana wake wobadwa yekha monga dipo lotiombola

11. Kodi zinatheka bwanji kuti munthu mmodzi akhale dipo loombola anthu ambili-mbili?

11 Kodi zinatheka bwanji kuti munthu mmodzi akhale dipo lokwanitsa kuombola anthu mamiliyoni ambili-mbili? Kumbukilani zimene zinacitika kuti anthu onse akhale ocimwa? Pamene Adamu anacimwa, anataya moyo wangwilo. Conco, iye sakanathanso kupatsila moyo wangwilo kwa ana ake. M’malo mwake, iye anapatsila ana ake ucimo ndi imfa. Yesu, amene Baibo imamucha “Adamu womalizila,” anali ndi moyo wangwilo monga munthu, ndipo sanacimwepo. (1 Akorinto 15:45) Kunena kwina, tingati Yesu analoŵa m’malo mwa Adamu kuti atipulumutse. Mwa kupeleka moyo wake wangwilo pocita cifunilo ca Mulungu mokhulupilika, Yesu anapeleka mtengo wolipilila zimene zinataika cifukwa ca ucimo wa Adamu. Mwa njila imeneyi, Yesu anapeleka ciyembekezo kwa mbadwa za Adamu.—Aroma 5:19; 1 Akorinto 15:21, 22.

12. Kodi kukhulupilika kwa Yesu kunatsimikizila ciani?

12 Baibo imafotokoza mwatsatane-tsatane zovuta zimene Yesu anapilila mpaka kufa. Anakwapulidwa koopsa, kupacikidwa mwankhanza, ndi kufa imfa yoŵaŵa pa mtengo wozunzikilapo. (Yohane 19:1, 16-18, 30; Zakumapeto, mapeji 205 mpaka 206) Koma n’cifukwa ciani kunali kofunikila kuti Yesu avutike conco? M’nkhani yakutsogolo m’buku lino, mudzaona kuti Satana anayambitsa cikaiko cakuti anthu sangakhalebe okhulupilika kwa Yehova akakumana ndi mayeselo. Pamene Yesu anakhalabe wokhulupilika ngakhale pokumana ndi mavuto aakulu, anatsimikizila kuti Satana anali wabodza pa cikaiko cimene anayambitsa. Pamene Yesu anali padziko lapansi, anaonetsa kuti zinali zotheka kuti munthu wangwilo, wokhala ndi ufulu wodzisankhila zocita, akhalebe wokhulupilika kwa Mulungu mosasamala kanthu ndi zimene Mdyelekezi akanacita. Ganizilani cabe mmene Yehova anakondwelela kuona kukhulupilika kwa Mwana wake wokondedwa ameneyu!—Miyambo 27:11.

13. Kodi dipo linapelekedwa bwanji?

13 Kodi dipo linapelekedwa bwanji? Pa Nisani 14, m’caka ca 33 C.E., pakalenda ya Ciyuda, Yehova analolela kuti mwana wake wangwilo ndi wopanda ucimo aphedwe. Conco, Yesu anapeleka moyo wake wangwilo monga munthu “kamodzi kokha.” (Aheberi 10:10) Patsiku lacitatu Yesu atamwalila, Yehova anamuukitsila ku moyo wauzimu. Pamene Yesu anabwelela kumwamba anapeleka kwa Mulungu mtengo wa moyo wake wangwilo, umene anapeleka monga dipo loombola ana a Adamu. (Aheberi 9:24) Yehova analandila mtengo wa nsembe ya Yesu monga dipo limene linafunikila kulanditsa mtundu wa anthu mu ukapolo ku ucimo ndi imfa.—Aroma 3:23, 24.

MMENE DIPO LINGAKUPINDULITSILENI

14, 15. Kodi tiyenela kucita ciani kuti ‘macimo athu akhululukidwe’?

14 Ngakhale kuti tili ocimwa, tikhoza kupeza madalitso abwino kwambili cifukwa ca dipo. Tiyeni tione ena mwa madalitso amene tingapeze pali pano ndi mtsogolo, cifukwa ca mphatso yopambana zonse yocokela kwa Mulungu imeneyi.

15 Kukhululukidwa macimo. Popeza kuti tinatengela ucimo, kucita zinthu zabwino kumakhala cinthu covuta kwa ife. Ife tonse timacimwa m’mau kapena m’zocita. Koma mwa nsembe ya dipo la Yesu, ‘macimo athu angakhululukidwe.’ (Akolose 1:13, 14) Koma kuti tikhululukidwe macimo athu, tifunikila kulapa mocokela pansi pa mtima. Tiyenelanso kupempha modzicepetsa kuti Yehova atikhululukile, cifukwa ca cikhulupililo cimene tili naco m’nsembe ya dipo la Yesu.—1 Yohane 1:8, 9.

16. N’ciani cimatithandiza kulambila Mulungu ndi cikumbumtima coyela? Ndipo cikumbumtima coyela cili ndi ubwino wanji?

16 Cikumbumtima coyela pamaso pa Mulungu. Cikumbumtima covutitsidwa cingapangitse munthu kutaya mtima mosavuta ndi kudziona kukhala wopanda pake. Komabe, kupyolela mwa cikhululukilo cimene cimatheka cifukwa ca dipo la Yesu, Yehova mokoma mtima amatilola kum’lambila ndi cikumbumtima coyela ngakhale kuti ndife opanda ungwilo. (Aheberi 9:13, 14) Zimenezi zimatithandiza kuti tikhale ndi ufulu wa kulankhula ndi Yehova m’pemphelo. (Aheberi 4:14-16) Kukhala ndi cikumbumtima coyela kumatipatsa mtendele wa maganizo, kumatisungila ulemu, ndiponso kumatipatsa cimwemwe.

17. Kodi imfa ya Yesu inatibweletsela madalitso ati?

17 Ciyembekezo ca moyo wosatha m’paladaiso padziko lapansi. Lemba la Aroma 6:23 limakamba kuti: “Malipilo a ucimo ndi imfa, koma mphatso imene Mulungu amapeleka ndi moyo wosatha kudzela mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.” Mu Nkhani 3 ya buku lino, tinaphunzila za madalitso amene adzakhala m’Paladaiso amene adzabwela padziko lapansi. (Chivumbulutso 21:3, 4) Madalitso a mtsogolo onsewa, kuphatikizapo moyo wosatha ndi thanzi langwilo, amatheka cifukwa Yesu anatifela. Koma kuti tikawalandile madalitso amenewo, tifunikila kuonetsa kuti timayamikila mphatso ya dipo.

KODI MUNGAONETSE BWANJI KUTI MUMAYAMIKILA?

18. N’cifukwa ciani tiyenela kumuyamikila Yehova cifukwa ca mphatso ya dipo?

18 N’cifukwa ciani tiyenela kumuyamikila kwambili Yehova pa dipo limene anapeleka? Mphatso imakhala yamtengo wapatali ngati wina anatailapo nthawi, mphamvu ndi ndalama. Mphatso imatifika pamtima ngati imaonetsa mmene munthu woipeleka amatikondela mocokela pansi pa mtima. Ndi mmenenso mphatso ya dipo ilili. Imapambana mphatso zonse zimene Mulungu anapelekapo, cifukwa anatailapo cinthu cofunika kwambili kwa iye. Lemba la Yohane 3:16 limati: “Mulungu anakonda kwambili dziko mwakuti anapeleka Mwana wake wobadwa yekha.” Dipo ndi umboni woonetsa bwino kwambili kuti Yehova amatikonda. Limaonetsanso cikondi ca Yesu kwa ife, cifukwa analola ndi mtima wonse kutifela. (Yohane 15:13) Conco, mphatso ya dipo iyenela kutipangitsa kutsimikiza mumtima mwathu kuti Yehova ndi Mwana wake amatikonda aliyense payekha-payekha.—Agalatiya 2:20.

A woman studying the Bible

Njila imodzi yoonetsela kuti mumayamikila mphatso ya Yehova ya dipo ndiyo kuphunzila za iye kuti mum’dziŵe bwino

19, 20. Kodi ndi njila ziti zimene mungaonetsele kuti mumayamikila mphatso ya dipo?

