NYIMBO 121
Kudziletsa N’kofunika
Yopulinta
1. Ise tikonda Yehova M’lungu.
Komabe tidziŵa ndise ocimwa.
Mtima ungatisoceletse.
Tifunikila kudziletsa.
2. Tsiku na tsiku timayesedwa
Kuti’se ticite zinthu zoipa.
Koma mwa Mau ake M’lungu
Atithandiza kupambana.
3. Timaimila dzina la M’lungu,
Conco, tizipewa kulitonzetsa.
Mu zocita na m’mau athu,
Tikhale anthu odziletsa.
(Onaninso 1 Akor. 9:25; Agal. 5:23; 2 Pet. 1:6.)