NYIMBO 114
“Khalani Oleza Mtima”
Yopulinta
(Yakobo 5:8)
1. Yehova Mbuye wathu
Amakonda dzina lake.
Iye afunitsitsa
Kuti lisamanyozedwe.
Kucokela kalelo
Iye apililabe.
Yehova sanatope,
Amaleza mtima.
Afuna kuti anthu
Onse akapulumuke.
Kuleza mtima kwake
Sikudzapita pacabe.
2. Tifunika kukhala
Oleza mtima kwa onse.
Tidzapeza mtendele
Ndipo tidzapewa mkwiyo.
Tidzapewa kuona
Zoipa mwa anzathu.
Tikhale odziletsa
Olo pa mavuto.
Titengele Yehova
Tikhale oleza mtima.
Ise tikayesetsa
Tidzapeza madalitso.
(Onaninso Eks. 34:14; Yes. 40:28; 1 Akor. 13:4, 7; 1 Tim. 2:4.)