19 Nanga mungaonetse bwanji kuti mumayamikila Mulungu cifukwa ca mphatso yake ya dipo? Coyamba, mufunikila kumudziŵa bwino wopeleka mphatso imeneyi, Yehova. (Yohane 17:3) Kuphunzila Baibo kudzakuthandizani kumudziŵa bwino Mulungu. Pamene muonjezela cidziŵitso canu ponena za iye, cikondi canu pa iye cidzakulila-kulila. Ndipo cikondi cimeneco cidzakupangitsani kumacita zinthu zomukondweletsa.—1 Yohane 5:3.

20 Muyenela kuonetsa cikhulupililo mu nsembe ya dipo la Yesu.Yesu mwini wake anakamba kuti: “Iye wokhulupilila mwa Mwanayo ali nao moyo wosatha.” (Yohane 3:36) Nanga tingaonetse bwanji kuti timakhulupilila mwa Yesu? Cikhulupililo cimeneci si coonetsa ndi mau cabe iyai. Lemba la Yakobo 2:26 limakamba kuti: “Cikhulupililo copanda nchito zake ndi cakufa.” Zoona, “nchito,” kapena kuti zocita zathu, n’zimene zimatsimikizila ngati cikhulupililo cathu n’coona. Njila imodzi yoonetsela kuti tili ndi cikhulupililo mwa Yesu ndiyo kucita khama kutengela citsanzo cake, m’kalankhulidwe ndi m’kacitidwe ka zinthu.—Yohane 13:15.

21, 22. (a) N’cifukwa ciani tiyenela kumapezeka pamwambo wapacaka wa Mgonelo wa Ambuye? (b) Nanga nkhani yotsatila idzafotokoza ciani?

21 Muzipezeka pamwambo wapacaka wa Mgonelo wa Ambuye. Pa Nisani 14, m’madzulo, m’caka ca 33 C.E., Yesu anayambitsa mwambo wapadela umene Baibo imaucha “mgonelo wa Ambuye.” (1 Akorinto 11:20; Mateyu 26:26-28) Mwambo umenewu umachedwanso kuti Cikumbutso ca imfa ya Kristu. Yesu anayambitsa mwambo umenewu kuti athandize atumwi ake ndi Akristu oona onse kumakumbukila kuti pamene iye anafa monga munthu wangwilo, anapeleka moyo wake monga dipo. Ponena za mwambo umenewu, Yesu analamula kuti: “Muzicita zimenezi pondikumbukila.” (Luka 22:19) Kucita mwambo umenewu kumatikumbutsa cikondi cacikulu cimene Yehova ndi Yesu anationetsa popeleka dipo. Conco, ife tingaonetse kuwayamikila kaamba ka dipo limeneli mwa kupezeka pa mwambo umenewu caka ndi caka.a

22 Kunena zoona, dipo limene Yehova anapeleka ndi mphatso yamtengo wapatali kwambili. (2 Akorinto 9:14, 15) Ndipo mphatso imeneyi ikhoza kupindulitsa ngakhale anthu amene anafa. Nkhani yotsatila idzafotokoza zimenezi.

a Kuti mumve zambili za tanthauzo la Mgonelo wa Ambuye, onani Zakumapeto, pamapeji 206 mpaka 208.

ZIMENE BAIBO IMAPHUNZITSA

  • Dipo ndi njila imene Yehova amapulumutsila anthu ku ucimo ndi imfa.—Aefeso 1:7.

  • Yehova anapeleka dipo mwa kutumiza padziko lapansi Mwana wake wobadwa yekha kuti adzatifele.—1 Yohane 4:9, 10.

  • Kupyolela m’dipo, timakhululukidwa macimo athu, timakhala ndi cikumbumtima coyela, ndipo timakhala ndi ciyembekezo ca moyo wosatha.—1 Yohane 1:8, 9.

  • Timaonetsa kuti timayamikila dipo mwa kuphunzila zambili za Yehova, mwa kuonetsa cikhulupililo mu nsembe ya dipo la Yesu, ndi mwa kupezeka pa Mgonelo wa Ambuye.—Yohane 3:16.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani