LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lmd phunzilo 6
  • Kucotsa Mantha

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kucotsa Mantha
  • Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Mmene Yesu Anacitila Zimenezi
  • Tiphunzilaponji kwa Yesu?
  • Tengelani Citsanzo ca Yesu
  • Pezani Mayankho pa Mafunso Aya:
    2018-2019 Pulogilamu ya Msonkhano wa Dela—Wa Woyang’anila Dela
  • Tilimbitseni Mtima
    ‘Imbani Mokweza ndi Mosangalala’ kwa Yehova
  • Tilimbitseni Mtima
    Imbilani Yehova—Nyimbo Zatsopano
  • Yehova Adzakuthandiza Kukhala Wolimba Mtima
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
lmd phunzilo 6

KUYAMBITSA MAKAMBILANO

Yesu akuuza Zakeyu kuti atsike mumtengo, koma anthu enawo akudabwa.

Luka 19:1-7

PHUNZILO 6

Kucotsa Mantha

Mfundo Yaikulu: “Tinalimba mtima mothandizidwa ndi Mulungu wathu ndipo tinalankhula kwa inu uthenga wabwino.”—1 Ates. 2:2.

Mmene Yesu Anacitila Zimenezi

Yesu akuuza Zakeyu kuti atsike mumtengo, koma anthu enawo akudabwa.

VIDIYO: Yesu Alalikila Zakeyu

1. Tambani VIDIYO, kapena ŵelengani Luka 19:1-7. Kenaka ganizilani pa mafunso otsatilawa:

  1. Cingakhale ciyani cinapangitsa anthu ena kum’pewa Zakeyu?

  2. Koma n’cifukwa ciyani Yesu anamulalikilabe?

Tiphunzilaponji kwa Yesu?

2. Tiyenela kucotsa mantha kuti tilalikile uthenga wa Ufumu mosayang’ana nkhope.

Tengelani Citsanzo ca Yesu

3. Dalilani Yehova. Mzimu wa Mulungu unapatsa Yesu mphamvu kuti alalikile. Inunso ungakupatseni mphamvu. (Mat. 10:19, 20; Luka 4:18) M’pempheni Yehova akucotseni mantha kuti muzitha kuwalalikila ngakhale anthu aja amene mungacite nawo mantha.—Mac. 4:29.

4. Pewani kuweluzilatu anthu. Anthu ena tingadodome kuwalalikila cifukwa ca maonekedwe awo, kulemekezeka kwawo, cuma, kuchuka, kapena cipembedzo cawo. Koma kumbukilani izi:

  1. Yehova na Yesu amaona zili mu mtima; ife sitingathe.

  2. Yehova angathandize munthu aliyense.

5. Khalani wopanda mantha komabe wosamala. (Mat. 10:16) Pewani mikangano. Mwaulemu, thetsani makambilano anu ngati munthuyo safuna kumvetsela uthenga wabwino, kapena mukaona kuti pangacitike coipa.—Miy. 17:14.

ONANINSO MALEMBA AWA

Mac. 4:31; Aef. 6:19, 20; 2 Tim. 1:7

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani