TSIKU LOYAMBA
‘Kondwelani nthawi zonse mwa Ambuye. Ndibwelezanso, Kondwelani’!—Afilipi 4:4
KUM’MAŴA
8:20 Vidiyo ya Nyimbo
8:30 Nyimbo Na. 111 na Pemphelo
8:40 NKHANI YA CHEYAMANI: Cifukwa Cake Yehova Ni “Mulungu Wacimwemwe” (1 Timoteyo 1:11)
9:15 YOSIILANA: Kodi N’ciani Cimabweletsa Cimwemwe?
• Umoyo Wosalila Zambili (Mlaliki 5:12)
• Cikumbumtima Coyela (Salimo 19:8)
• Nchito Yokhutilitsa (Mlaliki 4:6; 1 Akorinto 15:58)
• Mabwenzi Azoona (Miyambo 18:24; 19:4, 6, 7)
10:05 Nyimbo Na. 89 na Zilengezo
10:15 KUŴELENGA BAIBO MONGA SEŴELO: “Yehova Anawacititsa Kusangalala” (Ezara 1:1–6:22; Hagai 1:2-11; 2:3-9; Zekariya 1:12-16; 2:7-9; 3:1, 2; 4:6, 7)
10:45 Kondwelani na Nchito za Yehova za Cipulumutso (Salimo 9:14; 34:19; 67:1, 2; Yesaya 12:2)
11:15 Nyimbo Na. 148 na Kupumula
KUMASANA
12:30 Vidiyo ya Nyimbo
12:40 Nyimbo Na. 131
12:45 YOSIILANA: Kulitsani Cimwemwe m’Banja Mwanu
• Amuna, Pezani Cimwemwe mwa Akazi Anu (Miyambo 5:18, 19; 1 Petulo 3:7)
• Akazi, Pezani Cimwemwe mwa Amuna Anu (Miyambo 14:1)
• Makolo, Pezani Cimwemwe mwa Ana Anu (Miyambo 23:24, 25)
• Acicepele, Pezani Cimwemwe mwa Makolo Anu (Miyambo 23:22)
13:50 Nyimbo Na. 135 na Zilengezo
14:00 YOSIILANA: Cilengedwe Cimaonetsa Kuti Yehova Amafuna Kuti Tizikondwela
• Maluŵa Okongola (Salimo 111:2; Mateyu 6:28-30)
• Zakudya Zokoma (Mlaliki 3:12, 13; Mateyu 4:4)
• Mitundu Yokongola (Salimo 94:9)
• Matupi Athu Opangidwa Mwaluso (Machitidwe 17:28; Aefeso 4:16)
• Mamvekedwe Okoma Kumvetsela (Miyambo 20:12; Yesaya 30:21)
• Nyama Zocititsa Cidwi (Genesis 1:26)
15:00 Anthu “Olimbikitsa Mtendele Amasangalala”—Cifukwa Ciani? (Miyambo 12:20; Yakobo 3:13-18; 1 Petulo 3:10, 11)
15:20 Kukhala pa Ubwenzi Wolimba na Yehova Kumabweletsa Cimwemwe Cacikulu Koposa! (Salimo 25:14; Habakuku 3:17, 18)
15:55 Nyimbo Na. 28 na Pemphelo Lothela